Mateyu 14:1-36

14  Pa nthawiyo Herode,* wolamulira chigawo, anamva za Yesu+  ndipo anauza atumiki ake kuti: “Ameneyu ndi Yohane M’batizi. Anauka kwa akufa, ndipo n’chifukwa chake akuchita ntchito zamphamvu.”+  Pakuti Herode anagwira Yohane, kum’manga ndi kum’tsekera m’ndende chifukwa Herode anakwatira Herodiya, mkazi wa m’bale wake Filipo.+  Anachita zimenezi chifukwa Yohane anali kumuuza kuti: “N’kosaloleka kutenga mkaziyu kuti akhale mkazi wanu.”+  Komabe, ngakhale kuti Herode ankafuna kupha Yohane, anaopa khamu la anthu, chifukwa iwo anali kukhulupirira kuti ndi mneneri.+  Koma tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode+ litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa Herode kwambiri,  mwakuti analonjeza molumbira kuti adzapatsa mtsikanayo chilichonse chimene angapemphe.+  Tsopano mtsikanayu, mayi wake atachita kum’pangira, anapempha kuti: “Ndipatseni mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.”+  Mfumuyo inamva chisoni, koma poganizira lumbiro lake lija ndi anthu amene anali nawo paphwandolo, analamula kuti mutuwo uperekedwe.+ 10  Choncho anatuma munthu kukadula mutu wa Yohane m’ndende. 11  Kenako anabweretsa mutuwo m’mbale ndi kuupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anapita nawo kwa mayi ake.+ 12  Pambuyo pake, ophunzira ake anabwera kudzatenga mtembo wake ndi kukauika m’manda.+ Kenako anapita kukauza Yesu. 13  Yesu atamva zimenezi, anachoka kumeneko pa ngalawa n’kupita kumalo kopanda anthu kuti akakhale payekha.+ Koma khamu la anthu litamva zimenezo, linam’tsatira wapansi kuchokera m’mizinda yawo. 14  Tsopano Yesu atatsika m’ngalawayo anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anawamvera chisoni,+ ndi kuwachiritsira anthu awo odwala.+ 15  Koma chakumadzulo ophunzira ake anabwera kwa iye ndi kunena kuti: “Kuno n’kopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite m’midzimo kuti akagule chakudya.”+ 16  Koma Yesu anawayankha kuti: “Palibe chifukwa choti apitire. Inuyo muwapatse chakudya.”+ 17  Iwo anamuuza kuti: “Tilibe chilichonse pano, koma mitanda isanu ya mkate ndi nsomba ziwiri zokha basi.”+ 18  Ndiyeno iye anati: “Bweretsani zimenezo kuno.” 19  Kenako analamula khamu la anthulo kuti likhale pansi pa udzu. Pamenepo anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija, n’kuyang’ana kumwamba ndi kupempha dalitso.+ Atatero ananyemanyema mitanda ya mkate ija n’kupatsa ophunzirawo, ndipo iwonso anagawira khamulo.+ 20  Chotero onse anadya n’kukhuta, ndipo anatolera zotsala zodzaza madengu 12.+ 21  Koma amene anadya anali amuna pafupifupi 5,000 osawerengera akazi ndi ana aang’ono.+ 22  Kenako mwamsanga, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti akwere ngalawa ndi kutsogola kupita kutsidya lina, pamene iye anali kuuza anthuwo kuti azipita kwawo.+ 23  Pambuyo pake, atauza anthuwo kuti azipita, anakwera m’phiri yekhayekha kukapemphera.+ Ngakhale kuti kunali kutada, iye anakhalabe kumeneko yekhayekha. 24  Pa nthawiyi n’kuti ngalawa ija itapita kutali pakati pa madzi, ndipo inali kukankhidwa mwamphamvu ndi mafunde+ chifukwa anali kulimbana ndi mphepo yamphamvu. 25  Koma pa ulonda wachinayi* m’bandakucha, iye anafika kwa ophunzirawo akuyenda pamwamba pa madzi.+ 26  Pamene ophunzirawo anamuona akuyenda panyanjapo, anavutika mumtima, n’kumanena kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!”+ Ndipo anafuula mwamantha. 27  Koma nthawi yomweyo Yesu anawauza kuti: “Limbani mtima, ndine.+ Musachite mantha.” 28  Pamenepo Petulo anayankha kuti: “Ambuye, ngati ndinudi, ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwere kuli inuko.” 29  Iye anamuuza kuti: “Bwera!” Nthawi yomweyo Petulo anatsika m’ngalawamo+ n’kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. 30  Koma ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha, ndipo atayamba kumira anafuula kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!” 31  Nthawi yomweyo Yesu anatambasula dzanja lake ndi kum’gwira dzanja n’kumuuza kuti: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?”+ 32  Atakwera m’ngalawa, mphepo yamkuntho ija inaleka. 33  Pamenepo amene anali m’ngalawamo anam’gwadira ndi kunena kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.”+ 34  Ndipo anawolokera kumtunda ku Genesarete.+ 35  Anthu a m’dera limeneli atamuzindikira, anatumiza mithenga m’midzi yonse yapafupi, ndipo anthu anam’bweretsera odwala onse.+ 36  Anthu anali kum’pempha kuti angogwira chabe ulusi wopota wa m’mphepete mwa malaya ake akunja,+ ndipo onse amene anaugwira anachiriratu.

Mawu a M'munsi

Ameneyu anali Herode Antipa, mwana wa Herode Wamkulu.
Mu nthawi ya Aroma, Ayuda ankagawa usiku m’magawo anayi. Chigawo choyamba chinali kuyamba 6 koloko madzulo mpaka 9 koloko usiku. Chigawo chachiwiri chinali kuyamba 9 koloko mpaka 12 koloko usiku. Chigawo chachitatu chinali kuyamba 12 koloko usiku mpaka 3 koloko ndipo chigawo chachinayi chinali kuyamba 3 koloko mpaka 6 koloko m’mawa.