Mateyu 19:1-30

19  Tsopano Yesu atatsiriza mawu amenewa, anachoka ku Galileya ndi kubwera kumadera a kumalire kwa Yudeya kutsidya la Yorodano.+  Khamu lalikulu la anthu linam’tsatira, ndipo iye anawachiritsa kumeneko.+  Afarisi anabwera kwa iye, ndipo pofuna kumuyesa anamufunsa kuti: “Kodi n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”+  Yesu anayankha kuti: “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi+  n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake+ n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’?+  Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”+  Iwo anamufunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipereka kalata yothetsa ukwati kwa mkazi ndi kum’siya?”+  Iye anayankha kuti: “Chifukwa cha kuuma mtima kwanu,+ Mose anakulolezani kuti muzithetsa ukwati, koma kuyambira pa chiyambi sizinali choncho ayi.+  Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”*+ 10  Kenako ophunzira ake anati: “Ngati zili choncho kwa munthu ndi mkazi wake, ndiyetu ndi bwino kusakwatira.”+ 11  Iye anawauza kuti: “Si onse amene angathe kuchita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatso.+ 12  Pakuti ena sakwatira chifukwa chakuti anabadwa choncho kuchokera m’mimba mwa mayi awo,+ ndipo ena chifukwa chakuti anafulidwa ndi anthu. Koma pali ena amene safuna kukwatira chifukwa cha ufumu wakumwamba. Amene angathe kuchita zimenezi achite.”+ 13  Kenako anthu anam’bweretsera ana aang’ono kuti awaike manja ndi kuwapempherera, koma ophunzirawo anawakalipira.+ 14  Koma Yesu anawauza kuti: “Alekeni anawo, ndipo musawaletse kubwera kwa ine, pakuti ufumu wakumwamba ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa.”+ 15  Pamenepo anaika manja ake pa anawo, kenako anachoka kumeneko.+ 16  Tsopano munthu wina anafika kwa iye ndi kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, n’chiyani chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 17  Iye anamuyankha kuti: “N’chifukwa chiyani ukundifunsa chimene chili chabwino? Pali Mmodzi yekha amene ali wabwino.+ Chotero ngati ukufuna kukapeza moyo, uzisunga malamulo nthawi zonse.”+ 18  Koma iye anafunsa Yesu kuti: “Malamulo ati?”+ Yesu anati: “Akuti, Usaphe+ munthu,* Usachite chigololo,+ Usabe,+ Usapereke umboni wonamizira mnzako.+ 19  Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,+ komanso lakuti, Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 20  Mnyamatayo anayankha Yesu kuti: “Ndakhala ndikutsatira zonsezi, n’chiyaninso chimene ndikupereweza?” 21  Yesu anamuuza kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba,+ ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 22  Mnyamata uja atamva mawu amenewa, anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+ 23  Koma Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndithu ndikukuuzani, zidzakhalatu zovuta kuti munthu wolemera adzalowe mu ufumu wakumwamba.+ 24  Ndiponso ndikukuuzani kuti, N’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.”+ 25  Ophunzirawo atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anati: “Ndiye angapulumuke ndani?”+ 26  Yesu anawayang’anitsitsa n’kunena kuti: “Kwa anthu zimenezi n’zosathekadi, koma zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.”+ 27  Pamenepo Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani, kodi tidzapeza chiyani?”+ 28  Yesu anawayankha kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pampando wachifumu waulemerero, inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12, kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.+ 29  Aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kwambiri kuposa zimenezi, ndipo adzapeza moyo wosatha.+ 30  “Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza, ndipo omaliza adzakhala oyamba.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.
Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.