Mateyu 11:1-30

11  Tsopano Yesu atamaliza kupereka malangizo kwa ophunzira ake 12 aja, anachoka kumeneko n’kupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira kumizinda ina.+  Koma pamene Yohane anali m’ndende, anamva+ zimene Khristu anali kuchita, ndipo anatuma ophunzira ake  kukam’funsa kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?”+  Poyankha Yesu ananena kuti: “Pitani mukamuuze Yohane zimene mukumva ndi kuona:  Akhungu akuonanso,+ olumala+ akuyendayenda, akhate+ akuyeretsedwa ndipo ogontha+ akumva. Akufa+ akuukitsidwa, ndipo kwa aumphawi uthenga wabwino ukulengezedwa.+  Wodala amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.”+  Pamene ophunzira a Yohane anali kubwerera, Yesu anayamba kuuza khamu la anthulo za Yohane kuti: “Kodi munapita m’chipululu kukaona chiyani?+ Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo?+  Nanga munapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zapamwamba kapena? Iyayi, pajatu ovala zovala zapamwamba amapezeka m’nyumba za mafumu.+  Nangano n’chifukwa chiyani munapita makamaka? Kukaona mneneri kapena? Inde, ndikukuuzani, woposadi mneneri.+ 10  Malemba amanena za iyeyu kuti, ‘Taona! Inetu ndikutumiza mthenga wanga choyamba, amene adzakukonzera njira!’+ 11  Ndithu ndikukuuzani anthu inu, Mwa onse obadwa kwa akazi,+ sanabadwepo wamkulu woposa Yohane M’batizi. Koma munthu amene ali wocheperapo mu ufumu+ wakumwamba ndi wamkulu kuposa iyeyu. 12  Kuyambira m’masiku a Yohane M’batizi mpaka tsopano anthu akulimbikira kupeza mwayi wolowa mu ufumu wakumwamba, ndipo amene akulimbikira mwakhama akuupeza.+ 13  Pakuti zonse, Zolemba za aneneri ndi Chilamulo, zinalosera mpaka nthawi ya Yohane.+ 14  Kaya mukhulupirira kapena ayi, Yohane ndiye ‘Eliya woyembekezeka kubwera uja.’+ 15  Amene ali ndi makutu amve.+ 16  “Kodi m’badwo uwu ndiufanizire ndi ndani?+ Uli ngati ana aang’ono amene amakhala pansi m’misika n’kumafuulira anzawo osewera nawo+ 17  kuti, ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunadzigugude pachifuwa chifukwa cha chisoni.’+ 18  Mofanana ndi zimenezi, Yohane anabwera ndipo sanali kudya kapena kumwa.+ Koma anthu ankanena kuti, ‘Ali ndi chiwanda.’ 19  Kunabwera Mwana wa munthu ndipo anali kudya ndi kumwa,+ koma anthu akunenabe kuti, ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa.’+ Mulimonsemo, nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.”+ 20  Kenako anayamba kudzudzula mizinda imene anachitamo ntchito zambiri zamphamvu, chifukwa sinalape.+ 21  Iye anati: “Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida!+ chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanachitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu akanakhala atalapa kalekale, atavala ziguduli* ndi kukhala paphulusa.+ 22  Koma tsopano ndikukuuzani kuti, Chilango cha Turo ndi Sidoni pa Tsiku la Chiweruzo+ chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi chanu.+ 23  Iwenso Kaperenao,+ kodi udzakwezedwa kumwamba kapena? Ku Manda*+ n’kumene udzatsikira ndithu,+ chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanachitika ku Sodomu, mzindawo ukanakhala ulipobe mpaka lero. 24  Koma tsopano ndikukuuzani anthu inu kuti, Chilango cha Sodomu pa Tsiku la Chiweruzo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha Kaperenao.”+ 25  Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziulula kwa tiana.+ 26  Inde Atate wanga, ndikukutamandani chifukwa inu munavomereza kuti zimenezi zichitike. 27  Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate+ okha, komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha+ ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.+ 28  Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa,+ ndipo ndidzakutsitsimutsani. 29  Senzani goli+ langa ndipo phunzirani kwa ine,+ chifukwa ndine wofatsa+ ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa,+ 30  pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”
Onani Zakumapeto 5.