Mateyu 8:1-34

8  Atatsika m’phirimo, chikhamu cha anthu chinam’tsatira.  Kenako panafika munthu wakhate.+ Munthuyo anamugwadira n’kunena kuti: “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”  Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake n’kumukhudza, ndipo anati: “Ndikufuna. Khala woyera.”+ Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.+  Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi,+ koma upite ukadzionetse kwa wansembe,+ ndipo ukapereke mphatso+ imene Mose analamula, kuti ikhale umboni kwa iwo.”  Atalowa mumzinda wa Kaperenao,+ kapitawo wa asilikali anabwera kwa iye ndi kum’pempha  kuti: “Ambuye, wantchito wanga wafa ziwalo moti ali gone m’nyumba, ndipo akuzunzika koopsa.”  Iye anamuyankha kuti: “Ndikafika kumeneko ndikam’chiritsa.”  Poyankha, kapitawo wa asilikali uja anati: “Ambuye, sindine munthu woyenera kuti inu mukalowe m’nyumba mwanga, koma mungonena mawu okha ndipo wantchito wangayo achira.  Pakuti inenso ndili ndi akuluakulu ondiyang’anira, komanso ndili ndi asilikali amene ali pansi panga. Ndikauza mmodzi kuti, ‘Pita!’+ amapita, wina ndikamuuza kuti ‘Bwera!’ amabwera. Kapolo wanga ndikamuuza kuti, ‘Chita ichi!’ amachita.” 10  Atamva zimenezo, Yesu anadabwa ndipo anauza amene anali kum’tsatira aja kuti: “Kunena zoona, mu Isiraeli sindinapezemo aliyense wachikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.+ 11  Koma ndikukutsimikizirani kuti ambiri ochokera kum’mawa ndi kumadzulo+ adzabwera ndi kukhala patebulo limodzi ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo mu ufumu+ wakumwamba,+ 12  pamene ana a ufumuwo+ adzaponyedwa kunja kumdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”+ 13  Kenako Yesu anauza kapitawo wa asilikaliyo kuti: “Pita. Malinga ndi chikhulupiriro chako, chimene ukufuna chichitike.”+ Mu ola lomwelo, wantchito uja anachira. 14  Tsopano Yesu, atalowa m’nyumba mwa Petulo, anaona apongozi aakazi a Petulo+ ali gone, akudwala malungo.*+ 15  Choncho anagwira dzanja la mayiwo,+ ndipo malungowo anatheratu, moti anadzuka n’kuyamba kumutumikira.+ 16  Koma chakumadzulo, anthu anamubweretsera anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda, ndipo iye anatulutsa mizimu imeneyo ndi mawu okha. Onse amene sanali kumva bwino m’thupi anawachiritsa. 17  Anachita izi kuti zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti: “Iye anatenga matenda athu n’kunyamula zowawa zathu.”+ 18  Pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lamuzungulira, analangiza ophunzira ake kuti akankhire ngalawa pamadzi n’kupita kutsidya lina.+ 19  Tsopano kunabwera mlembi wina ndi kumuuza kuti: “Mphunzitsi, ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.”+ 20  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamira mutu wake.”+ 21  Kenako wina mwa ophunzira ake anamuuza kuti: “Ambuye, ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.” 22  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Iwe unditsatirebe ine, ndipo aleke akufa aike akufa awo.”+ 23  Ndiyeno pamene analowa m’ngalawa,+ ophunzira ake anam’tsatira. 24  Kenako panyanjapo panabuka mphepo yamphamvu moti mafunde anali kulowa m’ngalawamo, koma iye anali m’tulo.+ 25  Ndipo iwo anapita kukam’dzutsa+ kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!” 26  Koma iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?”+ Kenako anadzuka n’kudzudzula mphepo ndi nyanjayo, ndipo panachita bata lalikulu.+ 27  Chotero amunawo anadabwa n’kunena kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi wotani,+ moti ngakhale mphepo ndi nyanja zikum’mvera?” 28  Atafika kutsidya linalo, m’dera la Agadara,+ anakumana ndi amuna awiri ogwidwa ndi ziwanda+ akuchokera m’manda achikumbutso. Amunawa anali ochititsa mantha nthawi zonse moti panalibe aliyense woyesa dala kudutsa msewu umenewo. 29  Nthawi yomweyo iwo anafuula, kuti: “Kodi tili nanu chiyani, Mwana wa Mulungu?+ Kodi mwabwera kudzatizunza+ nthawi yoikidwiratu isanakwane?”+ 30  Koma pamtunda wautali ndithu kuchokera pamenepo, nkhumba zambiri zinali kudya. 31  Chotero ziwandazo zinayamba kum’chonderera kuti: “Ngati mukufuna kutitulutsa, mutitumize munkhumbazi.”+ 32  Pamenepo iye anaziuza kuti: “Pitani!” Choncho zinatuluka ndi kukalowa m’nkhumba zija. Nthawi yomweyo nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi ndi kulumphira m’nyanja, ndipo zinafera m’madzimo.+ 33  Koma amene anali kuyang’anira ziwetozo anathawa ndipo atalowa mumzinda anafotokoza zonse kuphatikizapo zimene zinachitikira amuna ogwidwa ndi ziwanda aja. 34  Zitatero, anthu onse mumzindawo anapita kukakumana ndi Yesu. Atamuona, anam’pempha kuti achoke m’madera akwawoko.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”