Mateyu 28:1-20

28  Tsiku la sabata litatha, m’bandakucha wa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya Mmagadala ndi Mariya wina uja anabwera kudzaona manda.+  Atafika pafupi, anazindikira kuti pachitika chivomezi champhamvu, pakuti mngelo wa Yehova anatsika kumwamba, ndipo anafika ndi kugubuduza chimwala chija, n’kukhala pachimwalapo.+  Maonekedwe ake anali ngati a mphezi,+ ndipo zovala zake zinali zoyera mbee!+  Alonda aja pochita mantha ndi mngeloyo, ananjenjemera ndipo anangouma gwaa ngati akufa.  Koma mngeloyo+ anauza amayiwo kuti: “Inu musachite mantha, chifukwa ndikudziwa kuti mukufuna Yesu+ amene anapachikidwa.  Iye sali pano chifukwa wauka kwa akufa+ monga ananenera. Bwerani muone pamene anagona.  Ndipo pitani mwamsanga mukauze ophunzira ake kuti wauka kwa akufa,+ moti padakali pano, watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona. Umenewutu ndi uthenga wanga kwa inu.”+  Choncho, iwo anachoka mwamsanga pamanda achikumbutsowo, ali ndi mantha ndiponso chimwemwe chochuluka, ndipo anathamanga kukauza ophunzira ake.+  Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo n’kunena kuti: “Moni amayi!” Pamenepo iwo anafika pafupi ndi kugwira mapazi ake ndi kumuweramira mpaka nkhope zawo pansi. 10  Kenako Yesu anawauza kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga,+ kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.” 11  Adakali m’njira, alonda+ ena anapita mumzinda ndipo anakauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitika. 12  Ansembe aakuluwo atakambirana ndi akulu, anapangana zochita ndipo anapereka ndalama zasiliva zambiri kwa asilikaliwo+ 13  n’kuwauza kuti: “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake+ anabwera usiku kudzamuba ife titagona.’ 14  Bwanamkubwa akamva zimenezi, tikamunyengerera ndipo inu musade naye nkhawa.” 15  Choncho anatenga ndalama zasilivazo ndi kuchita monga anawauzira ndipo nkhani imeneyi inafala kwambiri pakati pa Ayuda mpaka lero. 16  Koma ophunzira 11 aja anapita ku Galileya,+ kuphiri kumene Yesu anakonza kukakumana nawo. 17  Atamuona anamugwadira, koma ena anakayika ngati anali iye.+ 18  Tsopano Yesu anayandikira ndi kulankhula nawo kuti: “Ulamuliro wonse+ waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi. 19  Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse+ kuti akhale ophunzira anga.+ Muziwabatiza+ m’dzina la Atate,+ ndi la Mwana,+ ndi la mzimu woyera,+ 20  ndi kuwaphunzitsa+ kusunga+ zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.+ Ndipo dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu+ masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi* ino.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.