Mateyu 27:1-66

27  M’mawa kutacha, ansembe aakulu limodzi ndi akulu onse anakambirana ndi kugwirizana kuti aphe Yesu.+  Ndipo atam’manga, anapita kukam’pereka kwa bwanamkubwa Pilato.+  Pamenepo Yudasi amene anam’pereka uja ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti aphedwe, anavutika koopsa mumtima mwake moti anapita kukabweza ndalama 30+ zasiliva zija kwa ansembe aakulu ndiponso akulu.  Iye anati: “Ndachimwa popereka munthu wolungama.”*+ Koma iwo anamuyankha kuti: “Ife sizikutikhudza zimenezo. Udziwa wekha chochita!”+  Choncho iye anaponya ndalama zasiliva zija m’kachisi n’kuchoka, ndipo anakadzimangirira.+  Koma ansembe aakulu anatenga ndalama zasilivazo n’kunena kuti: “N’kosaloleka kuponya ndalamazi m’malo opatulika osungiramo chuma, chifukwa ndi malipiro a magazi.”  Koma atakambirana, anatenga ndalamazo n’kukagulira munda wa woumba mbiya kuti ukhale manda a alendo.  Choncho munda umenewu umatchedwa “Munda wa Magazi”+ mpaka lero.  Pamenepo zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yeremiya* zinakwaniritsidwa. Iye anati: “Ndipo anatenga ndalama 30 zasiliva,+ zomwe zinali mtengo wogulira munthu umene ena mwa ana a Isiraeli anamuikira, 10  ndipo anagulira munda wa woumba mbiya,+ malinga ndi zimene Yehova anandilamula.” 11  Tsopano Yesu anaimirira pamaso pa bwanamkubwa, ndipo bwanamkubwayo anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?”+ Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha.”+ 12  Koma pamene ansembe aakulu komanso akulu anali kumuneneza,+ iye sanayankhe chilichonse.+ 13  Pamenepo Pilato anamufunsa kuti: “Kodi sukumva zonse zimene akukunenezazi?”+ 14  Koma iye anangokhala duu, osanena kanthu, moti bwanamkubwayo anadabwa kwambiri.+ 15  Pa chikondwerero chilichonse, bwanamkubwayu anali ndi dongosolo lomasulira anthu mkaidi mmodzi amene anthuwo akufuna.+ 16  Ndipo pa nthawiyi panali mkaidi wina wowopsa kwambiri wotchedwa Baraba.+ 17  Choncho atasonkhana pamodzi, Pilato ananena kuti: “Kodi mukufuna ndikumasulireni ndani, Baraba kapena Yesu, uja amamuti Khristu?”+ 18  Pakuti iye anadziwa kuti anamupereka chifukwa cha kaduka.+ 19  Komanso atakhala pampando woweruzira milandu, mkazi wake anamutumizira mawu akuti: “Nkhani ya munthu wolungamayu isakukhudzeni.+ Inetu ndavutika kwambiri lero m’maloto+ chifukwa cha iyeyu.” 20  Koma ansembe aakulu limodzi ndi akulu analimbikitsa anthu kupempha kuti awamasulire Baraba,+ ndi kuti Yesu aphedwe. 21  Pamenepo bwanamkubwayo anawafunsa kuti: “Ndani mwa awiriwa amene mukufuna kuti ndikumasulireni?” Iwo anati: “Baraba.”+ 22  Pilato anafunsanso kuti: “Nanga Yesu, uja amamuti Khristu, ndichite naye chiyani?” Onse anayankha kuti: “Apachikidwe ameneyo!”+ 23  Iye anati: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani?” Koma atatero m’pamene anawonjezera kufuula kuti: “Apachikidwe basi!”+ 24  Poona kuti sizikuthandiza, komanso pakuyambika chipolowe, Pilato anangotenga madzi+ ndi kusamba m’manja pamaso pa khamu la anthulo, n’kunena kuti: “Inetu ndasamba m’manja, ndilibe mlandu wa magazi a munthu uyu. Zonse zili kwa inu.” 25  Atanena izi anthu onse anayankha kuti: “Magazi ake akhala pa ife ndi pa ana athu.”+ 26  Pamenepo anawamasulira Baraba, koma analamula kuti Yesu akwapulidwe+ kenako anamupereka kuti akam’pachike.+ 27  Ndiyeno asilikali a bwanamkubwa anatengera Yesu m’nyumba ya bwanamkubwa n’kusonkhanitsa khamu lonse la asilikali kwa iye.+ 28  Kumeneko anamuvula zovala zake ndi kumuveka chinsalu chofiira kwambiri.+ 29  Komanso analuka chisoti chachifumu chaminga ndi kumuveka kumutu n’kumupatsa bango m’dzanja lake lamanja. Kenako anamugwadira ndi kum’chitira zachipongwe+ kuti: “Mtendere ukhale nanu, inu Mfumu ya Ayuda!”+ 30  Atatero anamulavulira+ ndi kutenga bango lija ndi kuyamba kum’menya nalo m’mutu. 31  Atamaliza kumuchitira zachipongwezo,+ anamuvula chinsalu chija ndi kumuveka malaya ake akunja n’kupita naye kukamupachika.+ 32  Pamene anali kupita, anakumana ndi Simoni, nzika ya ku Kurene.+ Iwo anasenzetsa munthu ameneyu mtengo wozunzikirapo* wa Yesu. 33  Atafika pamalo otchedwa Gologota,+ kutanthauza kuti, Malo a Chibade, 34  anapatsa Yesu vinyo wosakaniza ndi ndulu+ kuti amwe, koma iye atalawa, anakana kumwa.+ 35  Atam’pachika+ anagawana malaya ake akunja+ mwa kuchita maere,+ 36  ndipo anakhala pansi n’kumamuyang’anira. 37  Komanso pamwamba pa mutu wake anakhomapo chikwangwani cha mawu osonyeza mlandu wake kuti: “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.”+ 38  Achifwamba awiri anapachikidwa limodzi ndi iye, mmodzi kudzanja lake lamanja, wina kumanzere kwake.+ 39  Tsopano anthu odutsa anayamba kunena mawu onyoza+ Yesu. Anali kupukusa+ mitu yawo 40  n’kumanena kuti: “Iwe wogwetsa kachisi+ ndi kum’manga m’masiku atatu, dzipulumutse! Ngati ulidi mwana wa Mulungu, tsikatu pamtengo wozunzikirapowo!”+ 41  Chimodzimodzinso ansembe aakulu limodzi ndi alembi komanso akulu. Nawonso anayamba kum’chita chipongwe ndi kunena kuti:+ 42  “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika! Ameneyutu ndi Mfumu+ ya Isiraeli, atsiketu pamtengo wozunzikirapowo kuti ife timukhulupirire.+ 43  Suja amakhulupirira Mulungu? Mulunguyo am’pulumutse+ tsopano ngati akumufunadi. Ndi ujatu anali kunena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu.’”+ 44  Nawonso achifwamba amene anapachikidwa naye limodzi anayamba kumunyoza.+ 45  Kuyambira cha m’ma 12 koloko masana* kunagwa mdima+ m’dziko lonselo, mpaka 3 koloko masana.*+ 46  Cha m’ma 3 kolokomo Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “Eʹli, Eʹli, laʹma sa·bach·thaʹni?” kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”+ 47  Atamva izi, ena mwa anthu amene anaimirira chapomwepo anayamba kunena kuti: “Munthuyu akuitana Eliya.”+ 48  Nthawi yomweyo mmodzi wa iwo anathamanga kukatenga chinkhupule ndi kuchiviika m’vinyo wowawasa+ ndipo anachiika kubango ndi kum’patsa kuti amwe.+ 49  Koma enawo anati: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzam’pulumutsa.”+ [[Munthu wina anatenga mkondo ndi kumubaya* m’mbalimu cham’mimba ndipo panatuluka magazi ndi madzi.]]*+ 50  Pamenepo Yesu anafuulanso mokweza mawu, kenako anatsirizika.+ 51  Nthawi yomweyo nsalu yotchinga+ ya m’nyumba yopatulika inang’ambika pakati kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ Dziko lapansi linagwedezeka, ndipo matanthwe anang’ambika.+ 52  Manda achikumbutso anatseguka ndipo mitembo yambiri ya anthu oyera amene anaikidwa mmenemo inaponyedwa kunja, 53  ndi kuonekera kwa anthu ambiri. (Pambuyo pa kuukitsidwa kwa Yesu, anthu amene anali kuchokera kumanda achikumbutsoko, analowa mumzinda woyera.)+ 54  Koma kapitawo wa asilikali ndi ena amene anali naye polondera Yesu ataona chivomezicho ndi zimene zimachitikazo, anachita mantha kwambiri ndipo anati: “Ndithudi, uyu analidi Mwana wa Mulungu.”+ 55  Komanso akazi ambiri ochokera ku Galileya amene ankatsatira Yesu kuti azimutumikira,+ anali komweko akuonerera chapatali ndithu.+ 56  Pakati pawo panali Mariya Mmagadala, Mariya mayi a Yakobo ndi Yose, ndiponso panali mayi a Yakobo ndi Yohane.*+ 57  Tsopano madzulo, munthu wina wachuma wa ku Arimateya, wotchedwa Yosefe, amenenso anakhala wophunzira wa Yesu,+ 58  anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu.+ Pilato analamula kuti amupatse mtembowo.+ 59  Yosefe anatenga mtembowo ndi kuukulunga munsalu yoyera yabwino kwambiri,+ 60  ndipo anakauika m’manda ake achikumbutso atsopano,+ amene anawasema m’thanthwe. Kenako anagubuduza chimwala chachikulu ndi kutseka pakhomo la manda achikumbutsowo, n’kuchoka.+ 61  Koma Mariya Mmagadala ndi Mariya wina anatsalira komweko, atakhala pansi pafupi ndi mandawo.+ 62  Tsiku lotsatira, pambuyo pa Tsiku Lokonzekera,+ ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhana pamaso pa Pilato, 63  ndi kunena kuti: “Bwana, ife takumbukira kuti wonyenga uja adakali moyo ananena kuti, ‘Patapita masiku atatu ndidzauka.’+ 64  Choncho lamulani kuti akhwimitse chitetezo pamandapo kufikira tsiku lachitatu, kuti ophunzira ake asabwere kudzamuba+ ndi kuuza anthu kuti, ‘Anauka kwa akufa!’ pakuti chinyengo chotsirizachi chidzakhala choipa kwambiri kuposa choyamba chija.” 65  Pilato anawayankha kuti: “Inu muli nawo asilikali olondera.+ Pitani kakhwimitseni chitetezo monga mmene mukudziwira.” 66  Choncho anapita ndi kukakhwimitsa chitetezo pamandawo mwa kutseka kwambiri mandawo ndi chimwala*+ n’kuikapo asilikali olondera.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “magazi olungama.”
Mawuwa kwenikweni ndi a pa Zek 11:12, 13. M’nthawi ya Mateyu, buku la Yeremiya linali loyambirira mumpukutu wa mabuku a aneneri. Chotero mwina mabuku onsewo a aneneri, kuphatikizapo la Zekariya, anali kutchedwa kuti Yeremiya. Yerekezani ndi Lu 24:44.
Onani Zakumapeto 9.
Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Ena amati “kugwaza.”
Onani mawu a m’munsi pa Mt 16:3.
Mawu ake enieni, “mayi wa ana a Zebedayo.”
Mawu achigiriki amanena kuti mwalawo anauchita zinazake kuti ngati wina atausuntha iwo adzadziwe.