Mateyu 1:1-25

1  Buku la mzere wa makolo+ a Yesu Khristu, mwana wa Davide,+ mwana wa Abulahamu:+   Abulahamu anabereka Isaki.+Isaki anabereka Yakobo.+Yakobo anabereka Yuda+ ndi abale ake.   Yuda anabereka Perezi+ ndi Zera, ndipo mayi awo anali Tamara.Perezi anabereka Hezironi.+Hezironi anabereka Ramu.+   Ramu anabereka Aminadabu.Aminadabu anabereka Naasoni.+Naasoni anabereka Salimoni.+   Salimoni anabereka Boazi, ndipo mayi ake anali Rahabi.+Boazi anabereka Obedi, ndipo mayi ake anali Rute.+Obedi anabereka Jese.+   Jese anabereka mfumu+ Davide.+  Davide anabereka Solomo,+ yemwe mayi ake anali mkazi wa Uriya.   Solomo anabereka Rehobowamu.+Rehobowamu anabereka Abiya.Abiya+ anabereka Asa.+   Asa anabereka Yehosafati.+Yehosafati anabereka Yehoramu.+Yehoramu anabereka Uziya.   Uziya anabereka Yotamu.+Yotamu anabereka Ahazi.+Ahazi anabereka Hezekiya.+ 10  Hezekiya anabereka Manase.+Manase+ anabereka Amoni.+Amoni+ anabereka Yosiya. 11  Yosiya+ anabereka Yekoniya+ ndi abale ake pa nthawi imene Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo.+ 12  Ayuda atatengedwa kupita ku Babulo, Yekoniya anabereka Salatiyeli.+Salatiyeli anabereka Zerubabele.+ 13  Zerubabele anabereka Abiyudi.Abiyudi anabereka Eliyakimu.Eliyakimu anabereka Azoro. 14  Azoro anabereka Zadoki.Zadoki anabereka Akimu.Akimu anabereka Eliyudi. 15  Eliyudi anabereka Eleazara.Eleazara anabereka Matani.Matani anabereka Yakobo. 16  Yakobo anabereka Yosefe mwamuna wake wa Mariya, amene anabereka Yesu,+ wotchedwa Khristu.+ 17  Chotero, mibadwo yonse kuchokera pa Abulahamu kukafika pa Davide inalipo mibadwo 14, ndipo kuchokera pa Davide kukafika nthawi imene Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo panali mibadwo 14. Kuchokera pa nthawi imene Ayudawo anatengedwa kupita ku Babulo kukafika pa Khristu, panali mibadwo 14. 18  Koma kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Pa nthawi imene mayi ake Mariya anali atalonjezedwa+ ndi Yosefe kuti adzam’kwatira, Mariyayo anapezeka kuti ali ndi pakati mwa mzimu woyera+ asanatengane. 19  Koma mwamuna wake Yosefe, pokhala munthu wolungama ndiponso posafuna kumuchititsa manyazi kwa anthu,+ anaganiza zomusiya+ mwamseri.* 20  Koma ataganiza mozama za nkhani imeneyi, mngelo wa Yehova* anamuonekera m’maloto n’kumuuza kuti: “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutengera Mariya mkazi wako kunyumba, chifukwa chakuti pakati alinapopa pachitika mwa mphamvu ya mzimu woyera.+ 21  Iye adzabereka mwana wamwamuna, ndipo dzina lake udzamutche Yesu,*+ chifukwa adzapulumutsa+ anthu ake+ ku machimo awo.”+ 22  Zonsezi zinachitika kuti zimene Yehova ananena kudzera mwa mneneri+ wake zikwaniritsidwe.+ Iye anati: 23  “Tamverani! Namwali+ adzatenga pakati ndipo adzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli,”+ lotanthauza “Mulungu Ali Nafe,”+ likamasuliridwa. 24  Ndiyeno Yosefe anadzuka ndi kuchita mmene mngelo wa Yehova anamulangizira. Anatenga mkazi wake ndi kupita naye kunyumba. 25  Koma sanagone+ naye mpaka anabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo anamutcha dzina lakuti Yesu.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “anaganiza zothetsa ukwati mwamseri.” Pa mwambo wachiyuda, kuti lonjezo loti anthu adzakwatirana lithe ankatsatira dongosolo lothetsera ukwati.
Onani Zakumapeto 2.
Pa Chiheberi dzinali amati “Yesuwa,” ndipo limatanthauza “Yehova Ndiye Chipulumutso.”