Mateyu 6:1-34
6 “Samalani kuti musamachite chilungamo chanu+ pamaso pa anthu ndi cholinga chakuti akuoneni, chifukwa mukatero simudzalandira mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba.
2 Chotero pamene ukupereka mphatso zachifundo,+ usalize lipenga+ muja amachitira onyenga m’masunagoge ndi m’misewu, kuti anthu awatamande. Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse.
3 Koma iwe, pamene ukupereka mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe zimene dzanja lako lamanja likuchita,
4 kuti mphatso zako zachifundo zikhale zamseri. Ukatero Atate wako amene akuyang’ana kuseriko adzakubwezera.+
5 “Komanso pamene mukupemphera, musamachite ngati anthu onyenga. Pakuti iwo amakonda kuimirira+ m’masunagoge ndi m’mphambano za misewu ikuluikulu kuti anthu aziwaona.+ Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse.
6 Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha+ ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka.+ Ukatero Atate wako amene amaona kuchokera kosaonekako adzakubwezera.
7 Iwe popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza+ ngati mmene amachitira anthu a mitundu ina, chifukwa iwo amaganiza kuti Mulungu awamvera akanena mawu ambirimbiri.
8 Chotero inu musafanane nawo, chifukwa Mulungu Atate wanu amadziwa zimene mukufuna+ musanapemphe n’komwe.
9 “Koma inu muzipemphera motere:+
“‘Atate wathu wakumwamba, dzina+ lanu liyeretsedwe.+
10 Ufumu+ wanu ubwere. Chifuniro chanu+ chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.+
11 Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.+
12 Mutikhululukire zolakwa* zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira.*+
13 Musatilowetse m’mayesero,+ koma mutilanditse kwa woipayo.’+
14 “Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani.+
15 Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.+
16 “Pamene mukusala kudya,+ lekani kumaonetsa nkhope yachisoni ngati mmene onyenga aja amachitira. Iwo amaipitsa nkhope zawo kuti aonekere kwa anthu kuti akusala kudya.+ Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse.
17 Koma iwe, pamene ukusala kudya, dzola mafuta m’mutu mwako ndi kusamba nkhope yako,+
18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya, koma kwa Atate wako amene ali kosaoneka.+ Ukatero Atate wako amene akukuona kuchokera kosaonekako adzakubwezera.
19 “Lekani kudziunjikira chuma+ padziko lapansi, pamene njenjete* ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba.
20 Koma unjikani chuma chanu kumwamba,+ kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge,+ ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba.
21 Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.
22 “Nyale ya thupi ndi diso.+ Chotero ngati diso lako lili lolunjika pa chinthu chimodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala.
23 Koma ngati diso lako lili loipa,+ thupi lako lonse lidzachita mdima. Choncho ngati kuwala kumene kuli mwa iwe ndiko mdima, ndiye kuti mdimawo ndi wandiweyani!+
24 “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo,+ kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.+
25 “Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Lekani kudera nkhawa+ moyo wanu kuti mudzadya chiyani, kapena mudzamwa chiyani, kapenanso kuti mudzavala chiyani.+ Kodi moyo suposa chakudya, ndipo kodi thupi siliposa chovala?+
26 Onetsetsani mbalame+ zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga chakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?+
27 Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha* mwa kuda nkhawa?+
28 Komanso pa nkhani ya zovala, n’chifukwa chiyani mukuda nkhawa? Phunzirani pa mmene maluwa+ akutchire amakulira. Sagwira ntchito, ndiponso sawomba nsalu.
29 Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo+ mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.
30 Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkheza pamoto, kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, achikhulupiriro chochepa inu?+
31 Choncho musamade nkhawa+ n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’
32 Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.+
33 “Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake,+ ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.+
34 Musamade nkhawa za tsiku lotsatira,+ chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “ngongole.”
^ Mawu ake enieni, “ali nafe ngongole.”
^ Mawu amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.
^ Mawu ake enieni, “amene angatalikitse moyo wake ndi mkono umodzi.”