Mateyu 26:1-75
26 Tsopano Yesu atatsiriza kunena mawu onsewa, anauza ophunzira ake kuti:
2 “Inu mukudziwa kuti pasika achitika pakangopita masiku awiri,+ ndipo Mwana wa munthu aperekedwa kuti akapachikidwe.”+
3 Pa nthawiyi, ansembe aakulu ndiponso akulu anasonkhana m’bwalo lamkati kunyumba ya mkulu wa ansembe wotchedwa Kayafa.+
4 Iwo anali kupangana+ zoti agwire Yesu mochenjera ndi kumupha.
5 Koma anali kumangonena kuti: “Tisadzamugwire pa chikondwerero, kuopera kuti anthu angadzachite chipolowe.”+
6 Pamene Yesu anali ku Betaniya+ m’nyumba ya Simoni wakhate,+
7 kunafika mayi wina ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala muli mafuta onunkhira okwera mtengo.+ Mayiyo atayandikira Yesu, anayamba kumuthira mafutawo m’mutu pamene iye anali kudya patebulo.
8 Ophunzira ake ataona zimenezi anakwiya n’kunena kuti: “N’kuwonongeranji chonchi?+
9 Mafuta amenewa akanagulitsidwa ndalama zambiri ndipo ndalamazo zikanaperekedwa kwa anthu osauka.”+
10 Yesu anadziwa zimenezi,+ ndipo anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Iyetu wandichitira zinthu zabwino.+
11 Osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+
12 Pakuti pamene mayiyu wathira mafuta onunkhirawa pathupi langa chonchi, wachita zimenezi kukonzekera kuikidwa kwanga m’manda.+
13 Ndithu ndikukuuzani, Kulikonse kumene uthenga wabwinowu udzalalikidwe m’dziko lonse, anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzam’kumbukira.”+
14 Pambuyo pake mmodzi wa ophunzira 12 aja, wotchedwa Yudasi Isikariyoti,+ anapita kwa ansembe aakulu
15 n’kuwafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikamupereka kwa inu?”+ Iwo anamulonjeza ndalama 30 zasiliva.+
16 Choncho kuchokera pamenepo anayesetsa kufunafuna mpata wabwino umene angamuperekere.+
17 Pa tsiku loyamba la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti malo odyerako pasika?”+
18 Iye anati: “Pitani mumzinda kwa Munthu wakutiwakuti+ ndipo mukamuuze kuti, Mphunzitsi wanena kuti, ‘Nthawi yanga yoikidwiratu yayandikira. Ndidzachita phwando la pasika pamodzi ndi ophunzira anga kunyumba kwako.’”+
19 Chotero ophunzirawo anachitadi monga mmene Yesu anawalamulira, ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa pasika.+
20 Nthawi yamadzulo,+ iye ndi ophunzira ake 12 aja anali kudya chakudya patebulo.+
21 Pamene anali kudya, iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, Mmodzi wa inu andipereka.”+
22 Chifukwa chomva chisoni kwambiri ndi zimenezi, aliyense anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi ndine kapena?”+
23 Poyankha iye anati: “Amene akusunsa nane limodzi m’mbalemu ndi amene ati andipereke.+
24 Zoona, Mwana wa munthu akuchokadi, monga Malemba amanenera+ za iye, koma tsoka+ kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu!+ Zikanakhala bwino munthu ameneyu akanapanda kubadwa.”
25 Poyankha, Yudasi amene anali atatsala pang’ono kumupereka anati: “Nanga n’kukhala ine Rabi?” Iye anati: “Wanena wekha.”
26 Pamene anali kudya, Yesu anatenga mkate,+ ndipo atapempha dalitso, anaunyemanyema+ n’kuupereka kwa ophunzira ake. Iye anati: “Eni, idyani. Mkate uwu ukuimira thupi langa.”+
27 Kenako anatenga kapu+ ndipo atayamika, anaipereka kwa iwo n’kunena kuti: “Imwani nonsenu.+
28 Vinyoyu akuimira+ ‘magazi+ anga a pangano,’+ amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri+ kuti machimo akhululukidwe.+
29 Koma ndikukuuzani kuti, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa ichi chochokera ku mphesa kufikira tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano limodzi ndi inu mu ufumu wa Atate wanga.”+
30 Potsirizira pake, atatha kuimba nyimbo zotamanda Mulungu,+ anatuluka n’kupita kuphiri la Maolivi.+
31 Kenako Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthawa ndi kundisiya ndekha usiku uno, pakuti Malemba amati, ‘Ndidzapha m’busa, ndipo nkhosa za m’gululo zidzabalalika.’+
32 Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya inu musanafikeko.”+
33 Koma Petulo anamuyankha kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!”+
34 Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza iwe, Usiku womwe uno tambala asanalire, undikana katatu.”+
35 Petulo anayankha kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” Ophunzira ena onse ananenanso chimodzimodzi.+
36 Kenako Yesu anafika nawo pamalo+ otchedwa Getsemane, ndipo anauza ophunzirawo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.”+
37 Popita kumeneko anatenga Petulo ndi ana awiri+ a Zebedayo. Ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika kwambiri mumtima mwake.+
38 Kenako anawauza kuti: “Moyo wanga ukumva chisoni chofa nacho.+ Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”+
39 Choncho atapita patsogolo pang’ono, anagwada mpaka nkhope yake pansi, ndipo anapemphera+ kuti: “Atate wanga, ngati n’kotheka, kapu+ iyi indipitirire. Koma osati mwa kufuna kwanga,+ koma mwa kufuna kwanu.”+
40 Atatero anabwerera pamene panali ophunzira ake aja ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Zoona anthu inu simungathe kukhalabe maso limodzi ndi ine ola limodzi?+
41 Khalani maso+ ndipo pempherani+ kosalekeza kuti musalowe m’mayesero.+ Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+
42 Anachokanso kachiwiri+ n’kupita kukapemphera kuti: “Atate wanga, ngati sizingatheke kuti kapuyi indipitirire mpaka nditamwa ndithu, chifuniro chanu chichitike.”+
43 Anabwerera n’kuwapezanso akugona, chifukwa zikope zawo zinali zitalemera.+
44 Choncho anawasiya ndi kupitanso kukapemphera kachitatu,+ kubwereza mawu omwe aja.
45 Pambuyo pake anabwerera kwa ophunzirawo n’kuwauza kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula! Taonani! Ola lakuti Mwana wa munthu aperekedwe m’manja mwa ochimwa layandikira.+
46 Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”+
47 Mawu adakali m’kamwa, Yudasi,+ mmodzi wa ophunzira 12 aja, anafika limodzi ndi khamu lalikulu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu ndi kwa akulu, atanyamula malupanga+ ndi zibonga.+
48 Apa n’kuti womupereka ameneyu atawapatsa chizindikiro chakuti: “Amene ndim’psompsone ndi ameneyo, mum’gwire.”+
49 Atafika, Yudasi analunjika kwa Yesu n’kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu Rabi!”+ Ndipo anam’psompsona.+
50 Koma Yesu+ anamufunsa kuti: “Bwanawe, ukupezeka kuno ndi cholinga chotani?” Nthawi yomweyo iwo anayandikira ndipo anagwira Yesu ndi kum’manga.+
51 Koma wina mwa amene anali ndi Yesu anasolola lupanga lake n’kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+
52 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake,+ pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.+
53 Kapena ukuganiza kuti sindingapemphe Atate wanga kuti anditumizire magulu ankhondo oposa 12 a angelo nthawi yomwe ino?+
54 Koma ndikachita zimenezo, nanga Malemba amene ananeneratu kuti izi ziyenera kuchitika adzakwaniritsidwa bwanji?”
55 Mu ola lomwelo Yesu anafunsa khamu la anthulo kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukukalimbana ndi wachifwamba?+ Tsiku ndi tsiku ndinali kukhala pansi m’kachisi+ ndi kuphunzitsa, koma simunandigwire.
56 Koma zonsezi zachitika kuti malemba a aneneri akwaniritsidwe.”+ Kenako ophunzira ake onse anamuthawa, n’kumusiya yekha.+
57 Amene anagwira Yesu aja anapita naye kwa Kayafa+ mkulu wa ansembe, kumene alembi ndi akulu anali atasonkhana.+
58 Koma Petulo anali kumutsatirabe chapatali ndithu, mpaka anafika m’bwalo lamkati+ kunyumba ya mkulu wa ansembeyo. Atalowa mkatimo, anakhala pansi pamodzi ndi antchito a m’nyumbamo kuti aone zotsatira zake.+
59 Pa nthawiyi ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda* anali kufunafuna umboni wonama kuti amunamizire mlandu Yesu ndi kumupha+
60 koma sanaupeze, ngakhale kuti kunabwera mboni zambiri zonama.+ Patapita nthawi, kunabwera mboni zina ziwiri
61 ndi kunena kuti: “Munthu ameneyu ananena kuti, ‘Ndikhoza kugwetsa kachisi wa Mulungu ndi kumumanganso m’masiku atatu.’”+
62 Pamenepo mkulu wa ansembe anaimirira ndi kumufunsa kuti: “Kodi ukusowa choyankha? Kodi n’zoona zimene awa akukunenezazi?”+
63 Koma Yesu anangokhala chete.+ Chotero mkulu wa ansembe anati: “Ndikukulumbiritsa pali Mulungu wamoyo,+ utiuze ngati ndiwedi Khristu+ Mwana wa Mulungu!”
64 Yesu anamuyankha+ kuti: “Mwanena nokha.+ Ndipo ndikukuuzani anthu inu kuti, kuyambira tsopano+ mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera pamitambo yakumwamba.”+
65 Pamenepo mkulu wa ansembe anang’amba malaya ake akunja n’kunena kuti: “Wanyoza Mulungu!+ Nanga n’kufunanso mboni zina pamenepa?+ Pano mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu.+
66 Tsopano inu mukuona bwanji pamenepa?” Iwo anayankha kuti: “Ayenera kuphedwa basi.”+
67 Kenako anayamba kumulavulira kunkhope+ ndi kum’menya+ nkhonya. Ena anamuwomba mbama,+
68 ndi kunena kuti: “Losera tione Khristu iwe.+ Wakumenya ndani?”+
69 Tsopano Petulo anakhala pansi m’bwalo lamkati, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye n’kunena kuti: “Inunso munali ndi Yesu wa ku Galileyayu!”+
70 Koma iye anakana pamaso pa onse kuti: “Sindikudziwa zimene ukunena.”
71 Atatuluka n’kupita kukanyumba kapachipata, mtsikana wina anamuzindikira ndi kuuza ena amene anali pafupi kuti: “Bambo awa anali limodzi ndi Yesu Mnazaretiyu.”+
72 Apanso Petulo anakana mochita kulumbira ndipo ananena kuti: “Ndithudi munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!”+
73 Patapita kanthawi pang’ono, amene anali ataimirira chapafupi anabwera ndi kuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli m’gulu la ophunzira ake. Ndipo kalankhulidwe kako kakugwiritsa.”+
74 Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira kuti: “Munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” Nthawi yomweyo tambala analira.+
75 Tsopano Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja, akuti: “Tambala asanalire, udzandikana katatu.”+ Ndipo anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”