Mateyu 15:1-39

15  Pa nthawiyo Afarisi ndi alembi ochokera ku Yerusalemu anabwera kwa Yesu.+ Iwo anam’funsa kuti:  “N’chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya miyambo ya makolo? Mwachitsanzo, sasamba m’manja* akafuna kudya chakudya.”+  Koma iye anawayankha kuti: “N’chifukwa chiyani inunso mumaphwanya malamulo a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?+  Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’+  Koma inu mumanena kuti, ‘Aliyense wouza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ine ndili nacho, chimene ndikanakuthandizirani, ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,”  asalemekeze bambo ake.’+ Chotero mwasandutsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake chifukwa cha miyambo yanu.+  Onyenga inu!+ Yesaya+ analosera moyenera za inu muja anati,  ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mtima wawo uli kutali ndi ine.+  Amandipembedza pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.’”+ 10  Atanena izi, anaitana khamu la anthu kuti liyandikire, ndipo anawauza kuti: “Mvetserani ndipo muzindikire tanthauzo lake:+ 11  Chimene chimalowa m’kamwa sichiipitsa munthu, koma chotuluka m’kamwa mwake n’chimene chimaipitsa munthu.”+ 12  Kenako ophunzira ake anafika ndi kumufunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti Afarisi akhumudwa ndi zimene mwanena zija?”+ 13  Koma iye anayankha kuti: “Mbewu iliyonse imene sinabzalidwe ndi Atate wanga wakumwamba idzazulidwa.+ 14  Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Chotero ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.”+ 15  Ndiyeno Petulo anam’pempha kuti: “Timasulireni fanizo lija.”+ 16  Pamenepo Yesu ananena kuti: “Kodi inunso mudakali osazindikira?+ 17  Inunso simudziwa kodi kuti chilichonse cholowa m’kamwa chimadutsa m’matumbo ndipo chimakatayidwa kuchimbudzi? 18  Koma zotuluka m’kamwa zimachokera mumtima, ndipo zimenezo zimaipitsa munthu.+ 19  Mwachitsanzo, maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za kuba, maumboni onama, ndi zonyoza Mulungu,+ zimachokera mumtima.+ 20  Izi n’zimene zimaipitsa munthu, koma kudya chakudya osasamba m’manja sikuipitsa munthu.”+ 21  Tsopano Yesu anachoka kumeneko ndi kupita m’zigawo za Turo ndi Sidoni.+ 22  Ndiyeno kunabwera mayi wina wa ku Foinike+ kuchokera m’zigawo zimenezo ndi kufuula kuti: “Ndichitireni chifundo+ Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi wagwidwa ndi chiwanda mochititsa mantha.” 23  Koma iye sanamuyankhe chilichonse. Choncho ophunzira ake anabwera ndi kum’pempha kuti: “Muuzeni kuti azipita, chifukwa akupitirizabe kufuula m’mbuyo mwathumu.” 24  Poyankha iye anati: “Ine sananditumize kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.”+ 25  Mayi uja atafika pafupi, anam’gwadira ndi kunena kuti: “Ambuye, ndithandizeni!”+ 26  Iye anamuyankha kuti: “Si bwino kutenga chakudya cha ana n’kuponyera tiagalu.” 27  Koma mayiyo anati: “Inde Ambuye, komatu tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa patebulo la ambuye awo.”+ 28  Pamenepo Yesu anamuyankha kuti: “Mayi iwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu. Zimene ukufuna zichitike kwa iwe.” Ndipo kuchokera mu ola limenelo mwana wake anachira.+ 29  Atachoka kumeneko, Yesu anafika pafupi ndi nyanja ya Galileya,+ ndipo anakwera m’phiri+ ndi kukhala pansi m’phirimo. 30  Kenako anthu ochuluka anakhamukira kwa iye. Anabwera ndi anthu olumala, othyoka ziwalo, akhungu, osalankhula, ndi ena ambiri osiyanasiyana, moti anawakhazika pamapazi ake mochita ngati akum’ponyera, ndipo anawachiritsa onsewo.+ 31  Khamu la anthulo linadabwa kuona osalankhula akulankhula, olumala akuyenda ndiponso akhungu akuona, ndipo anatamanda Mulungu wa Isiraeli.+ 32  Koma Yesu anaitana ophunzira ake n’kunena kuti:+ “Khamu la anthuli likundimvetsa chisoni,+ chifukwa anthuwa akhala ndi ine masiku atatu tsopano ndipo alibe chakudya. Sindikufuna kuwauza kuti azipita asanadye, chifukwa angalenguke panjira.” 33  Koma ophunzirawo anamuuza kuti: “Kopanda anthu ngati kuno tiipeza kuti mitanda ya mkate yokwanira khamu lonseli?”+ 34  Kenako Yesu anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Iwo anayankha kuti: “Tili nayo 7, ndi tinsomba towerengeka.” 35  Chotero atauza anthuwo kuti akhale pansi, 36  anatenga mitanda 7 ya mkate ija ndi nsomba zija. Atayamika, anainyemanyema n’kupatsa ophunzirawo ndipo iwo anagawira khamu la anthulo.+ 37  Anthu onsewo anadya ndi kukhuta, moti zotsala zimene anatolera zinadzaza madengu akuluakulu 7.+ 38  Koma amene anadya anali amuna 4,000, osawerengera akazi ndi ana aang’ono. 39  Pambuyo pake, atauza anthuwo kuti azipita kwawo, iye anakwera ngalawa n’kufika m’zigawo za Magadani.+

Mawu a M'munsi

Izi sizikutanthauza kuti anali kudya ndi m’manja mwakuda, koma kuti sanali kutsatira miyambo yachiyuda yosambira m’manja.