Mateyu 22:1-46
22 Popitiriza kuwayankha, Yesu anawauzanso mafanizo ena kuti:+
2 “Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati+ wa mwana wake.
3 Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa ku phwando laukwati,+ koma anthuwo sanafune kubwera.+
4 Kenako inatumanso akapolo ena+ kuti, ‘Kauzeni oitanidwawo kuti: “Ine ndakonza chakudya chamasana,+ ng’ombe zanga komanso nyama zanga zonenepa zaphedwa, ndipo zinthu zonse zakonzedwa kale. Bwerani ku phwando laukwati.”’+
5 Koma anthuwo ananyalanyaza ndi kuchoka. Wina anapita kumunda wake, wina kumalonda ake.+
6 Koma enawo anagwira akapolo akewo, ndi kuwachitira zachipongwe n’kuwapha.+
7 “Pamenepo mfumu ija inakwiya kwambiri, ndipo inatumiza asilikali ake kukawononga opha anthu amenewo ndi kutentha mzinda wawo.+
8 Kenako anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzedwa ndithu, koma oitanidwa aja anali osayenera.+
9 Chotero pitani m’misewu yotuluka mumzinda, ndipo aliyense amene mukam’peze, mukamuitanire phwando laukwatili.’+
10 Choncho akapolowo anapita m’misewu ndi kusonkhanitsa onse amene anawapeza, oipa ndi abwino omwe.+ Ndipo chipinda chodyeramo phwando laukwati chinadzaza ndi anthu oyembekezera kulandira chakudya.+
11 “Pamene mfumu ija inalowa kukayendera alendowo, inaona munthu wina mmenemo amene sanavale chovala chaukwati.+
12 Chotero inamufunsa kuti, ‘Bwanawe! Walowa bwanji muno usanavale chovala cha ukwati?’+ Iye anasowa chonena.
13 Kenako mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘M’mangeni manja ndi miyendo ndipo mum’ponye kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’+
14 “Pakuti oitanidwa ndi ambiri, koma osankhidwa ndi owerengeka.”+
15 Pamenepo Afarisi anachoka ndi kukapangana kuti am’kole m’mawu ake.+
16 Choncho anamutumizira ophunzira awo, limodzi ndi achipani cha Herode,+ ndipo iwo anati: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo mumaphunzitsa njira ya Mulungu m’choonadi, ndiponso simusamala kuti uyu ndani, chifukwa simuyang’ana maonekedwe a anthu.+
17 Ndiye tatiuzani, Mukuganiza bwanji? Kodi n’kololeka kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”+
18 Koma Yesu, podziwa kuipa mtima kwawo, ananena kuti: “Onyenga inu! Bwanji mukundiyesa?+
19 Ndionetseni khobidi la msonkho.” Pamenepo anam’bweretsera khobidi limodzi la dinari.
20 Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi ndi mawu akewa n’zandani?”+
21 Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” Pamenepo iye anawauza kuti: “Ndiye perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”+
22 Atamva zimenezi, anadabwa ndipo anangochokapo n’kumusiya.+
23 Pa tsikulo Asaduki, amene amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa iye n’kumufunsa kuti:+
24 “Mphunzitsi, Mose anati, ‘Ngati munthu wamwalira wopanda ana, m’bale wake ayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana.’+
25 Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira kenako n’kumwalira. Koma popeza kuti analibe ana, mkazi uja anakwatiwa ndi m’bale wa mwamuna wake.+
26 Zinachitika chimodzimodzi kwa wachiwiri ndi wachitatu, mpaka kwa onse 7 aja.+
27 Pamapeto pake mkaziyo nayenso anamwalira.
28 Kodi pamenepa, pouka kwa akufa, mkazi ameneyu adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatira?”+
29 Koma Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.+
30 Pakuti pouka kwa akufa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa,+ koma adzakhala ngati angelo akumwamba.
31 Kunena za kuuka kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti,+
32 ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?+ Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa.”+
33 Pakumva zimenezo, khamu la anthulo linadabwa ndi zimene anali kuphunzitsa.+
34 Afarisi atamva kuti Yesu anawasowetsa chonena Asaduki, anasonkhana monga gulu limodzi.
35 Ndipo mmodzi wa iwo, wodziwa Chilamulo,+ anafunsa Yesu momuyesa kuti:
36 “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?”+
37 Iye anamuyankha kuti: “‘Uzikonda Yehova* Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’+
38 Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba.
39 Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+
40 Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa, kuphatikizaponso Zolemba za aneneri.”+
41 Tsopano Afarisi aja atasonkhana pamodzi Yesu anawafunsa kuti:+
42 “Mukuganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi mwana wa Davide.”+
43 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani mouziridwa ndi mzimu,+ Davide anamutcha ‘Ambuye,’ muja anati,
44 ‘Yehova wauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako”’?+
45 Chotero ngati Davide anamutcha kuti ‘Ambuye,’ akukhala bwanji mwana wake?”+
46 Koma panalibe ngakhale mmodzi amene anatha kumuyankha, ndipo kuchokera tsiku limenelo palibe amene analimbanso mtima kumufunsa mafunso.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 2.