Mateyu 3:1-17

3  M’masiku amenewo, Yohane M’batizi+ anapita m’chipululu+ cha Yudeya n’kuyamba kulalikira.  Iye anali kulalikira kuti: “Lapani,+ pakuti ufumu wakumwamba wayandikira.”+  Mneneri Yesaya ananenera za iyeyu+ m’mawu awa: “Tamverani! Winawake akufuula m’chipululu kuti, ‘Konzani+ njira ya Yehova anthu inu! Wongolani misewu yake.’”  Koma Yohane ameneyu, anali kuvala chovala chaubweya wa ngamila+ ndi lamba wachikopa+ m’chiuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe+ ndi uchi.+  Choncho anthu ochokera ku Yerusalemu ndi ku Yudeya konse ndiponso ochokera m’midzi yonse yapafupi ndi Yorodano anali kubwera kwa iye.  Iye anali kuwabatiza mumtsinje wa Yorodano,+ ndipo anthuwo anali kuulula machimo awo poyera.  Pamene Yohane anaona Afarisi ndi Asaduki+ ambiri akubwera ku ubatizowo, anawauza kuti: “Ana a njoka inu,+ ndani wakuchenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwerawo?+  Ndiyetu mubale zipatso zosonyeza kulapa.+  Musamadzinyenge kuti, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’+ Pakuti ndikukuuzani kuti Mulungu angathe kuutsira Abulahamu+ ana kuchokera kumiyala iyi. 10  Nkhwangwa+ yaikidwa kale pamizu yamitengo. Chotero mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa+ ndi kuponyedwa pamoto.+ 11  Inetu ndikukubatizani m’madzi+ chifukwa cha kulapa kwanu,+ koma amene akubwera+ m’mbuyo mwanga ndi wamphamvu kuposa ine, ndipo sindili woyenera kumuvula nsapato zake.+ Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyera+ komanso ndi moto.+ 12  Fosholo yake youluzira mankhusu* ili m’manja mwake, ndipo malo ake opunthirapo mbewu adzawayeretseratu kuti mbee! Tirigu adzamututira m’nkhokwe,+ koma mankhusu adzawatentha+ ndi moto umene sungazimitsidwe.” 13  Kenako Yesu anabwera kwa Yohane ku Yorodano kuchokera ku Galileya,+ kuti iye amubatize.+ 14  Koma Yohane anayesa kumuletsa ponena kuti: “Ine ndiye wofunika kubatizidwa ndi inu, nanga inu mukubweranso kwa ine kodi?” 15  Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Pa nthawi ino lola kuti zikhale choncho, chifukwa n’koyenera kwa ife kutero kuti tikwaniritse chilungamo chonse.”+ Atatero, anasiya kumuletsa. 16  Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka,+ ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda+ kudzamutera.+ 17  Panamvekanso mawu+ ochokera kumwamba onena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga+ wokondedwa,+ amene ndimakondwera naye.”+

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.