Mateyu 5:1-48

5  Ataona khamu la anthu, anakwera m’phiri. Atakhala pansi, ophunzira ake anabwera kwa iye.  Kenako anayamba kuwaphunzitsa kuti:  “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu,+ chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.+  “Odala ndi anthu amene akumva chisoni, chifukwa adzasangalatsidwa.+  “Odala ndi anthu amene ali ofatsa,+ chifukwa adzalandira dziko lapansi.+  “Odala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu+ la chilungamo, chifukwa adzakhuta.+  “Odala ndi anthu achifundo,+ chifukwa adzachitiridwa chifundo.  “Odala ndi anthu oyera mtima,+ chifukwa adzaona Mulungu.+  “Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere,+ chifukwa adzatchedwa ‘ana+ a Mulungu.’ 10  “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa+ chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo. 11  “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani+ ndi kukuzunzani,+ komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. 12  Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe,+ chifukwa mphoto+ yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri+ amene analipo inu musanakhaleko. 13  “Inu ndinu mchere+ wa dziko lapansi. Koma ngati mchere watha mphamvu, kodi mphamvu yake angaibwezeretse motani? Sungagwire ntchito iliyonse koma ungafunike kuutaya kunja+ kumene anthu akaupondaponda. 14  “Inu ndinu kuwala kwa dziko.+ Mzinda ukakhala paphiri subisika. 15  Anthu akayatsa nyale, saivundikira ndi dengu,+ koma amaiika pachoikapo nyale ndipo imaunikira onse m’nyumbamo. 16  Momwemonso, onetsani kuwala+ kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino+ ndi kuti alemekeze+ Atate wanu wakumwamba. 17  “Musaganize kuti ndinabwera kudzawononga Chilamulo+ kapena Zolemba za aneneri. Sindinabwere kudzaziwononga koma kudzazikwaniritsa.+ 18  Ndithu ndikukuuzani kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingachoke mosavuta,+ kusiyana n’kuti kalemba kochepetsetsa kapena kachigawo kamodzi ka lemba kachoke m’Chilamulo zinthu zonse zisanachitike.+ 19  Chotero aliyense wophwanya+ lililonse la malamulo aang’ono awa ndi kuphunzitsa anthu kuphwanya malamulowo, adzakhala ‘wosayenera kulowa’ mu ufumu wakumwamba.+ Koma aliyense wotsatira ndi kuphunzitsa malamulowa,+ ameneyo adzakhala ‘woyenera kulowa’+ mu ufumu wakumwamba. 20  Pakuti ndikukuuzani inu kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha alembi ndi Afarisi,+ ndithudi simudzalowa+ mu ufumu wakumwamba. 21  “Inu munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti ‘Usaphe munthu.+ Aliyense amene wapha mnzake+ wapalamula mlandu wa kukhoti.’+ 22  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiriza kupsera mtima+ m’bale wake wapalamula mlandu+ wa kukhoti. Komano aliyense wonenera m’bale wake mawu achipongwe wapalamula mlandu wa ku Khoti Lalikulu. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe!’ adzapita ku Gehena* wamoto.+ 23  “Choncho ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe,+ ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa,+ 24  siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba,+ ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.+ 25  “Thetsa nkhani mofulumira ndi munthu wokuimba mlandu pamene ukupita naye kukhoti, kuti mwina wokuimba mlanduyo+ asakakupereke kwa woweruza. Komanso kuti woweruzayo asakakupereke kwa msilikali wa pakhoti kuti akuponye m’ndende. 26  Kunena zoona, sudzatulukamo kufikira utalipira kakhobidi kotsirizira.+ 27  “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’+ 28  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi+ mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo+ mumtima mwake.+ 29  Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa,* ulikolowole ndi kulitaya.+ Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe+ m’Gehena. 30  Komanso ngati dzanja lako lamanja limakuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya.+ Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe m’Gehena. 31  “Pajanso anati, ‘Aliyense wothetsa ukwati+ ndi mkazi wake, apatse mkaziyo kalata yothetsera ukwati.’+ 32  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wothetsa ukwati ndi mkazi wake, osati chifukwa cha dama,*+ amamuchititsa chigololo akakwatiwanso,+ ndipo aliyense wokwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.+ 33  “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire+ koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’+ 34  Koma ine ndikukuuzani kuti: Usamalumbire+ n’komwe, kutchula kumwamba, chifukwa ndi kumene kuli mpando wachifumu wa Mulungu,+ 35  kapena kutchula dziko lapansi chifukwa ndi chopondapo mapazi ake,+ kapena kutchula Yerusalemu chifukwa ndi mzinda+ wa Mfumu yaikulu. 36  Kapena usalumbire kutchula mutu wako, chifukwa sungathe kusandutsa ngakhale tsitsi limodzi kukhala loyera kapena lakuda. 37  Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi,+ pakuti mawu owonjezera pamenepa achokera kwa woipayo.+ 38  “Inu munamva kuti anati, ‘Diso kulipira diso, ndi dzino kulipira dzino.’+ 39  Koma ine ndikukuuzani kuti: Usalimbane ndi munthu woipa, koma wina akakumenya mbama patsaya lakumanja,+ umutembenuzirenso linalo. 40  Ngati munthu akufuna kukutengera kukhoti kuti akulande malaya ako amkati, m’patsenso akunja.+ 41  Winawake waudindo akakulamula kuti umunyamulire katundu mtunda wa kilomita imodzi, umunyamulire mtunda wa makilomita awiri.+ 42  Munthu akakupempha kanthu m’patse, ndipo munthu wofuna kukongola kanthu kwa iwe popanda chiwongoladzanja usamukanize.+ 43  “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnzako+ ndi kudana ndi mdani wako.’+ 44  Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu+ ndi kupempherera amene akukuzunzani,+ 45  kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.+ Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.+ 46  Pakuti mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzalandira mphoto yotani?+ Kodi okhometsa msonkho sachitanso zimenezo? 47  Ngati mupatsa moni abale anu okha, kodi n’chiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu ina nawonso sachita zomwezo? 48  Choncho khalani angwiro, monga mmene Atate wanu wakumwamba alili wangwiro.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 6.
Mawu ake enieni, “limakupunthwitsa.”
Onani Zakumapeto 7.