Mateyu 16:1-28
16 Kenako Afarisi+ ndi Asaduki anafika kwa Yesu. Pofuna kumuyesa, anam’pempha kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.+
2 Koma Yesu anawayankha kuti: “[[Kunja kukamada mumanena kuti, ‘Nyengo ikhala yabwino, chifukwa kumwamba kwachita cheza.’
3 Koma m’mawa mumanena kuti, ‘Lero kukuoneka kuti kugwa mvula, chifukwa kumwamba kwachita cheza koma kuli mdima wamvula.’ Mumadziwa kumasulira kaonekedwe ka kumwamba, koma simungathe kumasulira zizindikiro za nthawi ino.]]*+
4 M’badwo woipa ndi wachigololo ukufunitsitsabe chizindikiro, koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse+ kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.”+ Atanena izi, anachoka n’kuwasiya.+
5 Tsopano ophunzira ake anawolokera kutsidya lina koma anaiwala kutenga mikate.+
6 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Khalani maso ndipo samalani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi Asaduki.”+
7 Koma iwo anayamba kukambirana kuti: “Sitinatenge mikate pobwera kuno.”
8 Yesu anadziwa zimenezi ndipo ananena kuti: “Inu achikhulupiriro chochepa, mulibe mikate. Ndiye n’chifukwa chiyani mukukambirana zimenezi?+
9 Kodi mfundo yake simukuimvetsabe? Kapena kodi simukukumbukira anthu 5,000 amene anadya mitanda isanu ya mkate, komanso kuchuluka kwa madengu a zotsalira zimene munatolera?+
10 Kapena kodi simukukumbukira anthu 4,000 amene anadya mitanda 7 ya mkate, komanso kuchuluka kwa madengu akuluakulu a zotsalira zimene munatolera?+
11 Nanga bwanji simukuzindikira kuti sindikunena za mitanda ya mkate? Koma samalani ndi zofufumitsa za Afarisi ndi Asaduki.”+
12 Pamenepo anazindikira kuti sakunena kuti asamale ndi zofufumitsa mitanda ya mkate, koma kuti asamale ndi zimene Afarisi ndi Asaduki amaphunzitsa.+
13 Tsopano atafika m’zigawo za Kaisareya wa Filipi, Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu akumanena kuti Mwana wa munthu ndani?”+
14 Iwo anayankha kuti: “Ena akumanena kuti Yohane M’batizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akuti Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.”
15 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?”+
16 Poyankha, Simoni Petulo ananena kuti: “Ndinu Khristu,+ Mwana wa Mulungu wamoyo.”+
17 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, chifukwa si munthu* amene wakuululira zimenezi, koma Atate wanga amene ali kumwamba wachita zimenezi.+
18 Chotero inenso ndikukuuza kuti, Iwe ndiwe Petulo,+ ndipo pathanthwe+ ili ndidzamangapo mpingo wanga. Zipata za Manda+ sizidzaugonjetsa.+
19 Ine ndidzakupatsa makiyi a ufumu wakumwamba. Chilichonse chimene udzamanga padziko lapansi chidzakhala chitamangidwa kumwamba, ndipo chilichonse chimene udzamasula padziko lapansi chidzakhala chitamasulidwa kumwamba.”+
20 Pamenepo analamula ophunzirawo mwamphamvu kuti asauze aliyense kuti iye ndi Khristu.+
21 Kuyambira pamenepo, Yesu Khristu anayamba kuuza ophunzira ake kuti n’koyenera kuti iye apite ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+
22 Kenako Petulo anamutengera pambali ndi kuyamba kum’dzudzula kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.”+
23 Koma iye anatembenuka n’kuuza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana!+ Ndiwe chopunthwitsa kwa ine, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu,+ koma maganizo a anthu.”
24 Kenako Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo* ndipo anditsatire mosalekeza.+
25 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.+
26 Kodi munthu angapindulenji ngati atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake?+ Kapena munthu angapereke chiyani chosinthanitsa+ ndi moyo wake?
27 Pakuti Mwana wa munthu adzabwera ndithu mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo ake. Pa nthawi imeneyo adzapatsa aliyense mphoto malinga ndi makhalidwe ake.+
28 Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe kufikira choyamba ataona Mwana wa munthu akubwera monga mfumu.”+
Mawu a M'munsi
^ Mikutiramawu yophatikiza ikusonyeza mawu amene m’mipukutu ina yakale mulibe koma akupezeka m’mipukutu ina.
^ Mawu ake enieni, “mnofu ndi magazi.”
^ Onani Zakumapeto 9.