Mateyu 18:1-35

18  Pa nthawi imeneyo, ophunzira anayandikira Yesu ndi kunena kuti: “Ndani kwenikweni amene adzakhala wamkulu kwambiri mu ufumu wakumwamba?”+  Pamenepo iye anaitana mwana wamng’ono n’kumuimika pakati pawo+  ndi kunena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Mukapanda kutembenuka n’kukhala ngati ana aang’ono,+ simudzalowa mu ufumu wakumwamba.+  Chotero, aliyense amene adzadzichepetsa+ ngati mwana wamng’ono uyu ndi amene adzakhala wamkulu kwambiri mu ufumu wakumwamba.+  Ndiponso aliyense wolandira mwana wamng’ono ngati ameneyu m’dzina langa walandiranso ine.+  Koma aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana iti timene timakhulupirira mwa ine, zingamukhalire bwino kwambiri kumumangirira chimwala cha mphero+ m’khosi mwake, ngati chimene bulu amayendetsa, ndi kumumiza m’nyanja yaikulu.+  “Tsoka dzikoli chifukwa cha zopunthwitsa! Inde sitingachitire mwina, zopunthwitsazo ziyenera kubwera ndithu,+ koma tsoka lili kwa munthu wobweretsa chopunthwitsa!+  Chotero ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule ndi kulitaya kutali.+ Ndi bwino kuti ukapeze moyo ulibe chiwalo chimodzi kapena uli wolumala kusiyana ndi kuti ukaponyedwe m’moto wosatha uli ndi manja onse awiri kapena mapazi onse awiri.+  Komanso ngati diso lako limakupunthwitsa ulikolowole n’kulitaya. Ndi bwino kuti ukapeze moyo uli ndi diso limodzi kusiyana ndi kuti ukaponyedwe mu Gehena* wamoto uli ndi maso onse awiri.+ 10  Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo+ kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.+ 11 * —— 12  “Mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusochera,+ kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo?+ 13  Akaipeza, ndithu ndikunenetsa, amakondwera kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zosasochera zija.+ 14  Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.+ 15  “Komanso, ngati m’bale wako wachimwa, upite kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo.+ Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo.+ 16  Koma akapanda kukumvera, upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.+ 17  Akapanda kuwamvera amenewanso, uuze mpingo. Ndipo akapandanso kumvera mpingowo, kwa iwe akhale ngati munthu wochokera mu mtundu wina+ komanso ngati wokhometsa msonkho.+ 18  “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, zilizonse zimene mudzamanga padziko lapansi zidzakhala zitamangidwa kumwamba, ndipo zilizonse zimene mudzamasula padziko lapansi zidzakhala zitamasulidwa kumwamba.+ 19  Ndiponso ndikukuuzani kuti, ngati awiri mwa inu padziko lapansi pano adzagwirizana pa chilichonse chofunika kupempha, Atate wanga wakumwamba adzawachitira.+ 20  Pakuti kulikonse kumene awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa,+ ine ndidzakhala pakati pawo.”+ 21  Kenako Petulo anabwera kwa iye ndi kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi m’bale wanga angandichimwire kangati ndipo ine n’kumukhululukira?+ Mpaka nthawi 7 kodi?”+ 22  Yesu anayankha kuti: “Ndikukuuza kuti, osati nthawi 7 zokha ayi, koma, Mpaka nthawi 77.+ 23  “N’chifukwa chake ufumu wakumwamba uli ngati mfumu+ imene inafuna kuti akapolo ake abweze ngongole.+ 24  Itayamba kulandira ngongolezo, atumiki ake anabweretsa munthu amene anali ndi ngongole ya matalente 10,000 [omwe ndi madinari 60 miliyoni] kwa mfumuyo. 25  Koma popeza kuti analibe choti apereke pobweza ngongoleyo, mbuye wake analamula kuti mwamuna ameneyu, mkazi wake, ana ake komanso zonse zimene anali nazo zigulitsidwe ndi kum’bwezera ndalama zake.+ 26  Pamenepo kapoloyu anagwada pansi ndi kuyamba kumuweramira n’kunena kuti, ‘Ndilezereniko mtima chonde, ndidzakubwezerani zonse.’ 27  Izi zinamvetsa chisoni mbuyeyo ndipo anamusiya kapoloyo+ ndi kumukhululukira ngongole yake ija.+ 28  Koma kapoloyo atatuluka anakumana ndi kapolo mnzake amene iye anamukongoza madinari 100.+ Iye anamugwira ndi kumukanyanga pakhosi, n’kunena kuti, ‘Bweza ngongole ija mwamsanga.’ 29  Kapolo mnzakeyo anagwada pansi ndi kuyamba kumudandaulira kuti, ‘Mundilezereko mtima chonde,+ ndidzakubwezerani.’ 30  Koma iye sanalole, ndipo anapita kukam’pereka kundende mpaka pamene adzabweze ngongoleyo. 31  Akapolo anzake ataona zimene zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita kwa mbuye wawo ndi kukafotokoza zonse zimene zinachitika.+ 32  Ndiyeno mbuye wakeyo anamuitanitsa ndi kumuuza kuti, ‘Kapolo woipa iwe, ine ndakukhululukira ngongole yonse ija utandidandaulira. 33  Kodi nawenso sukanam’chitira chifundo+ kapolo mnzako, monga momwe ine ndinakuchitira chifundo?’+ 34  Pamenepo mbuye wakeyo anakwiya,+ ndipo anamupereka kwa oyang’anira ndende, mpaka pamene adzabweze ngongole yonse. 35  Mofanana ndi zimenezi,+ Atate wanga wakumwamba adzathana ndi inu ngati aliyense wa inu sakhululukira m’bale wake ndi mtima wonse.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 6.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.