Mateyu 21:1-46

21  Tsopano anayandikira ku Yerusalemu, ndipo atafika ku Betefage paphiri la Maolivi, Yesu anatuma ophunzira awiri+  n’kuwauza kuti: “Pitani m’mudzi umene mukuuonawo. Kumeneko mukapeza bulu atam’mangirira limodzi ndi mwana wake wamphongo. Mukawamasule ndi kuwabweretsa kwa ine.+  Wina aliyense akakakufunsani chilichonse, mukanene kuti, ‘Ambuye akuwafuna.’ Ndipo nthawi yomweyo akawatumiza kuno.”  Izi zinachitikadi kuti zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri zikwaniritsidwe, zakuti:  “Uzani mwana wamkazi wa Ziyoni kuti, ‘Taona! Mfumu yako ikubwera kwa iwe.+ Ndi yofatsa+ ndipo yakwera bulu wamng’ono wamphongo, mwana wa nyama yonyamula katundu.’”+  Choncho ophunzirawo ananyamuka ndi kukachita zimene Yesu anawalamula.  Iwo anabweretsa bulu uja limodzi ndi mwana wake wamphongo. Kenako anayala malaya awo akunja pa abuluwo ndipo iye anakwerapo.+  Anthu ambiri m’khamulo anayala malaya awo akunja+ mumsewu ndipo ena anayamba kudula nthambi za mitengo n’kuziyala mumsewu.+  Koma khamu la anthu, limene linali patsogolo pake ndi m’mbuyo mwake linali kufuula kuti: “M’pulumutseni+ Mwana wa Davide!+ Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!*+ M’pulumutseni kumwambamwambako!”+ 10  Tsopano atalowa mu Yerusalemu,+ mzinda wonse unagwedezeka. Ena anali kufunsa kuti: “Kodi ameneyu ndani?” 11  Khamu la anthulo linali kuyankha kuti: “Ameneyu ndi mneneri+ Yesu, wochokera ku Nazareti, ku Galileya!” 12  Kenako Yesu analowa m’kachisi ndi kuthamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda.+ 13  Iye anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,’+ koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”+ 14  Anthu akhungu ndi olumala anabwera kwa iye m’kachisimo, ndipo anawachiritsa. 15  Ansembe aakulu ndi alembi ataona zodabwitsa zimene anachitazo+ komanso anyamata amene anali kufuula m’kachisimo kuti: “M’pulumutseni+ Mwana wa Davide!”+ anakwiya kwambiri 16  ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukumva zimene awa akunenazi?” Yesu anayankha kuti: “Inde. Kodi simunawerenge+ zimenezi kuti, ‘M’kamwa mwa ana ndi mwa ana oyamwa mwaikamo mawu otamanda’?”+ 17  Kenako iye anawasiya n’kutuluka mumzindawo kupita ku Betaniya, ndipo anagona kumeneko.+ 18  Pamene anali kubwerera kumzinda uja m’mawa, anamva njala.+ 19  Kenako anaona mkuyu m’mbali mwa msewu ndipo atapita pomwepo, sanapezemo chilichonse+ koma masamba okhaokha. Choncho anauza mtengowo kuti: “Kuyambira lero sudzabalanso zipatso kwamuyaya.”+ Ndipo mkuyuwo unafota nthawi yomweyo. 20  Ophunzira aja ataona zimenezi, anadabwa ndi kunena kuti: “Zatheka bwanji kuti mkuyuwu ufote nthawi yomweyi?”+ 21  Poyankha Yesu ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro, osakayika,+ mudzatha kuchita zimene ndachitira mkuyu umenewu. Komanso kuposa pamenepa, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano ukadziponye m’nyanja,’ ndipo zidzachitikadi.+ 22  Chinthu chilichonse chimene mudzapempha m’mapemphero anu, mudzalandira ngati muli ndi chikhulupiriro.”+ 23  Tsopano Yesu analowa m’kachisi, ndipo pamene anali kuphunzitsa, ansembe aakulu ndiponso akulu anabwera kwa iye ndi kumufunsa kuti:+ “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 24  Poyankha Yesu anati: “Inenso ndikufunsani chinthu chimodzi. Mukandiuza chinthu chimenecho, inenso ndikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi:+ 25  Kodi ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?”+ Koma iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’+ 26  Komanso sitinganene kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ chifukwa tikuopa khamu la anthuli,+ pakuti onsewa amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.”+ 27  Chotero poyankha Yesu, iwo anati: “Sitikudziwa.” Nayenso anati: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.+ 28  “Kodi mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana awiri.+ Ndipo anapita kwa mwana woyamba n’kumuuza kuti: ‘Mwana wanga, lero upite kukagwira ntchito m’munda wa mpesa.’ 29  Iye poyankha anati, ‘Ndipita bambo,’+ koma sanapite. 30  Kenako anapita kwa mwana wachiwiri uja n’kumuuzanso chimodzimodzi. Iye poyankha anati, ‘Ayi sindipita.’ Koma pambuyo pake anamva chisoni+ ndipo anapita. 31  Ndani mwa ana awiriwa amene anachita chifuniro cha bambo ake?”+ Iwo anati: “Wachiwiriyu.” Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti okhometsa msonkho ndi mahule akukusiyani m’mbuyo n’kukalowa mu ufumu wa Mulungu. 32  Pakuti Yohane anabwera kwa inu m’njira yachilungamo,+ koma inu simunam’khulupirire.+ Koma okhometsa msonkho ndi mahule anam’khulupirira,+ Ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunamve chisoni n’kusintha maganizo anu kuti mum’khulupirire. 33  “Mverani fanizo lina: Panali munthu wina yemwe analima munda wa mpesa+ ndi kumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa ndi kumanga nsanja.+ Atatero anausiya m’manja mwa alimi n’kupita kudziko lina.+ 34  Nyengo ya zipatso itafika, anatumiza akapolo ake kwa alimiwo kuti akatenge zipatso zake. 35  Koma alimi aja anagwira akapolo ake aja ndipo mmodzi anam’menya, wina anamupha, wina anam’ponya miyala.+ 36  Anatumizanso akapolo ena ambiri kuposa oyamba aja, koma amenewa anawachitanso chimodzimodzi.+ 37  Pamapeto pake anawatumizira mwana wake, n’kunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ 38  Alimiwo ataona mwanayo anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe ndi kutenga cholowa chakecho!’+ 39  Choncho anamugwira ndi kum’tulutsa m’munda wa mpesawo n’kumupha.+ 40  Chotero, kodi mwinimunda wa mpesa uja akadzabwera, adzachita nawo chiyani alimiwo?” 41  Iwo anayankha kuti: “Chifukwa chakuti ndi oipa, adzawawononga koopsa+ ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa alimi ena, amene angam’patse zipatso m’nyengo yake.”+ 42  Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Kodi simunawerenge zimene Malemba amanena zakuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana+ ndi umene wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.+ Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’? 43  Ichi n’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu n’kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.+ 44  Komanso munthu wogwera pamwala umenewu adzaphwanyika. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, udzamupereratu.”+ 45  Tsopano ansembe aakulu ndi Afarisi atamvetsera mafanizo akewa, anazindikira kuti anali kunena za iwo.+ 46  Komabe, ngakhale kuti anali kufunafuna mpata wakuti amugwire, ankaopa khamu la anthu, chifukwa anthuwo anali kukhulupirira kuti iye ndi mneneri.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.