Mateyu 10:1-42
10 Chotero anaitana ophunzira ake 12 aja ndi kuwapatsa ulamuliro pa mizimu yonyansa,+ kuti athe kuitulutsa ndi kuchiritsa matenda a mtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.
2 Mayina a atumwi 12+ aja ndi awa:+ Simoni, wotchedwa Petulo,*+ ndi Andireya+ m’bale wake. Yakobo mwana wa Zebedayo+ ndi m’bale wake Yohane.
3 Filipo ndi Batolomeyo,+ Tomasi+ ndi Mateyu+ wokhometsa msonkho, Yakobo mwana wa Alifeyo,+ Tadeyo,
4 Simoni Kananiya,*+ ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anapereka+ Yesu.
5 Yesu anatumiza atumwi 12 amenewa, ndipo anawapatsa malangizo awa:+ “Musapite mumsewu wa anthu a mitundu ina, ndipo musalowe mumzinda wa Asamariya.+
6 M’malomwake, nthawi zonse muzipita kwa nkhosa zosochera za nyumba ya Isiraeli.+
7 Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’+
8 Chiritsani odwala,+ ukitsani anthu akufa, yeretsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.+
9 Musatenge golide, siliva kapena mkuwa m’zikwama zanu za ndalama.+
10 Musatenge thumba la chakudya cha pa ulendo, kapena malaya awiri amkati, nsapato kapena ndodo, chifukwa wantchito ayenera kulandira chakudya chake.+
11 “Mukalowa mumzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenerera, ndipo mukhalebe momwemo kufikira nthawi yochoka.+
12 Pamene mukulowa m’nyumba, perekani moni kwa a m’banja limenelo.
13 Ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere umene mukuifunira ukhale panyumbayo,+ koma ngati si yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.
14 Kulikonse kumene munthu sakakulandirani kapena kumvetsera mawu anu, potuluka m’nyumba imeneyo kapena mumzinda umenewo sansani fumbi kumapazi anu.+
15 Ndithu ndikukuuzani, Chilango cha Sodomu+ ndi Gomora pa Tsiku la Chiweruzo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha mzinda umenewo.+
16 “Taonani! Ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu.+ Chotero khalani ochenjera ngati njoka+ koma oona mtima ngati nkhunda.+
17 Chenjerani ndi anthu,+ pakuti adzakuperekani kumakhoti aang’ono,+ ndipo adzakukwapulani+ m’masunagoge awo.+
18 Inde, adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu+ chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni+ kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina.
19 Koma akakuperekani kumeneko, musade nkhawa za mmene mukalankhulire kapena zimene mukanene. Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule,+
20 pakuti wolankhula simudzakhala inu panokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzera mwa inu.+
21 Komanso munthu adzapereka m’bale+ wake ku imfa, ndipo bambo adzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo awo ndipo adzawaphetsa.+
22 Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa,+ koma yekhayo amene adzapirire mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.+
23 Akakuzunzani mumzinda wina, muthawire mumzinda wina,+ pakuti ndithu ndikukuuzani, simudzamaliza kuzungulira+ mizinda yonse ya Isiraeli Mwana wa munthu asanafike.+
24 “Wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo kapolo saposa mbuye wake.+
25 Wophunzira amangofanana ndi mphunzitsi wake, ndipo kapolo amangofanana ndi mbuye wake.+ Ngati anthu atchula mwininyumba kuti Belezebule,*+ kuli bwanji ena a m’banja lakelo, kodi sadzawanena zoposa pamenepa?
26 Choncho musawaope, pakuti palibe chobisika chimene sichidzaululika, ndipo palibe chinsinsi chimene sichidzadziwika.+
27 Zimene ndimakuuzani mu mdima, muzinene poyera, ndipo zimene mumamva anthu akunong’onezana, muzilalikire pamadenga.+
28 Musachite mantha+ ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo, m’malomwake, muziopa iye+ amene angathe kuwononga zonse ziwiri, moyo ndi thupi lomwe m’Gehena.*+
29 Kodi mpheta ziwiri si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu?+ Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa.+
30 Ndipotu tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga.+
31 Choncho musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.+
32 “Chotero aliyense wovomereza pamaso pa anthu kuti ali kumbali yanga, inenso ndidzavomereza+ pamaso pa Atate wanga wakumwamba kuti ndili kumbali yake.
33 Koma aliyense wondikana ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamukana+ pamaso pa Atate wanga wakumwamba.
34 Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi, sindinabweretse mtendere+ koma lupanga.
35 Pakuti ndinabwera kudzagawanitsa anthu. Ndinabwera kudzachititsa munthu kutsutsana ndi bambo ake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake, ndiponso mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.+
36 Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.
37 Amene amakonda kwambiri bambo ake kapena mayi ake kuposa ine sali woyenera ine. Komanso amene amakonda kwambiri mwana wake wamwamuna kapena wamkazi kuposa ine sali woyenera ine.+
38 Ndiponso aliyense wosalandira mtengo wake wozunzikirapo* ndi kunditsatira sali woyenera ine.+
39 Aliyense wopulumutsa moyo wake adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.+
40 “Amene wakulandirani walandiranso ine, ndipo amene walandira ine walandiranso amene anandituma.+
41 Amene walandira mneneri chifukwa ndi mneneri adzalandira mphoto yofanana ndi imene mneneri amalandira,+ ndipo amene walandira munthu wolungama chifukwa ndi wolungama adzalandira mphoto yofanana ndi imene munthu wolungama amalandira.+
42 Aliyense wopatsa mmodzi wa tiana iti ngakhale madzi ozizira okha m’kapu kuti amwe chifukwa ndi wophunzira, ndithu ndikukuuzani, ameneyo mphoto yake sidzatayika ngakhale pang’ono.”+
Mawu a M'munsi
^ “Petulo” amatchedwa ndi mayina asanu. Pano akutchedwa “Simoni, wotchedwa Petulo.” Pa Mt 16:16 akutchedwa “Simoni Petulo,” pa Mac 15:14, “Sumeoni,” ndipo pa Yoh 1:42, “Kefa.” Koma nthawi zambiri amatchedwa “Petulo,” monga mmene zilili pa Mt 14:28.
^ Dzina lakuti “Kananiya” likutanthauza munthu wachangu.
^ “Belezebule” ndi dzina lina la Satana.
^ Onani Zakumapeto 6.
^ Onani Zakumapeto 9.