Zefaniya 3:1-20

  • Yerusalemu, mzinda wogalukira ndiponso wachinyengo (1-7)

  • Kuweruza ndiponso kubwezeretsa (8-20)

    • Kusintha nʼkuyamba kulankhula chilankhulo choyera (9)

    • Anthu odzichepetsa komanso ooneka onyozeka adzapulumutsidwa (12)

    • Yehova adzakondwera ndi Ziyoni (17)

3  Tsoka kwa mzinda wogalukira, woipitsidwa komanso wopondereza anthu ake.+  2  Mzindawo sunamvere+ ndipo sunalole kulangizidwa,+ Sunakhulupirire Yehova+ komanso sunayandikire Mulungu wake.+  3  Akalonga ake ali ngati mikango yobangula.+ Oweruza ake ali ngati mimbulu imene ikuyenda usiku.Imene pofika mʼmawa imadya chilichonse osasiya ngakhale fupa.  4  Aneneri ake ndi amwano ndiponso achinyengo.+ Ansembe ake amaipitsa zinthu zopatulika,+Ndipo amaphwanya malamulo.+  5  Yehova ndi wolungama mumzindawo+ ndipo salakwitsa. Mʼmawa uliwonse iye amadziwitsa anthu chilungamo chake,+Moti mofanana ndi kuwala, chilungamocho sichisowa. Koma wosalungama sachita manyazi.+  6  “Ine ndinawononga mitundu ya anthu ndi kusakaza nsanja zawo zamʼmakona. Ndinawononga misewu yawo moti simunkayendanso anthu. Mizinda yawo inakhala mabwinja ndipo simunatsale munthu aliyense.+  7  Ndiyeno ndinati, ‘Mosakayikira udzandiopa ndipo udzalola kulangizidwa,’+ Kuti iye* asawonongedwe.+Ndidzamuimba mlandu wa zonsezi.* Koma mʼpamene ankafunitsitsa kwambiri kuchita zoipa.+  8  Yehova wanena kuti: ‘Choncho pitirizani kundiyembekezera,*+Mpaka tsiku limene ndidzanyamuke kuti ndikatenge zinthu za anthu omwe ndawagonjetsa.*Chiweruzo changa ndi choti ndisonkhanitse mitundu ya anthu, ndisonkhanitse maufumu,Kuti ndiwasonyeze mkwiyo wanga, ndithu mkwiyo wanga wonse woyaka moto,+Chifukwa moto wa mkwiyo wanga udzawotcheratu dziko lonse lapansi.+  9  Pa nthawiyo ndidzasintha chilankhulo cha anthu kuti chikhale chilankhulo choyera,Kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova,Nʼkumamutumikira mogwirizana.’*+ 10  Kuchokera kuchigawo cha mitsinje ya ku Itiyopiya,Anthu amene akundichonderera, anthu anga obalalitsidwa, adzandibweretsera mphatso.+ 11  Pa tsiku limenelo, sudzachita manyaziChifukwa cha zinthu zonse zimene unachita pondigalukira,+Popeza ndidzachotsa anthu odzikweza pakati panu.Ndipo sudzakhalanso wodzikweza mʼphiri langa lopatulika.+ 12  Ndidzasiya anthu odzichepetsa ndi ofatsa kuti akhalebe pakati panu,+Ndipo iwo adzapeza chitetezo mʼdzina la Yehova. 13  Aisiraeli otsala+ sadzachita zinthu zosalungama.+Sadzalankhula bodza kapena kukhala ndi lilime lachinyengo.Iwo adzadya ndi kugona ndipo sipadzakhala wowaopseza.”+ 14  Fuula mosangalala, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni!* Fuula chifukwa chopambana, iwe Isiraeli!+ Sangalala ndiponso kondwera ndi mtima wonse, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!*+ 15  Yehova wakuchotsera ziweruzo zake.+ Wabweza mdani wako.+ Yehova, Mfumu ya Isiraeli, ali pakati panu.+ Ndipo sudzaopanso kuti tsoka likugwera.+ 16  Tsiku limenelo Yerusalemu adzauzidwa kuti: “Usaope iwe Ziyoni,+ Ndipo manja ako asafooke. 17  Yehova Mulungu wako ali pakati panu+ Ndipo adzakupulumutsa chifukwa ndi wamphamvu. Iye adzakondwera nawe.+ Adzakhala phee chifukwa chokhutira ndi chikondi chimene akukusonyeza, Ndipo adzafuula mosangalala chifukwa chokondwera nawe. 18  Ndidzasonkhanitsa anthu amene akumva chisoni chifukwa chosapezeka pazikondwerero zako.+Iwo sanali ndi iwe chifukwa anali ku ukapolo kumene ankanyozedwa.+ 19  Pa nthawiyo ndidzalanga onse amene akukupondereza,+Ndipo ndidzapulumutsa wotsimphina.+Ndidzasonkhanitsa anthu amene anabalalitsidwa.+ Ndidzachititsa kuti akhale otchuka* komanso azitamandidwa,Mʼdziko lonse limene anachititsidwa manyazi. 20  Pa nthawiyo ndidzakubweretsani,Ndidzachita zimenezi pa nthawi imene ndidzakusonkhanitseni. Ndikadzabwezeretsa iwe ukuona, anthu a mtundu wako amene anatengedwa kupita ku ukapolo,+Ndidzachititsa kuti ukhale wotchuka* komanso uzitamandidwa,+ pakati pa anthu a mitundu yonse yapadziko lapansi,” watero Yehova.

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “Ndidzamulanga chifukwa cha zonsezi.”
^ Kutanthauza Yerusalemu.
^ Kapena kuti, “kundidikirira moleza mtima.”
^ Mabaibulo ena amati, “ndidzanyamuke ngati mboni.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “phewa ndi phewa.”
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzina.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzina.”