Oweruza 5:1-31

  • Nyimbo imene Debora ndi Baraki anaimba atapambana (1-31)

    • Nyenyezi zinamenya nkhondo yolimbana ndi Sisera (20)

    • Mtsinje wa Kisoni unasefukira (21)

    • Okonda Yehova ali ngati dzuwa (31)

5  Tsiku limenelo, Debora+ limodzi ndi Baraki+ mwana wa Abinowamu, anaimba nyimbo iyi:+   “Posiya tsitsi lalitali lili losamanga mu Isiraeli monga lumbiro la nkhondo,Chifukwa cha kudzipereka kwa anthu,+Tamandani Yehova.   Mvetserani mafumu inu. Inu olamulira, tcherani khutu. Ine ndidzaimbira Yehova. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli.+   Yehova, pamene munayenda kuchokera ku Seiri,+Pamene munaguba kuchokera kudera la Edomu,Dziko linagwedezeka ndipo kumwamba kunagwetsa madzi,Mitambo inagwetsa madzi.   Mapiri anasungunuka* pamaso pa Yehova,+Ngakhalenso Sinai anasungunuka pamaso pa Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli.+   Mʼmasiku a Samagara+ mwana wa Anati,Mʼmasiku a Yaeli,+ mʼnjira munalibe odutsamo,Ndipo anthu oyenda ankadutsa njira zolambalala.   Anthu okhala mʼmidzi ya Isiraeli anachoka,Anachoka mpaka pamene ine Debora+ ndinafika,Mpaka pamene ine ndinakhala ngati mayi mu Isiraeli.+   Anasankha milungu yatsopano;+Atatero nkhondo inafika mʼmizinda.+ Panalibe chishango kapena mkondo waungʼono,Pakati pa anthu 40,000 mu Isiraeli.   Mtima wanga uli pa atsogoleri a asilikali a Isiraeli,+Amene anadzipereka kuti apite ndi anthu.+ Tamandani Yehova. 10  Inu okwera abulu ofiirira,Inu okhala pamakapeti abwino* kwambiri,Komanso inu oyenda mumsewu,Ganizirani izi: 11  Mawu a anthu otunga madzi anamveka pamalo otungira madzi;Kumeneko ankafotokoza ntchito zolungama za Yehova,Ankafotokoza ntchito zolungama za anthu ake okhala mʼmidzi ya Isiraeli. Kenako anthu a Yehova anapita kumizinda. 12  Dzuka, dzuka Debora iwe!+ Dzuka, dzuka imba nyimbo!+ Imirira Baraki iwe!+ Tsogolera anthu amene wawagwira, iwe mwana wa Abinowamu. 13  Kenako opulumuka anapita kwa anthu olemekezeka.Anthu a Yehova anabwera kwa ine, pokalimbana ndi anthu amphamvu. 14  Amene anali mʼchigwa anachokera mʼfuko la Efuraimu,Akukutsatira iwe Benjamini, pakati pa anthu a mtundu wako. Atsogoleri a asilikali anachokera kwa Makiri,+Ndipo osunga zida za mlembi, anachokera mʼfuko la Zebuloni. 15  Akalonga a fuko la Isakara anali ndi Debora,Mmene anachitira Isakara, ndi mmenenso anachitira Baraki.+ Anamutumiza kuchigwa akuyenda wapansi.+ Pakati pa magulu a fuko la Rubeni, panali kufufuza mozama za mumtima. 16  Unakhaliranji pansi pakati pa zikwama ziwiri za katundu,Nʼkumamvetsera nyimbo za zitoliro zoimbira nkhosa?+ Popeza pa magulu a fuko la Rubeni panali kufufuza mozama za mumtima. 17  Anthu a ku Giliyadi anangokhala kutsidya lina la Yorodano.+Ndipo nʼchifukwa chiyani Dani anangokhala mʼsitima?*+ Aseri anangokhala phee mʼmbali mwa nyanja,Osachoka pamadoko ake.+ 18  Anthu a fuko la Zebuloni anaika moyo wawo pangozi.Anthu a mʼfuko la Nafitali anachitanso zomwezo+ mʼmapiri.+ 19  Mafumu anabwera ndi kumenya nkhondo.Kenako mafumu a Kanani anamenya nkhondo;+Anamenya nkhondo ku Taanaki, pafupi ndi madzi a ku Megido.+ Iwo sanapezepo siliva woti atenge.+ 20  Nyenyezi zinamenya nkhondo zili kumwamba;Zinamenyana ndi Sisera zili mʼnjira zawo. 21  Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,+Mtsinje wakalekale, mtsinje wa Kisoni. Moyo wanga iwe, unapondereza adani amphamvu. 22  Kenako mapazi a mahatchi* anamvekaPamene ankathamanga atakwiya.+ 23  Mngelo wa Yehova anati: ‘Tembererani Merozi,Tembererani anthu ake,Chifukwa sanathandize Yehova,Sanabwere ndi anthu amphamvu kudzathandiza Yehova.’ 24  Mkazi wodalitsika kwambiri ndi Yaeli+Mkazi wa Hiberi Mkeni;+Ndi wodalitsika kwambiri pakati pa akazi onse okhala mʼmatenti. 25  Sisera anapempha madzi, Yaeli anamʼpatsa mkaka. Anamupatsa mkaka, mʼmbale yolowa yabwino kwambiri.+ 26  Kenako anatenga chikhomo cha tenti.Ndi dzanja lake lamanja anatenga hamala yolemera. Atatero anakhoma Sisera nʼkuphwanya mutu,Anaphwanya ndi kuboola fupa lapafupi ndi khutu.+ 27  Sisera anagwa nʼkugona pakati pa mapazi a Yaeli;Pakati pa mapazi ake, iye anagwa nʼkugona;Pamene anagwerapo, anagona pomwepo atagonja. 28  Munthu wamkazi anayangʼana pawindo,Amayi a Sisera anayangʼana pawindo ndipo anati,‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lankhondo likuchedwa kubwera? Nʼchifukwa chiyani mapazi a mahatchi a magaleta ake akuchedwa kumveka?’+ 29  Akazi anzeru pakati pa azimayi ake olemekezeka ankamuyankha;Iyenso ankadziyankha mumtima kuti, 30  ‘Ayenera kuti akugawa zinthu zimene apeza,Akugawa mtsikana mmodzi, kapena atsikana awiri kwa msilikali aliyense,Nsalu zokongola za Sisera, ndithu nsalu zokongola,Chovala chopeta chokongola, inde, zovala ziwiri zopeta,Zoti amuna omwe alanda zinthu avale mʼmakosi awo.’ 31  Inu Yehova, adani anu onse afafanizidwe,+Koma amene amakukondani awale ngati mmene dzuwa limawalira likamatuluka.” Ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 40.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “anagwedezeka.”
Kapena kuti, “pansalu zoyala pansi zabwino.”
Kapena kuti, “mʼzombo.”
Ena amati “mahosi.”