Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Makhalidwe Okuthandizani Kupanga Ophunzira

Makhalidwe Okuthandizani Kupanga Ophunzira

Makhalidwe Okuthandizani Kupanga Ophunzira

“Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.”​—MATEYO 28:19.

1. Kodi atumiki ena a Mulungu m’mbuyomu anafunika kukhala ndi luso komanso makhalidwe ati?

NTHAWI zina atumiki a Yehova amafunika kukhala ndi luso komanso makhalidwe amene angawathandize kuchita chifuniro chake. Atauzidwa ndi Mulungu, Abulahamu ndi Sara anasamuka mu mzinda wotukuka wa Uri. Kuti achite zimenezi, anafunika kukhala ndi luso komanso makhalidwe a anthu okhala m’mahema. (Aheberi 11:8, 9, 15) Kuti atsogolere Aisiraeli polowa m’Dziko Lolonjezedwa, Yoswa anafunika kulimba mtima, kudalira Yehova komanso kudziwa Chilamulo Chake. (Yoswa 1:7-9) N’kutheka kuti Bezaleli ndi Aholiabu anali anthu aluso, komabe mzimu wa Mulungu unawathandiza kupititsa patsogolo luso lawolo n’cholinga choti iwo ayang’anire ndi kugwira ntchito yokonza chihema.​—Eksodo 31:1-11.

2. Kodi tikambirana mafunso ati okhudza ntchito yopanga ophunzira?

2 Patapita zaka zambiri Yesu Khristu anapatsa otsatira ake ntchito. Iye anati: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse. . . . Kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyo 28:19, 20) Palibenso anthu ena amene anapatsidwa mwayi wogwira ntchito yaikulu ngati imeneyi. Kodi ndi makhalidwe ati amene angafunike kuti munthu agwire bwino ntchito yopanga ophunzira? Kodi tingatani kuti tikhale ndi makhalidwe amenewa?

Kondani Mulungu ndi Mtima Wonse

3. Kodi lamulo loti tipange ophunzira limatipatsa mwayi wotani?

3 Pamafunika kukonda Yehova ndi mtima wonse kuti tilankhule ndi anthu n’cholinga choti ayambe kulambira Mulungu woona. Aisiraeli ankasonyeza kukonda Mulungu ndi mtima wonse mwa kumvera malamulo ake, kupereka nsembe zovomerezeka, komanso kum’tamanda poimba nyimbo. (Deuteronomo 10:12, 13; 30:19, 20; Salmo 21:13; 96:1, 2; 138:5) Popeza timapanga ophunzira, nafenso timasunga malamulo a Mulungu, komanso timasonyeza kuti timakonda Yehova mwa kuuza ena za iye ndiponso zolinga zake. Tiyenera kulankhula motsimikiza ndiponso kusankha bwino mawu ofotokoza mmene tikumvera chifukwa cha chiyembekezo chimene Mulungu watipatsa.​—1 Atesalonika 1:5; 1 Petulo 3:15.

4. N’chifukwa chiyani Yesu ankasangalala kuuza anthu za Yehova?

4 Chifukwa chokonda Yehova ndi mtima wonse, Yesu ankasangalala kuuza ena zolinga za Mulungu, Ufumu wa Mulungu, ndiponso kulambira koona. (Luka 8:1; Yohane 4:23, 24, 31) Ndipotu Yesu ananena kuti: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha iye amene anandituma ine ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Wamasalmo ananena za Yesu kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m’kati mwamtima mwanga. Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu; onani, sindidzaletsa milomo yanga, mudziwa ndinu Yehova.”​—Salmo 40:8, 9; Aheberi 10:7-10.

5, 6. Tchulani khalidwe lalikulu limene anthu opanga ophunzira ayenera kukhala nalo.

5 Chifukwa chokonda Mulungu, anthu amene angophunzira kumene choonadi cha m’Baibulo nthawi zina amauza ena za Yehova ndi Ufumu wake. Iwo amachita zimenezi motsimikiza mtima, moti ena amakopeka n’kuyambanso kuphunzira Malemba. (Yohane 1:41) Kukonda Mulungu ndi khalidwe lalikulu limene limatilimbikitsa kugwira nawo ntchito yopanga ophunzira. Kuti chikondi chimenechi chisazirale tiyenera kuphunzira ndi kusinkhasinkha Mawu ake nthawi zonse.​—1 Timoteyo 4:6, 15; Chivumbulutso 2:4.

6 Mosakayikira, kukonda Yehova n’kumene kunathandiza Yesu Khristu kukhala mphunzitsi wachangu. Komatu si zokhazi zimene zinamuthandiza kukhala wogwira mtima polalikira za Ufumu. Kodi ndi khalidwe lina liti limene linathandiza Yesu kugwira bwino ntchito yopanga ophunzira?

Sonyezani Kuti Mumakonda Anthu

7, 8. Kodi Yesu ankawaona bwanji anthu?

7 Yesu ankakonda anthu ndipo ankachita nawo chidwi. Ngakhale pamene anali “mmisiri” wamkulu wa Mulungu, asanabwere pa dziko lapansi, iye ankakonda anthu. (Miyambo 8:30, 31) Atabwera pa dziko lapansi, Yesu ankakomera mtima anthu ndipo ankatsitsimutsa anthu obwera kwa iye. (Mateyo 11:28-30) Yesu ankasonyeza chikondi ndi kukoma mtima kwa Yehova ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu ayambe kulambira Mulungu woona. Anthu osiyanasiyana ankamvetsera zonena za Yesu chifukwa choti iye ankawaganizira.​—Luka 7:36-50; 18:15-17; 19:1-10.

8 Mwamuna wina atamufunsa zoyenera kuchita kuti akapeze moyo wosatha, “Yesu anamuyang’ana ndipo anam’konda.” (Maliko 10:17-21) Ponena za anthu amene anaphunzitsidwa ndi Yesu ku Betaniya, Baibulo limati: “Yesu anali kuwakonda, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.” (Yohane 11:1, 5) Yesu ankakonda kwambiri anthu moti panthawi ina analephera kupuma n’cholinga choti awaphunzitse. (Maliko 6:30-34) Chifukwa choti Yesu ankakonda kwambiri anthu, palibenso munthu wina amene angafanane naye pankhani yokhala wogwira mtima pothandiza anthu kuti ayambe kulambira koona.

9. Kodi Paulo anali ndi khalidwe lotani pamene ankapanga ophunzira?

9 Nayenso mtumwi Paulo ankakonda kwambiri anthu amene ankawalalikira. Mwachitsanzo, polankhula ndi anthu amene anakhala Akhristu ku Tesalonika iye anati: “Pokhala ndi chikondi chachikulu kwa inu, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo ya ife eni, chifukwa munakhala okondedwa kwa ife.” Chifukwa cha chikondi chimene Paulo anasonyeza, anthu ena ku Tesalonika ‘anasiya mafano awo kuti atumikire Mulungu wamoyo.’ (1 Atesalonika 1:9; 2:8) Ngati tisonyeza chikondi chenicheni kwa anthu monga mmene Yesu ndi Paulo anachitira, ifenso tingakhale ndi mwayi woona uthenga wabwino ukuwafika pa mtima anthu a “maganizo oyenerera moyo wosatha.”​—Machitidwe 13:48.

Khalani ndi Mtima Wodzipereka

10, 11. N’chifukwa chiyani mtima wodzipereka uli wofunika pamene tikupanga ophunzira?

10 Anthu odzipereka amakhala ogwira mtima popanga ophunzira. Cholinga chawo pamoyo sichikhala kupeza chuma. Pankhani imeneyi Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Zidzakhalatu zovuta zedi kuti anthu a ndalama adzalowe mu ufumu wa Mulungu!” Ophunzirawo anadabwa nawo mawu akewo, koma Yesu anapitiriza kuti: “Ana inu, kulowa mu ufumu wa Mulungu n’kovuta kwabasi! N’chapafupi kuti ngamila ilowe pa diso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.” (Maliko 10:23-25) Yesu anafuna kuti otsatira ake azikhala moyo wosalira zambiri kuti agwire bwino ntchito yopanga ophunzira. (Mateyo 6:22-24, 33) N’chifukwa chiyani mtima wodzipereka umatithandiza popanga ophunzira?

11 Pamafunika kuchita khama kwambiri kuti tiphunzitse anthu zinthu zimene Yesu anatilamulira. Nthawi zambiri, munthu wopanga ophunzira amayesetsa kuti aziphunzira Baibulo ndi munthu wachidwi mlungu uliwonse. Pofuna kuti asavutike kwambiri kupeza anthu achidwi, olengeza Ufumu ena asiya ntchito n’kumagwira maganyu. Akhristu ambiri aphunzira chinenero china n’cholinga choti azilalikira kwa anthu amitundu ina m’dera lawo. Enanso asiya nyumba zawo n’kusamukira ku dera kapena dziko lina n’cholinga chokagwira mokwanira ntchito yokolola. (Mateyo 9:37, 38) Zonsezi zimafuna kuti munthu akhale ndi mtima wodzipereka. Komatu, kuti munthu akhale wogwira mtima popanga ophunzira pamafunikanso zinthu zina.

Khalani Woleza Mtima Koma Wosawononga Nthawi

12, 13. N’chifukwa chiyani kuleza mtima kuli kofunika pamene tikupanga ophunzira?

12 Khalidwe linanso limene lingatithandize popanga ophunzira ndi kuleza mtima. Uthenga umene Akhristufe timalalikira ndi wofunika changu, koma timafunika kuleza mtima chifukwa zimatenga nthawi kuti munthu akhale wophunzira. (1 Akorinto 7:29) Yesu analeza mtima ndi m’bale wake Yakobe. Ngakhale kuti Yakobe ankadziwa bwino zimene Yesu ankalalikira, zinam’tengera nthawi ndithu kuti akhale wophunzira. (Yohane 7:5) Panangodutsa kanthawi kochepa kuchokera pamene Yesu anafa kufika pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Koma zikuoneka kuti Yakobe anakhala wophunzira m’kanthawi kameneka, chifukwa Malemba amasonyeza kuti anali nawo pamapemphero pamodzi ndi mayi ake, abale ake, komanso atumwi. (Machitidwe 1:13, 14) Kenako, Yakobe anapita patsogolo kwambiri mwauzimu moti anadzakhala ndi udindo waukulu mumpingo wachikhristu.​—Machitidwe 15:13; 1 Akorinto 15:7.

13 Akhristu ali ngati alimi amene akulima mbewu zochedwa kukula. Zimatenga nthawi kuti munthu amvetse Mawu a Mulungu, akonde Yehova, komanso kuti akhale ndi maganizo a Khristu. Choncho, kuleza mtima n’kofunika. Yakobe analemba kuti: “Lezani mtima abale, kufikira kukhalapo kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Iye amayembekezerabe zipatso zofunika kwambiri za m’nthaka. Amakhala wodekha mpaka itagwa mvula yoyamba ndi mvula yomaliza. Nanunso khalani oleza mtima; limbitsani mitima yanu, chifukwa kukhalapo kwa Ambuye kwayandikira.” (Yakobe 5:7, 8) Yakobe analimbikitsa okhulupirira anzake kuti akhale oleza mtima ‘kufikira kukhalapo kwa Ambuye.’ Ngati ophunzira sanamvetse mfundo inayake, Yesu ankawafotokozera kapena kuwauza fanizo lokhudza mfundoyo, ndipo ankatero moleza mtima. (Mateyo 13:10-23; Luka 19:11; 21:7; Machitidwe 1:6-8) Ino ndi nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye, choncho kuleza mtima n’kofunika kwambiri pamene tikupanga ophunzira. Anthu amene akuyamba kutsatira Yesu masiku ano afunika kuphunzitsidwa moleza mtima.​—Yohane 14:9.

14. Ngakhale kuti timaleza mtima popanga ophunzira, kodi tingatani kuti tigwiritse ntchito bwino nthawi yathu?

14 Ngakhale kuti timaleza mtima, anthu ambiri salabadira uthenga wa m’Baibulo umene timawaphunzitsa. (Mateyo 13:18-23) Ngati titayesa kuphunzira ndi munthu kwanthawi yaitali koma munthuyo osalabadira, timam’siya kaye n’kukafufuza ena amene angalabadire choonadi cha m’Baibulo. (Mlaliki 3:1, 6) Ngakhale munthu amene amayamikira choonadi amafunika kumuthandiza kuti asinthe maganizo, mtima ndiponso zolinga zake pamoyo. Mofanana ndi Yesu, timaleza mtima ndi ophunzira amene akuchedwa kukhala ndi maganizo oyenera.​—Maliko 9:33-37; 10:35-45.

Kulitsani Luso la Kuphunzitsa

15, 16. N’chifukwa chiyani tifunika kulankhula zomveka komanso kukonzekera bwino pamene tikupanga ophunzira?

15 Makhalidwe ofunika kwambiri popanga ophunzira ndi kukonda Mulungu ndi anthu, mtima wodzipereka, ndiponso kuleza mtima. M’pofunikanso kukulitsa luso lathu la kuphunzitsa kuti tizitha kuphunzitsa anthu mosavuta komanso momveka. Mwachitsanzo, mfundo zimene Mphunzitsi Waluso, Yesu Khristu, ankaphunzitsa zinali zamphamvu chifukwa chakuti zinali zosavuta kumva. Mwina mungakumbukire mfundo zimene Yesu anaphunzitsa monga zakuti: “Kundikani chuma chanu kumwamba.” “Musamapatse agalu zinthu zopatulika.” “Nzeru imatsimikizirika kukhala yolungama mwa ntchito zake.” “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.” (Mateyo 6:20; 7:6; 11:19; 22:21) Komabe, sikuti Yesu ankangonena mawu achidule. Iye ankaphunzitsa momveka bwino ndipo ankafotokoza mfundo zina ngati panafunika kuti atero. Kodi tingatsatire bwanji kaphunzitsidwe ka Yesu?

16 Kukonzekera bwino n’kofunika kwambiri kuti tithe kuphunzitsa zinthu m’njira yosavuta kumva. Ngati munthu wopanga ophunzira sanakonzekere, amalankhula zinthu zambirimbiri. Angasokoneze mfundo zazikulu chifukwa chongolankhula mwachisawawa mfundo zonse zomwe akudziwa pankhaniyo. Koma mtumiki amene wakonzekera bwino amaganizira za munthu yemwe akumuphunzitsayo, amasinkhasinkha nkhaniyo ndipo amafotokoza momveka bwino mfundo zofunika zokha basi. (Miyambo 15:28; 1 Akorinto 2:1, 2) Amaganiziranso zimene wophunzirayo akudziwa kale pankhaniyo, n’kuona mfundo zofunika kutsindika pa phunzirolo. Iye angakhale ndi mfundo zambiri zokhudza nkhaniyo, koma kuti anene zinthu momveka bwino ayenera kuchotsa mfundo zosafunika kwenikweni.

17. Kodi tingathandize bwanji anthu kuganizira bwino Malemba?

17 M’malo mongowauza anthu mfundo, Yesu ankawathandiza kuganiza. Mwachitsanzo, tsiku lina iye anafunsa kuti: “Simoni ukuganiza bwanji? Kodi mafumu a dziko lapansi amalandira ndalama za ziphaso kapena za msonkho kuchokera kwa ndani? Kuchokera kwa ana awo kapena kwa anthu achilendo?” (Mateyo 17:25) Kufotokoza mfundo za m’Baibulo kumakhala kosangalatsa kwambiri. Choncho, tiyenera kudziletsa kuti nayenso wophunzirayo azilankhula maganizo ake pankhani yomwe tikuphunzira naye. Ndi bwinonso kuti tisamapanikize munthu ndi mafunso. Koma tizipereka mafanizo ndiponso kufunsa mafunso mwanzeru kuti wophunzirayo amvetse mfundo za m’Malemba zimene tikukambirana naye m’mabuku ofotokoza Baibulo.

18. Kodi munthu amene ali ndi “luso la kuphunzitsa” amachita zotani?

18 Malemba amanena za “luso la kuphunzitsa.” (2 Timoteyo 4:2; Tito 1:9) M’malo mongothandiza munthu wophunzira Baibulo kuloweza mfundo zinazake, munthu wophunzitsa mwaluso amathandiza wophunzirayo kusiyanitsa pakati pa zinthu zoona ndi zabodza, zoyenera ndi zolakwika, komanso pakati pa nzeru ndi kupusa. Ngati tichita zimenezi n’cholinga choti munthu azikonda Yehova ndi mtima wake wonse, munthuyo angaone ubwino wa kumvera Yehova.

Khalani Wakhama Pantchito Yopanga Ophunzira

19. Kodi Akhristu onse amathandiza bwanji popanga ophunzira?

19 Mpingo wachikhristu ndi gulu lopanga ophunzira. Munthu watsopano akakhala wophunzira, Akhristu onse amasangalala osati munthu amene anam’phunzitsa yekhayo ayi. Mwachitsanzo, anthu akamafufuza mwana amene wasowa, munthu mmodzi ndi amene angapeze mwanayo. Mwanayo akapezeka n’kumupereka kwa makolo ake, anthu onse amene anali kumufufuza aja amasangalala. (Luka 15:6, 7) Zimenezi n’zofanana ndi ntchito yopanga ophunzira. Akhristu onse ali pakalikiliki kufufuza anthu amene angakhale ophunzira a Yesu. Ndipo munthu watsopano akayamba kubwera ku misonkhano pa Nyumba ya Ufumu, Akhristu onse amamuthandiza kuti aziyamikira kulambira koona. (1 Akorinto 14:24, 25) Motero, Akhristu onse amasangalala kuti chaka chilichonse anthu atsopano ambirimbiri akukhala ophunzira.

20. Kodi muyenera kutani ngati mukufuna kuphunzitsa ena choonadi cha m’Baibulo?

20 Akhristu okhulupirika ambiri angakonde kuphunzitsa munthu kuti adziwe Yehova ndiponso kulambira koona. Koma nthawi zina zimenezi sizichitika, ngakhale kuti Akhristuwo akuyesetsa kwambiri. Ngati zili choncho ndi inu, pitirizani kukulitsa chikondi chanu kwa Yehova, kondani anthu, khalani ndi mtima wodzipereka, lezani mtima, ndipo kulitsani luso lanu la kuphunzitsa. Koposa zonse, muzitchula m’pemphero kuti mukufunitsitsa kuphunzitsa anthu. (Mlaliki 11:1) Khazikani mtima pansi podziwa kuti zilizonse zimene mukuchita potumikira Yehova, zimathandiza kwambiri pantchito yopanga ophunzira imene imalemekeza Mulungu.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani ntchito yopanga ophunzira imasonyeza kuti timakonda Mulungu?

• Kodi anthu opanga ophunzira afunika kukhala ndi makhalidwe ati?

• Kodi munthu amene ali ndi “luso la kuphunzitsa” amachita zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Akhristu amasonyeza kuti amakonda Mulungu ndi mtima wonse mwa kupanga ophunzira

[Chithunzi patsamba 23]

N’chifukwa chiyani anthu opanga ophunzira ayenera kukonda ena?

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi anthu opanga ophunzira afunika kukhala ndi makhalidwe ena ati?

[Chithunzi patsamba 25]

Akhristu onse amasangalala ndi zotsatira za ntchito yopanga ophunzira