Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Cholinga Chanu Pamoyo N’chiyani?

Kodi Cholinga Chanu Pamoyo N’chiyani?

Kodi Cholinga Chanu Pamoyo N’chiyani?

KENNY ankagwira ntchito yapamwamba pakampani ina, ankayendera galimoto yapamwamba, ndiponso ankakhala m’nyumba yosanja m’dera la anthu olemera kwambiri mumzinda wina waukulu. Iye analinso katswiri wa masewera odumpha m’ndege ikuuluka, ndipo ankasangalala akamachita zimenezi. Koma kodi zimenezi zinam’pangitsa kuona moyo wake kukhala waphindu? M’magazini ina, iye anati: “Tsopano ndili ndi zaka 45, koma ndilibe tsogolo lililonse . . . Sindikuona phindu lililonse la moyo.”​—The Wall Street Journal.

Elyn anayesetsa kuti akhale katswiri wa masewera otsetsereka pamadzi oundana. Izi zinathekadi ndipo anakhala wotchuka kwambiri. Komabe anadandaula kuti: “Poyamba ndinkaganiza kuti ndidzakhala wosangalala kwambiri. Koma pano ndimasungulumwa kwambiri. Ngakhale kuti ndinali ndi ndalama zambiri ndinkadziwa kuti ndidzakalamba. Ndipo moyo wanga ukanakhala wopanda phindu ngati cholinga changa chikanangokhala kutchuka basi.”

Hideo anali katswiri wa zojambulajambula. Iye sankagulitsa zithunzi zake, ati poopa kuti angalowetse pansi luso lake. Hideo anamwalira ali ndi zaka 98 ndipo chakumapeto kwa moyo wake anapereka zambiri mwa zinthu zimene anajambula kuti zisungidwe ku nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi. Pamoyo wake wonse Hideo ankangochita zojambulajambula basi. Koma iye sanali wosangalala chifukwa ankaganiza kuti n’zosatheka kuti akhale katswiri weniweni wa zojambulajambula.

Anthu ena amayesetsa kwambiri kuthandiza anzawo. Taonani chitsanzo ichi cha bambo wina amene anali bwana wamkulu pakampani ina yopanga mafilimu ku Hollywood. Iye anali wachiwiri kwa pulezidenti wa bungwe lina la makampani opanga mafilimu ku United States. Chifukwa cha zimenezi iye ankacheza ndi anthu otchuka kwambiri ndipo ankakhala ku dera la anthu olemera kwambiri. Atapita kukacheza m’dziko la Cambodia, mtsikana wina anabwera kudzam’pempha ndalama m’chipinda china chodyera mumzinda wa Phnom Penh. Iye anamupatsa ndalama zokwana dola imodzi ndi botolo la zakumwa. Mtsikanayo anayamikira kwambiri. Koma usiku wotsatira mtsikanayo anabweranso kudzapempha. Apa bwanayu anaona kuti kungom’patsa zinthu zimene akufuna panthawiyo kunali kosakwanira.

Patatha chaka chimodzi bwanayu anaganiza zosintha ntchito. Anasiya ntchito yake ija n’kukayamba kuthandiza anthu ovutika ku Cambodia. Iye anatsegula sukulu imenenso inkapereka chakudya ndiponso malo ogona. Komabe, ngakhale kuti nthawi zina amasangalala ndi zinthu zimene akuchita, iye amavutikanso maganizo chifukwa mavuto oti athane nawo akuwonjezeka.

Anthu anayi amene tatchulawa ankaganiza kuti akudziwa cholinga chawo pamoyo. Koma akakwanitsa kuchita zimene ankaona kuti ndiye cholinga cha moyo wawo, iwo ankaona kuti sizikupangitsa moyo kukhala waphindu. Kodi inuyo muli ndi cholinga chotani pamoyo wanu? Kodi chinthu chofunika kwambiri pamoyo wanu n’chiyani? Kodi mukutsimikiza kuti simudzanong’oneza bondo ndi zimene mukuchita pa moyo wanu?