Luka 2:1-52

2  Tsopano m’masiku amenewo, Kaisara Augusito analamula+ kuti anthu onse m’dzikolo akalembetse m’kaundula.  Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya.  Anthu onse anapita kukalembetsa,+ aliyense kumzinda wakwawo.  Yosefe nayenso anachoka ku Galileya, mumzinda wa Nazareti, n’kupita ku Yudeya, kumzinda wa Davide wotchedwa Betelehemu,+ chifukwa anali wa m’banja ndi m’fuko la Davide.+  Anapita kukalembetsa limodzi ndi Mariya,+ amene anamanga naye banja malinga ndi pangano.+ Pa nthawiyi n’kuti Mariya tsopano ali wotopa ndi pakati.+  Ali kumeneko, masiku oti achire anakwana.  Ndipo anabereka mwana wake woyamba wamwamuna.+ Anamukulunga ndi nsalu n’kumugoneka modyeramo ziweto,+ chifukwa anasowa malo m’nyumba ya alendo.  M’dzikomo munalinso abusa amene anali kugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse mosinthana maulonda.  Mwadzidzidzi mngelo wa Yehova+ anaima chapafupi ndi iwo, ndipo ulemerero wa Yehova+ unawawalira ponsepo, mwakuti anachita mantha kwambiri. 10  Koma mngeloyo anawauza kuti: “Musaope! Ine ndabwera kudzalengeza kwa inu uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu chimene anthu onse adzakhala nacho.+ 11  Chifukwa lero wakubadwirani Mpulumutsi,+ amene ndi Khristu Ambuye,+ mumzinda wa Davide.+ 12  Ndikukupatsani chizindikiro ichi: Mukapeza mwana wakhanda wokutidwa m’nsalu, atagona modyeramo ziweto.” 13  Mwadzidzidzi, panaoneka khamu lalikulu lakumwamba+ pamodzi ndi mngeloyo, likutamanda Mulungu+ kuti: 14  “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba,+ ndipo pansi pano mtendere+ pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.”+ 15  Choncho angelowo atawachokera kubwerera kumwamba, abusawo anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tipite ndithu ku Betelehemu tikaone zimene zachitikazo, zimene Yehova+ watidziwitsa.” 16  Pamenepo anapita mwachangu ndipo anakapeza Mariya ndi Yosefe, komanso mwana wakhandayo atagona modyeramo ziweto. 17  Ataona khandalo, anafotokoza zimene anauzidwa zokhudza mwana ameneyu. 18  Onse amene anamva anadabwa ndi zimene abusawo anali kuwauza. 19  Koma Mariya anasunga mawu onsewa ndi kuganizira tanthauzo la zimenezi mumtima mwake.+ 20  Ndiyeno abusa aja anabwerera, akulemekeza ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anamva ndi kuziona, ndendende mmene anawauzira muja. 21  Tsopano masiku 8+ atakwanira kuti achite mdulidwe+ wa mwanayo, anamupatsanso dzina lakuti Yesu.+ Dzina limeneli ndi limene mngelo uja anatchula m’mbuyomo, Mariya asanakhale ndi pakati.+ 22  Komanso, masiku akuti iwo ayeretsedwe+ malinga ndi chilamulo cha Mose atakwanira, anapita naye ku Yerusalemu kukam’pereka kwa Yehova. 23  Izi zinali zogwirizana ndi zimene Malemba amanena m’chilamulo cha Yehova kuti: “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa adzakhala woyera kwa Yehova.”*+ 24  Kumeneko iwo anapereka nsembe malinga ndi zimene chilamulo cha Yehova chimanena kuti: “Njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.”+ 25  Ndiyeno mu Yerusalemu munali munthu wina dzina lake Simiyoni. Mwamuna ameneyu anali wolungama ndi woopa Mulungu. Anali kuyembekezera nthawi imene Mulungu adzatonthoze Isiraeli,+ ndipo mzimu woyera unali pa iye. 26  Komanso Mulungu anamuululira mwa mzimu woyera kuti sadzafa asanaone Khristu+ wa Yehova. 27  Tsopano motsogoleredwa ndi mzimu,+ anabwera kukachisi. Ndipo pamene makolo a mwanayo, Yesu, anamubweretsa kudzamuchitira mwambo wa chilamulo,+ 28  iye analandira mwanayo m’manja mwake ndi kutamanda Mulungu, kuti: 29  “Tsopano, Ambuye Wamkulu Koposa, mukulola kapolo wanu kupita mu mtendere+ malinga ndi zimene inu munanena. 30  Chifukwa maso anga aona njira yanu yopulumutsira+ 31  imene mwakonzeratu pamaso pa mitundu yonse ya anthu.+ 32  Maso anga aona kuwala+ kochotsa nsalu yophimba+ mitundu ya anthu+ ndi ulemerero wa anthu anu Aisiraeli.” 33  Bambo ake ndi mayi ake anali kungodabwa ndi zimene Simiyoni anali kunena zokhudza mwanayo. 34  Komanso, Simiyoni anadalitsa makolowo, ndipo anauza Mariya, mayi a mwanayo kuti: “Tamverani! Uyu waikidwa kuti ambiri agwe,+ ndiponso kuti ambiri adzukenso mu Isiraeli,+ ndi kuti akhale chizindikiro chimene anthu adzachitsutse+ 35  kuti zimene anthu ambiri akuganiza mumtima mwawo zionekere poyera.+ Koma iwe lupanga lalitali lidzalasa moyo wako.”+ 36  Kunalinso Anna mneneri wamkazi, mwana wa Fanueli, wa fuko la Aseri. Mayi ameneyu anali wachikulire kwambiri, ndipo anakhala ndi mwamuna wake zaka 7 zokha kuchokera pa unamwali wake. 37  Tsopano anali mkazi wamasiye,+ ndipo anali ndi zaka 84 koma sanali kusowa pakachisi. Anali kuchita utumiki wopatulika usana ndi usiku,+ anali kusala kudya ndi kupereka mapembedzero. 38  Mu ola limenelo, iye anafika pafupi ndi kuyamba kuyamika Mulungu. Komanso analankhula za mwanayo kwa onse amene anali kuyembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.+ 39  Choncho, atachita zonse mogwirizana ndi chilamulo+ cha Yehova, anabwerera ku Galileya, kumzinda wawo wa Nazareti.+ 40  Ndipo mwanayo anali kukulirakulira ndi kukhala wamphamvu.+ Nzeru zake zinali kuchuluka ndipo Mulungu anapitiriza kukondwera naye.+ 41  Tsopano chaka ndi chaka makolo ake anali kukonda kupita ku Yerusalemu,+ ku chikondwerero cha pasika. 42  Choncho pamene anali ndi zaka 12, iwo anapita naye kumeneko malinga ndi mwambo+ wa chikondwererocho, 43  ndipo anakhala kumeneko mpaka tsiku lomaliza. Koma pamene anali kubwerera, mnyamatayo Yesu anatsalira ku Yerusalemu, ndipo makolo ake sanadziwe zimenezo. 44  Poganiza kuti iye anali nawo m’gulu la anthu apaulendowo, anayenda ulendo wa tsiku lathunthu.+ Kenako anayamba kumufunafuna mwa achibale ndi anzawo. 45  Koma atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anamufufuza pena paliponse. 46  Tsopano patapita masiku atatu, anamupeza ali m’kachisi,+ atakhala pakati pa aphunzitsi. Anali kuwamvetsera ndi kuwafunsa mafunso. 47  Koma onse amene anali kumumvetsera anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.+ 48  Makolo akewo atamuona anadabwa kwambiri, ndipo mayi ake anamufunsa kuti: “Mwanawe, n’chifukwa chiyani wativutitsa chonchi? Ine ndi bambo akowa tinada nkhawa kwambiri ndipo timakufunafuna.” 49  Koma iye anawayankha kuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kodi simunadziwe kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?”+ 50  Koma iwo sanamvetse zimene anali kuwauzazo.+ 51  Pamenepo ananyamuka nawo limodzi kubwerera ku Nazareti, ndipo anapitiriza kuwamvera.+ Apanso mayi akewo anasunga mosamala kwambiri mawu onsewa mumtima mwawo.+ 52  Koma Yesu anali kukulabe m’nzeru+ ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kukondwera naye.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.