Luka 6:1-49
6 Tsiku lina pa sabata, Yesu anali kudutsa m’munda wa tirigu, ndipo ophunzira ake anali kubudula+ ngala za tirigu. Anali kuzifikisa m’manja mwawo n’kumadya.+
2 Afarisi ena ataona zimenezi anati: “N’chifukwa chiyani mukuchita zosemphana ndi malamulo+ pa sabata?”+
3 Koma Yesu anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide+ anachita pamene iye ndi amuna amene anali naye anamva njala?+
4 Kodi simunawerenge kuti analowa m’nyumba ya Mulungu ndi kutenga mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu+ n’kudya, ndipo ina anapatsa amuna amene anali naye limodzi? Malamulo salola aliyense kudya mkate umenewu koma ansembe okha.”+
5 Kenako anapitiriza kuwauza kuti: “Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa sabata.”+
6 Tsiku linanso la sabata,+ iye analowa m’sunagoge n’kuyamba kuphunzitsa. Mmenemo munali munthu amene dzanja lake lamanja linali lopuwala.+
7 Alembi ndi Afarisi anali kumuyang’anitsitsa+ tsopano, kuti aone ngati angachiritse munthu pa sabata. Iwo anali n’cholinga chakuti am’peze chifukwa.+
8 Koma iye anadziwa zimene iwo anali kuganiza.+ Choncho anauza munthu wa dzanja lopuwalayo kuti: “Nyamuka, uimirire pakatipa.” Munthuyo ananyamuka n’kuima chilili.+
9 Pamenepo Yesu anawafunsa kuti: “Ndikufunseni anthu inu, Kodi malamulo amalola kuchita chiti pa sabata? Chabwino kapena choipa?+ Kupulumutsa moyo kapena kuuwononga?”+
10 Atamwaza maso uku ndi uku kuwayang’ana onsewo, anauza munthu uja kuti: “Tambasula dzanja lako.” Munthuyo anachitadi zimenezo, ndipo dzanja lakelo linakhalanso labwinobwino.+
11 Koma iwo anapenga ndi mkwiyo ndipo anayamba kukambirana zoti amuchite Yesu.+
12 M’masiku amenewa, Yesu anapita kuphiri kukapemphera,+ ndipo anachezera kupemphera kwa Mulungu usiku wonse.+
13 Kutacha, anaitana ophunzira ake ndi kusankha 12 pakati pawo. Amenewa anawatcha “atumwi.”+
14 Iye anasankha Simoni, amenenso anam’patsa dzina lakuti Petulo,+ ndi m’bale wake Andireya. Anasankhanso Yakobo ndi Yohane,+ Filipo+ ndi Batolomeyo,
15 Mateyu ndi Tomasi,+ Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwa “wachangu.”+
16 Komanso anasankha Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anam’pereka.+
17 Kenako anatsika nawo ndi kuima pamalo am’munsi, athyathyathya. Pamenepo panali khamu lalikulu la ophunzira ake. Panalinso chikhamu cha anthu+ ochokera ku Yudeya konse ndi ku Yerusalemu konse, komanso kumadera am’mphepete mwa nyanja a ku Turo ndi ku Sidoni. Onsewo anabwera kudzamumvetsera ndi kudzachiritsidwa matenda awo.+
18 Ngakhalenso amene anali kusautsidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa.
19 Onse m’khamulo anali kuyesetsa kuti amukhudze,+ chifukwa mphamvu+ zinali kutuluka mwa iye ndi kuchiritsa onsewo.
20 Pamenepo anakweza maso ake ndi kuyang’ana ophunzira ake, ndipo anawauza kuti:+
“Odala ndinu osaukanu,+ chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.
21 “Inu amene mukumva njala+ tsopano ndinu odala, chifukwa mudzakhuta.+
“Inu amene mukulira tsopano ndinu odala, chifukwa mudzaseka.+
22 “Ndinu odala anthu akamadana nanu,+ kukusalani, kukunyozani ndi kukana+ dzina lanu n’kumanena kuti ndi loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu.
23 Kondwerani pa tsiku limenelo ndi kudumphadumpha, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti zomwezo ndi zimenenso makolo awo akale anachitira aneneri.+
24 “Koma tsoka inu anthu achuma,+ chifukwa mwalandiriratu zonse zokusangalatsani.+
25 “Tsoka inu amene mukukhuta tsopano, chifukwa mudzamva njala.+
“Tsoka inu amene mukuseka tsopano, chifukwa mudzamva chisoni ndi kulira.+
26 “Muli ndi tsoka, anthu onse akamanena zabwino za inu, pakuti zoterezi n’zimene makolo awo akale anachitira aneneri onyenga.+
27 “Koma inu amene mukumvetseranu ine ndikukuuzani kuti, Pitirizani kukonda adani anu+ ndi kuchita zabwino+ kwa amene akudana nanu.
28 Pitirizani kudalitsa okutembererani ndi kupempherera amene akukunyozani.+
29 Amene wakumenya patsaya ili,+ um’patsenso linalo. Amene wakulanda+ malaya ako akunja, usamuletse kutenga malaya ako amkati.
30 Aliyense amene wakupempha kanthu mupatse,+ ndipo amene wakulanda zinthu usamuumirize kuti abweze.
31 “Komanso, zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.+
32 “Kodi mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, mudzapeza phindu lotani? Pakuti ngakhale ochimwa amakonda amene amawakonda.+
33 Ngati mumachita zabwino kwa okhawo amene amakuchitirani zabwino, mudzapindulanji kwenikweni? Pakuti ngakhale ochimwa amachita zomwezo.+
34 Komanso, ngati mumakongoza popanda chiwongoladzanja+ kwa okhawo amene mukuyembekezera kuti adzabweza ngongoleyo, mudzapindulanji? Ochimwanso amakongoza ochimwa anzawo popanda chiwongoladzanja, kuti adzawabwezere zomwezo.+
35 Mosiyana ndi zimenezo, inu pitirizani kukonda adani anu. Pitirizani kuchita zabwino, ndi kukongoza+ popanda chiwongoladzanja, osayembekezera kulandira kalikonse. Mukatero, mphoto yanu idzakhala yaikulu ndipo mudzakhala ana a Wam’mwambamwamba,+ chifukwa iye ndi wachifundo+ kwa osayamika ndi kwa oipa.
36 Pitirizani kukhala achifundo, potengera Atate wanu amenenso ali wachifundo.+
37 “Komanso, lekani kuweruza ena, mukatero inunso simudzaweruzidwa.+ Lekani kutsutsa ena, ndipo inunso simudzatsutsidwa. Pitirizani kukhululukira anthu machimo awo ndipo machimo anunso adzakhululukidwa.+
38 Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.+ Adzakhuthulira m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”+
39 Kenako anawauzanso fanizo lakuti: “Wakhungu sangatsogolere wakhungu mnzake, angatero ngati? Ngati atatero onse awiri angagwere m’dzenje, si choncho kodi?+
40 Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense amene waphunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake.+
41 Nanga n’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso kamene kali m’diso la m’bale wako, koma osaona mtanda wa denga la nyumba umene uli m’diso lako?+
42 Ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘M’bale, taima ndikuchotse kachitsotso kamene kali m’diso lakoka,’ koma iwe osaona mtanda wa denga la nyumba umene uli m’diso lako?+ Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo,+ ndipo ukatero udzatha kuona bwinobwino mmene ungachotsere kachitsotso kamene kali m’diso la m’bale wako.+
43 “Kulibe mtengo wabwino umene ungabale chipatso chowola. Ndipo palibe mtengo wowola umene ungabale chipatso chabwino.+
44 Pakuti mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake.+ Mwachitsanzo, anthu sathyola nkhuyu mumtengo waminga, kapena kudula mphesa m’chitsamba chaminga.+
45 Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino+ cha mtima wake. Koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma chake choipa, pakuti pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.+
46 “Nanga n’chifukwa chiyani mumandiitana kuti ‘Ambuye! Ambuye!’ koma osachita zimene ndimanena?+
47 Aliyense wobwera kwa ine kudzamva mawu anga, ndi kuwachita, ndikuuzani amene amafanana naye:+
48 Iyeyo ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama kwambiri ndi kuyala maziko pathanthwe. Ndipo pamene mtsinje unasefukira,+ madzi anawomba nyumbayo, koma sanathe kuigwedeza, chifukwa anaimanga bwino.+
49 Koma amene akumva ndi kusachita,+ ali ngati munthu womanga nyumba yopanda maziko padothi. Apanso mtsinje unasefukira n’kuwomba nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo inagwa, mwakuti kugwa+ kwa nyumba imeneyo kunali kwamkokomo.”+