Luka 20:1-47
20 Tsiku lina pamene anali kuphunzitsa anthu m’kachisi ndi kulengeza uthenga wabwino, panafika ansembe aakulu, alembi pamodzi ndi akulu.+
2 Iwo anamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+
3 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Inenso ndikufunsani funso limodzi, ndipo mundiyankhe:+
4 Kodi ubatizo wa Yohane unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu?”+
5 Pamenepo iwo anayamba kukambirana okhaokha kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye anena kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’+
6 Koma tikanena kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ anthu onsewa atiponya miyala,+ chifukwa iwo akukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yohane+ anali mneneri.”+
7 Choncho anayankha kuti sakudziwa kumene unachokera.
8 Pamenepo Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”+
9 Ndiyeno iye anayamba kuuza anthuwo fanizo ili: “Munthu wina analima munda wa mpesa,+ ndipo anasiya mundawo m’manja mwa alimi n’kupita kudziko lina kumene anakhalako nthawi yaitali ndithu.+
10 Koma nyengo ya zipatso itakwana anatumiza kapolo+ wake kwa alimiwo,+ kuti akamupatseko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo.+ Komano alimiwo anamumenya ndi kumubweza chimanjamanja.+
11 Koma iye anawatumiziranso kapolo wina. Ameneyonso anamumenya ndi kumuchitira chipongwe, ndipo anamubweza chimanjamanja.+
12 Anatumizanso wachitatu.+ Uyunso anamuvulaza ndi kumuponya kunja.
13 Zitatero mwini munda wa mpesa uja anati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Chabwino, nditumiza mwana wanga wokondedwa.+ Mwana wanga yekhayu ayenera kuti akamulemekeza ndithu.’
14 Alimiwo atamuona anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa. Tiyeni timuphe kuti cholowacho chikhale chathu.’+
15 Atatero anamutulutsa+ m’munda wa mpesawo ndi kumupha.+ Pamenepa, kodi mwini munda wa mpesa uja adzachita chiyani kwa alimiwo?+
16 Adzabwera ndi kupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.”+
Atamva zimenezi iwo anati: “Ayi zisatero ndithu!”
17 Koma iye anawayang’ana ndi kunena kuti: “Pajatu malemba amati, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana,+ umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.’+ Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani?
18 Aliyense wogwera pamwala umenewo adzaphwanyika.+ Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere,+ udzam’pereratu.”+
19 Tsopano alembi ndi ansembe aakulu aja, pozindikira kuti iye anali kunena za iwo mufanizolo, anayesetsa kupeza mpata kuti amugwire ola lomwelo, koma anaopa anthu.+
20 Ndiyeno ataonetsetsa zochita zake, anatuma aganyu mwachinsinsi kuti akadzionetse ngati olungama, n’cholinga choti akamukole+ m’mawu ake, kuti akamupereke ku boma ndi kwa bwanamkubwa.+
21 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti mumanena ndi kuphunzitsa molondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi.+
22 Kodi n’kololeka kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”+
23 Koma Yesu anazindikira ndale zawo ndipo anawauza kuti:+
24 “Ndionetseni khobidi la dinari. Kodi nkhope ndi mawu ali pamenepo n’zandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.”+
25 Iye anawauza kuti: “Chotero perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+
26 Pamenepo iwo analephera kumutapa m’kamwa pa zimene ananenazi pamaso pa anthu, mwakuti pothedwa nzeru ndi yankho lake, anangokhala chete kusowa chonena.+
27 Koma Asaduki ena, amene amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa anafika+ ndi kuyamba kumufunsa,
28 kuti: “Mphunzitsi, Mose+ anatilembera kuti, ‘Ngati munthu wamwalira n’kusiya mkazi amene sanabereke naye ana, m’bale wake+ atenge mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana mwa mkaziyo.’+
29 Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anatenga mkazi, koma anamwalira wopanda mwana.+
30 Wachiwirinso chimodzimodzi.
31 Kenako wachitatu anamutenga. Zinachitika chimodzimodzi kwa amuna onse 7 aja: onse anamwalira osasiya ana.+
32 Pa mapeto pake mkazi uja nayenso anamwalira.+
33 Kodi pamenepa, pouka kwa akufa, mkazi ameneyu adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatira?”+
34 Yesu anawayankha kuti: “Ana a m’nthawi* ino amakwatira+ ndi kukwatiwa.
35 Koma amene ayesedwa oyenerera+ kudzapeza moyo pa nthawi* imeneyo+ ndi kudzaukitsidwa kwa akufa+ sadzakwatira kapena kukwatiwa.
36 Ndiponso iwo sadzafanso,+ chifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu mwa kukhala ana a kuuka kwa akufa.+
37 Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza m’nkhani ya chitsamba cha minga.+ M’nkhani imeneyo iye ananena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’+
38 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo.”+
39 Poyankha ena mwa alembiwo anati: “Mphunzitsi, mwanena bwino.”
40 Ananena zimenezi chifukwa sanathenso kulimba mtima kuti amufunse funso lina ngakhale limodzi.
41 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+
42 Pakuti Davide mwiniyo ananena m’buku la Masalimo kuti, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja
43 kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”’+
44 Chotero Davide anamutcha ‘Ambuye.’ Nanga akukhala bwanji mwana wake?”
45 Kenako, anthu onse akumvetsera, iye anauza ophunzirawo kuti:+
46 “Chenjerani ndi alembi. Iwo amakonda kuyendayenda atavala mikanjo. Amakonda kupatsidwa moni m’misika ndi kukhala m’mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo.+
47 Iwo ndi amene amadyerera nyumba za akazi amasiye,+ ndipo mwachiphamaso amapereka mapemphero ataliatali. Anthu amenewa adzalandira chiweruzo champhamvu.”+