Luka 21:1-38
21 Tsopano atakweza maso anaona anthu olemera akuponya zopereka zawo moponyamo zopereka.+
2 Kenako anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobidi tiwiri tating’ono mmenemo.+
3 Ndipo iye anati: “Kunena zoona, Mkazi wamasiyeyu, ngakhale kuti ndi wosauka, waponya zochuluka kuposa onse amene aponya.+
4 Pakuti onsewa aponya zopereka zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene akanatha kuchirikiza nazo moyo wake.”+
5 Nthawi ina, anthu ena anali kulankhula za kachisi, mmene anam’kongoletsera ndi miyala yochititsa kaso komanso mphatso zoperekedwa kwa Mulungu.+
6 Choncho iye anati: “Kunena za zinthu izi mukuzionazi, masiku adzafika pamene sipadzakhala mwala wosiyidwa pano pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+
7 Pamenepo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti kwenikweni, ndipo chizindikiro chosonyeza kuti zili pafupi kuchitika n’chiyani?”+
8 Iye anayankha kuti: “Samalani kuti asadzakusocheretseni.+ Pakuti ambiri adzabwera m’dzina langa, n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ adzanenanso kuti, ‘Nthawi ija yayandikira.’+ Musadzawatsatire.
9 Komanso, mukadzamva phokoso la nkhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha.+ Pakuti zimenezi ziyenera kuchitika choyamba, koma mapeto sadzafika nthawi yomweyo.”
10 Anapitiriza kuwauza kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina,+ ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+
11 Kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala+ m’malo osiyanasiyana. Kudzaoneka zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa.+
12 “Koma zonsezi zisanachitike, anthu adzakugwirani ndi kukuzunzani,+ adzakuperekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakutengerani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa.+
13 Umenewu udzakhala mpata wanu wochitira umboni.+
14 Chotero tsimikizirani m’mitima yanu kuti musachite kukonzekera zoti mukayankhe podziteteza,+
15 chifukwa ine ndidzakuuzani mawu oti munene ndi kukupatsani nzeru, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.+
16 Komanso makolo anu enieniwo,+ abale anu, anthu oyandikana nanu ndi mabwenzi anu, adzakuperekani, ndipo adzapha ena a inu.+
17 Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+
18 Komatu ngakhale tsitsi limodzi lokha+ la m’mutu mwanu silidzawonongeka ayi.
19 Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.+
20 “Chinanso, mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu,+ mudzadziwe kuti chiwonongeko chake chayandikira.+
21 Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali m’madera akumidzi asadzalowe mumzindawo,+
22 chifukwa amenewa ndi masiku obwezera chilango, kuti zonse zimene zinalembedwa zikwaniritsidwe.+
23 Tsoka kwa akazi apakati ndi kwa oyamwitsa ana m’masiku amenewo!+ Pakuti m’dzikoli mudzakhala mavuto aakulu ndi mkwiyo pa anthu awa.
24 Anthu adzaphedwa ndi lupanga ndiponso kutengedwa ukapolo kupita nawo ku mitundu ina yonse.+ Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu, kufikira nthawi zoikidwiratu+ za anthu a mitundu inawo zitakwanira.
25 “Komanso, padzakhala zizindikiro padzuwa,+ mwezi ndi nyenyezi. Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika, ndipo adzathedwa nzeru chifukwa cha mkokomo wa nyanja+ ndi kuwinduka kwake.+
26 Mwakuti anthu adzakomoka chifukwa cha mantha+ ndi kuyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi+ kumene kuli anthu, pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.+
27 Kenako adzaona Mwana wa munthu+ akubwera mumtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.+
28 Koma zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire chilili ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.”
29 Atanena izi, anawauza fanizo kuti: “Onetsetsani mtengo wa mkuyu ndi mitengo ina yonse:+
30 Mukaona mitengo ikuphukira, mumadziwa ndithu kuti tsopano dzinja lili pafupi.+
31 Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.+
32 Ndithu ndikukuuzani, M’badwo umenewu sudzatha wonse kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zitachitika.+
33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka,+ koma mawu anga sadzachoka ayi.+
34 “Koma samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri,+ ndi nkhawa+ za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa+
35 ngati msampha.+ Pakuti lidzafikira onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi.+
36 Chotero khalani maso+ ndipo muzipemphera mopembedzera+ nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.”+
37 Masana Yesu anali kuphunzitsa m’kachisi,+ koma usiku anali kupita kukagona kuphiri lotchedwa phiri la Maolivi.+
38 Ndipo anthu onse+ anali kulawirira m’mawa kwambiri kupita kwa iye kukachisi kuti akamumvetsere.