Luka 13:1-35

13  Pa nthawiyo, panali anthu ena amene anam’fotokozera za Agalileya+ amene magazi awo, Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo.  Choncho poyankha iye anawauza kuti: “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewo anali ochimwa kwambiri+ kuposa Agalileya ena onse chifukwa chakuti zimenezo zinawachitikira?  Ndithudi ayi. Choncho ndikukuuzani kuti ngati simulapa, nonsenu mudzawonongeka mofanana ndi iwowo.+  Nanga bwanji za anthu 18 aja, amene nsanja inawagwera ku Siloamu n’kuwapha? Kodi mukuganiza kuti iwo anali ochimwa kwambiri kuposa anthu onse okhala mu Yerusalemu?  Ndithudi ayi. Choncho ndikukuuzani kuti, ngati simulapa, nonsenu mudzawonongeka ngati mmene iwo anawonongekera.”+  Kenako anayamba kufotokoza fanizo ili: “Munthu wina anali ndi mkuyu m’munda wake wa mpesa,+ ndipo anapita kukafuna chipatso mumtengowo,+ koma sanapezemo chilichonse.+  Ndiyeno anauza munthu wosamalira munda wa mpesawo kuti, ‘Kwa zaka zitatu+ tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna nkhuyu mumtengo uwu, koma sindinapezemo ngakhale imodzi. Dula mtengo umenewu!+ N’chifukwa chiyani ukungowononga nthaka?’  Wosamalira mundayo anayankha kuti, ‘Mbuyanga, bwanji muusiye+ chaka chino chokha. Ine ndikumba mouzungulira n’kuthirapo manyowa.  Ukadzabala zipatso m’tsogolo, zidzakhala bwino, koma ngati sudzabala mudzaudule.’”+ 10  Tsopano anali kuphunzitsa m’sunagoge winawake pa sabata. 11  Mmenemo munali mayi wina amene mzimu+ woipa unamudwalitsa zaka 18. Anali wopindika msana moti sankatha kuweramuka. 12  Yesu atamuona, anamulankhula kuti: “Mayi, mwamasuka+ ku matenda anu.” 13  Pamenepo anaika manja ake pamayiyo, ndipo nthawi yomweyo anaweramuka,+ n’kuyamba kutamanda Mulungu. 14  Koma mtsogoleri wa sunagoge ataona izi, anakwiya chifukwa Yesu anachiritsa munthu pa sabata.+ Choncho anayamba kuuza khamu la anthu kuti: “Pali masiku 6 oyenera kugwira ntchito. Muzibwera masiku amenewo kudzachiritsidwa, osati tsiku la sabata.”+ 15  Koma Ambuye anamuyankha kuti: “Onyenga inu,+ kodi aliyense wa inu samasula ng’ombe yake kapena bulu wake m’khola pa sabata ndi kupita naye kukam’mwetsa madzi?+ 16  Kodi sikunali koyenera kuti mayi uyu, amenenso ndi mwana wa Abulahamu,+ amene Satana anamumanga zaka 18, amasulidwe m’maunyolo amenewa tsiku la sabata?” 17  Atanena zimenezi, onse omutsutsa anachita manyazi.+ Koma khamu lonse la anthu linayamba kukondwera ndi zodabwitsa zonse zimene iye anachita.+ 18  Pamenepo anapitiriza kuti: “Kodi ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, ndiuyerekeze ndi chiyani?+ 19  Uli ngati kanjere ka mpiru,* kamene munthu anakatenga ndi kukaponya m’munda wake. Kenako kanamera ndi kukhala mtengo, moti mbalame zam’mlengalenga+ zinapeza malo okhala m’nthambi zake.”+ 20  Iye ananenanso kuti: “Kodi ufumu wa Mulungu ndiuyerekeze ndi chiyani? 21  Uli ngati chofufumitsa chimene mayi wina anachitenga ndi kuchibisa mu ufa wokwana mbale zoyezera zazikulu zitatu, moti mtanda wonsewo unafufuma.”+ 22  Yesu anayenda mumzinda ndi mzinda, komanso mudzi ndi mudzi. Anali kuphunzitsa ndi kupitiriza ulendo wake wopita ku Yerusalemu.+ 23  Tsopano munthu wina anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi amene akupulumuka ndi owerengeka okha?”+ Iye anawauza kuti: 24  “Yesetsani+ mwamphamvu kulowa pakhomo lopapatiza.+ Chifukwa ambiri ndikukuuzani, adzafunitsitsa kulowamo koma sadzatha.+ 25  Mwininyumba akanyamuka ndi kukakhoma chitseko, ndiyeno inu n’kuima panja ndi kuyamba kugogoda pachitsekopo, n’kumanena kuti, ‘Titsegulireni ambuye,’+ iye poyankha adzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera.’+ 26  Pamenepo mudzayamba kunena kuti, ‘Tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo inu munaphunzitsa m’misewu yathu.’+ 27  Koma iye adzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera. Ndichokereni pano, nonsenu ochita zinthu zosalungama!’+ 28  Kunjako n’kumene inu mudzalira ndi kukukuta mano,+ pamene mudzaona Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, komanso aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu,+ koma inuyo atakukankhirani kunja. 29  Komanso, anthu adzabwera kuchokera kumbali za kum’mawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kum’mwera,+ ndipo adzadya patebulo mu ufumu wa Mulungu.+ 30  Ndithudi amene ali omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.”+ 31  Mu ola lomwelo kunafika Afarisi ena ndi kumuuza kuti: “Nyamukani muchoke kuno, chifukwa Herode* akufuna kukuphani.” 32  Iye anawayankha kuti: “Pitani mukaiuze nkhandwe+ imeneyo kuti, ‘Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchita ntchito yochiritsa lero ndi mawa, tsiku lachitatu ndidzamaliza.’+ 33  Komabe ndiyenera kupitiriza ulendo wanga lero ndi mawa ndi tsiku linalo, chifukwa n’kosayenera kuti mneneri amuphere kunja kwa Yerusalemu.+ 34  Yerusalemu, Yerusalemu! wakupha+ aneneri ndi kuponya miyala+ anthu otumidwa kwa iwe . . . mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako monga mmene nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko ake,+ koma anthu inu simunafune zimenezo.+ 35  Tsopano tamverani! Mulungu wachoka ndi kukusiyirani nyumba* yanuyi.+ Ndithu ndikukuuzani, simudzandionanso kufikira pamene mudzanene kuti, ‘Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!’”+

Mawu a M'munsi

“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakang’ono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita anayi ndipo kamachita nthambi.
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.
Kutanthauza kachisi.