Luka 8:1-56

8  Mosakhalitsa, Yesu anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira+ ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ndipo atumwi 12 aja anali naye limodzi.  Analinso ndi amayi+ ena amene anawatulutsa mizimu yoipa ndi kuwachiritsa matenda awo. Ena mwa iwo anali Mariya wotchedwanso Mmagadala, amene anamutulutsa ziwanda 7.+  Jowana+ mkazi wa Kuza kapitawo wa Herode, Suzana ndi amayi ena ambiri, amene anali kutumikira Yesu ndi atumwiwo pogwiritsa ntchito chuma chawo.  Ndiyeno khamu lalikulu la anthu litasonkhana, limodzi ndi ena amene anali kumulondola kuchokera m’mizinda yosiyanasiyana, Yesu anawafotokozera fanizo kuti:+  “Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu zake. Pamene anali kufesa, zina zinagwera m’mbali mwa msewu ndipo zinapondedwapondedwa, kenako zinadyedwa ndi mbalame zam’mlengalenga.+  Zina zinagwera pathanthwe. Koma zitamera, zinauma chifukwa panalibe chinyontho.+  Zinanso zinagwera paminga. Mingazo zinali kukulira limodzi ndi mbewuzo ndipo zinalepheretsa mbewuzo kukula.+  Koma zina zinagwera panthaka yabwino, ndipo zitakula, zinabala zipatso kuwirikiza maulendo 100.”+ Atanena zimenezi, analankhula mokweza mawu kuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+  Koma ophunzira ake anayamba kumufunsa tanthauzo la fanizo limeneli.+ 10  Iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira zinsinsi zopatulika za ufumu wa Mulungu. Koma kwa enawo, zonse ndi mafanizo okhaokha.+ Izi zili choncho kuti kuona aziona ndithu, koma kukhale kopanda phindu, kumvanso azimva ndithu, koma asazindikire tanthauzo lake.+ 11  Koma fanizoli+ tanthauzo lake ndi ili: Mbewuzo ndi mawu a Mulungu.+ 12  Zogwera m’mbali mwa msewuzo ndi anthu amene amamva mawuwo.+ Kenako Mdyerekezi+ amabwera ndi kudzachotsa mawuwo m’mitima yawo kuti asakhulupirire ndi kupulumuka.+ 13  Zogwera pathanthwe ndi anthu amene amati akangomva mawuwo, amawalandira ndi chimwemwe, koma oterewa alibe mizu. Amakhulupirira kwa kanthawi, koma nthawi yoyesedwa ikafika amagwa.+ 14  Zimene zinagwera paminga, ndi anthu amene amva mawu a Mulungu. Koma chifukwa chotengeka ndi nkhawa, chuma ndi zosangalatsa za moyo uno,+ amalephera kukula bwino, ndipo zipatso zawo sizikhwima.+ 15  Komano zogwera panthaka yabwino, ndi anthu amene pambuyo pomva mawuwo ndi mtima woona+ komanso wabwino, amawagwiritsitsa ndi kubereka zipatso mwa kupirira.+ 16  “Palibe amene amati akayatsa nyale, amaivundikira ndi chiwiya kapena kuiika pansi pa bedi. Koma amaiika pachoikapo nyale kuti amene akulowa aone kuwala.+ 17  Chilichonse chobisidwa+ chidzaonekera poyera. Ndipo zinthu zonse zosungidwa mwachinsinsi kwambiri zidzadziwika ndi kuululika.+ 18  Choncho muzimvetsera mwatcheru kwambiri. Pakuti amene ali nazo, adzapatsidwa zochuluka,+ koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene akuganizira kuti ali nazo.”+ 19  Tsopano mayi ake ndi abale ake+ anabwera kumeneko, koma chifukwa cha khamu la anthu, analephera kufika kumene iyeyo anali.+ 20  Koma ena anamuuza kuti: “Mayi anu ndi abale anu aima panjapo akufuna kuonana nanu.”+ 21  Poyankha Yesu anawauza kuti: “Mayi anga ndi abale anga ndi awa amene amamvetsera mawu a Mulungu ndi kuwachita.”+ 22  Tsiku lina m’masiku amenewo Yesu ndi ophunzira ake anakwera ngalawa, ndipo anawauza kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja.” Pamenepo iwo anayamba kupalasa.+ 23  Koma ulendowo uli mkati Yesu anagona tulo. Kenako panyanjapo panayamba kuwomba mphepo yamkuntho, ndipo madzi anayamba kudzaza m’ngalawamo moti akanatha kumira.+ 24  Kenako anapita kwa iye kukam’dzutsa. Iwo anati: “Mlangizi, Mlangizi, tikufa!”+ Chotero iye anadzuka ndi kudzudzula+ mphepo ndi mafunde amphamvuwo, mwakuti zinaleka, ndipo panachita bata. 25  Ndiyeno anawafunsa kuti: “Chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo anagwidwa ndi mantha ndipo anathedwa nzeru, mwakuti anayamba kufunsana kuti: “Kodi ameneyu ndani kwenikweni, wochita kulamula mphepo ndi madzi ndipo n’kumumvera?”+ 26  Ndiyeno anakocheza m’dera la Agerasa, tsidya linalo, moyang’anana ndi Galileya.+ 27  Koma atangotsika n’kufika kumtunda, anakumana ndi munthu wina waziwanda wochokera mumzindawo. Kwa nthawi yaitali ndithu, munthuyo anali kungokhala osavala, komanso sanali kukhala kunyumba, koma kumanda.+ 28  Ataona Yesu anafuula kwambiri ndi kudzigwetsa pansi pamaso pake. Kenako anafuula ndi mawu amphamvu kuti: “Kodi ndili nanu chiyani,+ Yesu, Mwana wa Mulungu Wam’mwambamwamba? Chonde, chonde, musandizunze.”+ 29  (Pakuti iye anali kuuza mzimu wonyansawo kuti utuluke mwa munthuyo. Mzimu umenewu unamugwira mwamphamvu+ kwa nthawi yaitali ndithu. Mobwerezabwereza anali kumumanga ndi maunyolo komanso matangadza n’kumamuyang’anira. Koma chifukwa cha mphamvu ya chiwandacho, anali kudula maunyolowo ndi kuthawira kumalo opanda anthu.) 30  Yesu anamufunsa kuti: “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti: “Khamu,” chifukwa mwa iye munalowa ziwanda zambiri.+ 31  Ziwandazo zinali kumuchonderera+ kuti asazilamule kuti zipite kuphompho.+ 32  Tsopano gulu lalikulu ndithu la nkhumba+ linali kudya paphiri kumeneko. Chotero ziwandazo zinamuchonderera kuti azilole kukalowa munkhumbazo.+ Ndipo iye anazilola. 33  Choncho ziwandazo zinatuluka mwa munthuyo ndi kukalowa munkhumbazo. Pamenepo nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi ndi kulumphira m’nyanja ndipo zinamira.+ 34  Koma oyang’anira ziwetozo ataona zimene zinachitikazo, anathawa ndi kukanena zimenezi mumzinda ndi m’midzi.+ 35  Zitatero anthu anabwera kudzaona zomwe zachitikazo. Atafika kwa Yesu anapeza munthu amene anam’tulutsa ziwanda uja atakhala pansi pafupi ndi Yesu. Anamupeza atavala bwino komanso maganizo ake ali bwinobwino, ndipo iwo anachita mantha.+ 36  Amene anaona zochitikazo anawafotokozera mmene munthu wogwidwa ziwandayo anam’chiritsira.+ 37  Choncho khamu lonse lochokera m’midzi yapafupi ya Agerasa linam’pempha kuti achoke kwawoko, chifukwa linagwidwa ndi mantha aakulu.+ Pamenepo iye anakwera ngalawa kuti azipita. 38  Ndiyeno munthu amene anam’tulutsa ziwanda uja anapempha kuti aziyenda naye. Koma Yesu anauza munthuyo kuti apite kwawo. Iye anati:+ 39  “Pita kunyumba, ndipo ukafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.”+ Munthu uja anapitadi, ndipo anali kufalitsa mumzinda wonsewo zimene Yesu anam’chitira.+ 40  Yesu atabwerera ku Galileya, khamu la anthu linamulandira ndi manja awiri, chifukwa onse anali kumuyembekeza.+ 41  Kenako panafika munthu wina dzina lake Yairo. Iyeyu anali mtsogoleri wa sunagoge. Ndiyeno anadzigwetsa pamapazi a Yesu ndi kum’chonderera kuti akalowe m’nyumba yake.+ 42  Yairo anachita zimenezi chifukwa mwana wake wamkazi wazaka pafupifupi 12, mwana yekhayo amene anali naye, anali pafupi kumwalira.+ Pamene anali kupita anthu ambiri anakhamukira komweko.+ 43  Ndiyeno panali mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi+ kwa zaka 12, ndipo palibe aliyense amene anatha kum’chiritsa.+ 44  Mayiyu anamudzera kumbuyo Yesu n’kugwira ulusi wopota wa m’mphepete+ mwa malaya ake akunja.+ Nthawi yomweyo anasiya kutaya magazi.+ 45  Pamenepo Yesu anati: “Ndani wandigwira?”+ Onse atakana, Petulo anati: “Mlangizi, anthu onsewa akuzungulirani ndipo akukupanikizani.”+ 46  Koma Yesu anati: “Wina wandigwira, chifukwa ndamva kuti mphamvu+ yatuluka mwa ine.”+ 47  Mayiyo ataona kuti zimene wachitazo zadziwika anapita kwa Yesu akunjenjemera, ndipo anagwada ndi kuulula pamaso pa anthu onse chimene chinam’chititsa kuti amugwire, komanso mmene wachirira nthawi yomweyo.+ 48  Koma iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.+ Pita mu mtendere.”+ 49  Ali mkati molankhula, panafika nthumwi ya mtsogoleri wa sunagoge uja, ndipo anamuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira. Musiyeni mphunzitsiyu musamuvutitse.”+ 50  Yesu atamva zimenezi, anamuyankha kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi,+ ndipo mwana wako apulumuka.” 51  Atafika kunyumbako sanalole kuti aliyense alowe naye kupatulapo Petulo, Yohane ndi Yakobo, komanso bambo ndi mayi a mtsikanayo.+ 52  Koma anthu onse anali kulira ndi kudziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni. Choncho Yesu anawauza kuti: “Tontholani,+ pakuti mwanayu sanamwalire ayi, koma akugona.”+ 53  Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kumuseka monyodola, chifukwa anali kudziwa kuti wamwalira.+ 54  Koma iye anamugwira dzanja ndi kuitana kuti: “Mtsikana iwe, dzuka!”+ 55  Pamenepo mzimu wake+ unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anadzuka.+ Ndiyeno anawauza kuti am’patse chakudya mtsikanayo.+ 56  Pamenepo, makolo akewo anakondwa kwambiri, koma Yesu anawalangiza kuti asauze aliyense zimene zachitikazo.+

Mawu a M'munsi