Luka 17:1-37

17  Kenako Yesu anauza ophunzira ake kuti: “N’zosatheka kuti pakhale popanda zopunthwitsa.+ Koma tsoka kwa munthu amene zopunthwitsazo zimadzera mwa iye!+  Zingamuyendere bwino kwambiri atamukoloweka chimwala cha mphero m’khosi mwake ndi kumuponya m’nyanja,+ kusiyana n’kuti akhumudwitse mmodzi wa tiana iti.+  Samalani ndithu. Ngati m’bale wako wachita tchimo um’dzudzule,+ ndipo akalapa umukhululukire.+  Ngakhale akuchimwire maulendo 7 pa tsiku, n’kubwera kwa iwe maulendo 7, kudzanena kuti, ‘Ndalapa ine,’ umukhululukire ndithu.”+  Tsopano atumwiwo anauza Ambuye kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”+  Pamenepo Ambuye anawayankha kuti: “Mukanakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mukanatha kuuza mtengo wa mabulosi uwu kuti, ‘Zuka pano, kadzibzale m’nyanjamo!’ ndipo ukanakumverani.+  “Ndani wa inu angauze kapolo wake amene wangofika kumene kuchokera ku ntchito yolima kapena yoweta nkhosa kuti, ‘Fika kutebulo kuno msanga udzadye’?  Kodi sadzamuuza kuti, ‘Ndikonzere chakudya chamadzulo, uvale epuloni ndi kunditumikira kufikira nditamaliza kudya ndi kumwa, pambuyo pake iwenso udye ndi kumwa’?  Ndipo munthuyo sangamuyamike kapoloyo chifukwa zimene wachitazo ndi ntchito yake, si choncho kodi? 10  Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munapatsidwa ngati ntchito yanu, muzinena kuti, ‘Ife ndife akapolo opanda pake.+ Tangochita zimene tinayenera kuchita.’” 11  Tsopano pamene anali kupita ku Yerusalemu, anadutsa mkatikati mwa Samariya ndi Galileya.+ 12  Pamene anali kulowa m’mudzi wina, anakumana ndi amuna 10 akhate+ koma iwo anaima chapatali ndithu. 13  Kenako anafuula mokweza, kuti: “Yesu, Mlangizi,+ tichitireni chifundo!” 14  Yesu atawaona anawauza kuti: “Pitani mukadzionetse kwa ansembe.”+ Ndiyeno pamene anali kupita anayeretsedwa.+ 15  Mmodzi wa iwo ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, akutamanda Mulungu+ mokweza mawu. 16  Atafika anagwada pamaso pa Yesu n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ ndipo anamuthokoza. Munthu ameneyu anali Msamariya.+ 17  Pamenepo Yesu anati: “Amene ayeretsedwa si anthu 10 kodi? Nanga ena 9 ali kuti? 18  Kodi sanapezeke wina aliyense wobwerera kudzalemekeza Mulungu koma munthu wa mtundu wina yekhayu?” 19  Ndiyeno Yesu anauza munthuyo kuti: “Nyamuka uzipita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ 20  Tsopano Afarisi atamufunsa kuti ufumu wa Mulungu udzabwera liti,+ iye anawayankha kuti: “Ufumu wa Mulungu sudzabwera mwa maonekedwe ochititsa chidwi ayi. 21  Ndipo anthu sadzanena kuti, ‘Onani kuno!’ kapena, ‘Uko!’+ Pakuti ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”+ 22  Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Adzafika masiku pamene mudzalakalaka kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu koma simudzaliona.+ 23  Ndipo anthu adzakuuzani kuti, ‘Onani uko!’ kapena ‘Onani kuno!’+ Musadzapiteko kapena kuwatsatira.+ 24  Pakuti monga mphezi,+ mwa kung’anima kwake, imawala kuchokera mbali ina pansi pa thambo kukafika mbali ina pansi pa thambo, zidzakhalanso choncho ndi Mwana wa munthu.+ 25  Koma ayenera kukumana ndi mavuto ochuluka choyamba ndi kukanidwa ndi m’badwo uwu.+ 26  Komanso, monga zinachitikira m’masiku a Nowa,+ zidzachitikanso chimodzimodzi m’masiku a Mwana wa munthu.+ 27  M’masiku amenewo anthu anali kudya, kumwa, amuna anali kukwatira, akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa, ndipo chigumula chinafika ndi kuwononga anthu onsewo.+ 28  Chimodzimodzinso ndi zimene zinachitika m’masiku a Loti.+ M’masiku amenewo anthu anali kudya, kumwa, kugula, kugulitsa, kubzala ndi kumanga. 29  Koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule ngati mvula n’kuwononga anthu onse.+ 30  Zidzakhalanso choncho pa tsikulo, pamene Mwana wa munthu adzaonekera.+ 31  “Pa tsiku limenelo, munthu amene adzakhale padenga la nyumba koma katundu wake ali m’nyumbamo, asadzatsike kukatenga katundu wakeyo. Chimodzimodzinso munthu amene adzakhale ali m’munda, asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya m’mbuyo. 32  Kumbukirani mkazi wa Loti.+ 33  Aliyense wofunitsitsa kusunga moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake adzausunga.+ 34  Ndithu ndikukuuzani, Usiku umenewo amuna awiri adzagonera limodzi pamphasa. Mmodzi adzatengedwa, koma wina adzasiyidwa.+ 35  Amayi awiri adzakhala akupera limodzi pamphero. Mmodzi adzatengedwa, koma wina adzasiyidwa.”+ 36 * —— 37  Choncho iwo anamufunsa kuti: “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti Ambuye?” Iye anawauza kuti: “Kumene kuli thupi lakufa,+ ziwombankhanga zidzasonkhana komweko.”+

Mawu a M'munsi

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.