Luka 7:1-50

7  Yesu atamaliza mawu ake onse amene anthu anali kumvetsera, analowa mumzinda wa Kaperenao.+  Kumeneko kapolo wa kapitawo wina wa asilikali, amene kapitawoyo anali kum’konda kwambiri, anali kudwala ndipo anali pafupi kumwalira.+  Kapitawoyo atamva za Yesu, anatumiza akulu a Ayuda kwa iye kukam’pempha kuti abwere kudzapulumutsa kapolo wakeyo.  Choncho anthuwo atafika kwa Yesu anayamba kum’chonderera ndi mtima wonse, kuti: “N’ngoyeneradi kuti mum’thandize,  chifukwa amakonda anthu amtundu wathu+ ndipo anatimangira sunagoge.”  Choncho Yesu ananyamuka nawo limodzi. Koma atatsala pang’ono kufika kunyumbako, anakumana ndi mabwenzi a kapitawo wa asilikali uja, amene anawatuma kuti adzamuuze kuti: “Mbuyanga, musavutike, pakuti ine sindili woyenera kuti inu mulowe m’nyumba mwanga.+  N’chifukwa chake inenso sindinabwere kwa inu, poona kuti ndine wosayenera kutero. Koma mungonena mawu okha ndipo mtumiki wanga achira.  Pakuti inenso ndili ndi akuluakulu ondiyang’anira, komanso ndili ndi asilikali amene ali pansi panga. Ndikauza mmodzi kuti, ‘Pita!’ amapita, wina ndikamuuza kuti ‘Bwera!’ amabwera. Kapolo wanga ndikamuuza kuti, ‘Chita ichi!’ amachita.”+  Yesu atamva zimenezi anadabwa ndi munthu ameneyu. Kenako anacheukira khamu la anthu omutsatira aja n’kunena kuti: “Kunena zoona, ngakhale mu Isiraeli sindinapezemo chikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.”+ 10  Koma amene anatumidwa aja atabwerera kunyumba, anapeza kapolo uja ali bwinobwino.+ 11  Patangopita kanthawi pang’ono, ananyamuka kupita kumzinda wotchedwa Naini. Ophunzira ake ndi khamu lalikulu la anthu anayenda naye limodzi. 12  Atayandikira pachipata cha mzindawo, anakumana ndi anthu atanyamula maliro.+ Womwalirayo anali mwana wamwamuna yekhayo+ kwa mayi ake. Komanso mayi akewo anali mkazi wamasiye. Khamu lalikulu ndithu la anthu ochokera mumzindawo linali limodzi ndi mayiwo. 13  Pamene Ambuye anaona mayiwo, anawamvera chifundo,+ ndipo anawauza kuti: “Tontholani mayi.”+ 14  Atatero anayandikira ndi kugwira chithathacho. Pamenepo onyamulawo anangoima chilili, ndipo iye anati: “Mnyamata iwe, ndikunena ndi iwe, Dzuka!”+ 15  Pamenepo wakufayo anadzuka ndi kukhala tsonga, ndipo anayamba kulankhula. Kenako anam’pereka kwa mayi ake.+ 16  Zitatero anthu onse anagwidwa ndi mantha,+ moti anayamba kutamanda Mulungu, kuti: “Mneneri wamkulu+ waonekera pakati pathu.” Analinso kunena kuti, “Mulungu wacheukira anthu ake.”+ 17  Nkhani imeneyi yonena za Yesu inafala ponseponse mu Yudeya monse ndi m’madera onse ozungulira. 18  Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza zonsezi.+ 19  Choncho Yohane anaitanitsa ophunzira ake awiri ndi kuwatuma kwa Ambuye kukafunsa kuti: “Kodi Mesiya* amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?”+ 20  Atafika kwa iye amunawo anati: “Yohane M’batizi watituma kudzakufunsani kuti: ‘Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?’” 21  Mu ola limenelo iye anachiritsa nthenda zambiri+ ndi anthu ambiri odwala mwakayakaya ndi kutulutsa mizimu yoipa. Ndipo anachiritsa akhungu ochuluka moti anayamba kuona. 22  Choncho poyankha anauza amuna awiri aja kuti: “Pitani+ mukamuuze Yohane zimene mwaona ndi kumva: Akhungu+ akuona, olumala akuyenda, akhate akuyeretsedwa, ogontha akumva, akufa akuukitsidwa ndipo aumphawi akumva+ uthenga wabwino.+ 23  Wodala ndi amene sanapunthwe chifukwa cha ine.”+ 24  Amithenga a Yohane aja atachoka, iye anayamba kuuza khamu la anthulo za Yohane kuti: “Kodi munapita m’chipululu kukaona chiyani? Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo?+ 25  Nanga munapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zapamwamba kapena?+ Iyayi, pajatu ovala zovala zapamwamba ndiponso amoyo wamwanaalirenji amakhala m’nyumba zachifumu.+ 26  Nangano munapita kukaona chiyani makamaka? Mneneri kapena?+ Inde, ndikukuuzani, woposadi mneneri.+ 27  Malemba amanena za iyeyu kuti, ‘Taona! Inetu ndikutumiza mthenga wanga choyamba,+ amene adzakukonzera njira.’+ 28  Ndithudi ndikukuuzani, Mwa onse obadwa mwa akazi, palibe wamkulu+ woposa Yohane. Koma munthu amene ali wocheperapo mu ufumu wa Mulungu ndiye wamkulu kuposa iyeyu.”+ 29  (Pamenepo anthu onse ndi okhometsa msonkho omwe atamva zimenezi, analengeza kuti Mulungu ndi wolungama,+ popeza iwo anali atabatizidwa ndi ubatizo wa Yohane.+ 30  Koma Afarisi ndi anthu odziwa Chilamulo ananyalanyaza malangizo+ amene Mulungu anawapatsa. Choncho Yohane sanawabatize.) 31  “Kodi anthu a m’badwo uwu ndiwayerekeze ndi ndani, ndipo akufanana ndi ndani?+ 32  Iwo ali ngati ana aang’ono amene akhala pansi mumsika n’kumafuulirana kuti, ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunalire.’+ 33  Mofanana ndi zimenezi, Yohane M’batizi anabwera ndipo sadya chakudya kapena kumwa vinyo, koma inu mumanena kuti, ‘Ali ndi chiwanda.’+ 34  Kunabwera Mwana wa munthu ndipo iye akudya ndi kumwa, koma inu mumati, ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa!’+ 35  Mulimonsemo, nzeru+ imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha zotsatira zake.”+ 36  Tsopano Mfarisi wina anaumiriza Yesu kuti akadye naye. Choncho anapita kunyumba+ ya Mfarisiyo ndipo anamupatsa chakudya. 37  Koma mayi wina amene anali wodziwika mumzindawo kuti ndi wochimwa, anamva kuti Yesu akudya chakudya m’nyumba ya Mfarisi. Choncho anapita komweko ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala,+ muli mafuta onunkhira. 38  Atafika anagwada kumapazi kwake ndi kuyamba kulira, mwakuti anayamba kunyowetsa mapazi ake ndi misozi, kwinaku akupukuta mapaziwo ndi tsitsi la m’mutu mwake. Komanso anapsompsona mapazi akewo mwachikondi ndi kuwapaka mafuta onunkhirawo. 39  Mfarisi amene anamuitana uja ataona izi, mumtima mwake anati: “Munthu uyu akanakhala mneneri,+ akanadziwa kuti mkazi amene akumugwirayu ndi ndani, ndiponso kuti ndi wotani. Akanadziwa kuti ndi wochimwa.”+ 40  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Simoni, ndikufuna ndikuuze kanthu kena.” Iye anati: “Ndiuzeni Mphunzitsi!” 41  “Amuna awiri anatenga ngongole kwa munthu wina wokongoza ndalama. Mmodzi anatenga ngongole ya madinari 500,+ koma winayo anatenga ngongole ya madinari 50. 42  Atasowa chopereka kuti abweze ngongolezo, mwiniwake uja anakhululukira+ onsewo ndi mtima wonse. Kodi ndani mwa awiriwo amene angam’konde kwambiri?” 43  Poyankha Simoni anati: “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira zochulukayo.” Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola.” 44  Atatero anacheukira mayi uja ndi kuuza Simoni kuti: “Ukumuona kodi mayi uyu? Ngakhale kuti ndalowa m’nyumba yako, sunandipatse madzi+ otsukira mapazi anga. Koma mayi uyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuipukuta ndi tsitsi lake. 45  Iwe sunandipsompsone,+ koma chilowereni muno, mayiyu sanaleke kupsompsona mapazi anga mwachikondi. 46  Iwe sunathire mafuta m’mutu mwanga,+ koma mayiyu wapaka mapazi anga mafuta onunkhira. 47  Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuza kuti, machimo ake akhululukidwa,+ ngakhale kuti ndi ochuluka. N’chifukwa chake akusonyeza chikondi chochuluka. Koma amene wakhululukidwa machimo ochepa amasonyezanso chikondi chochepa.” 48  Kenako anauza mayiyo kuti: “Machimo ako akhululukidwa.”+ 49  Pamenepo onse amene anakhala naye patebulopo anayamba kudzifunsa mumtima mwawo kuti: “Kodi munthu ameneyu n’ngotani wokhozanso ngakhale kukhululukira machimo?”+ 50  Koma iye anauza mayiyo kuti: “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa.+ Pita mu mtendere.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Wobwerayo.”