Luka 24:1-53

24  Pa tsiku loyamba la mlungu, amayi aja analawirira m’mawa kwambiri kupita kumandako, atatenga zonunkhira zimene anakonza zija.+  Koma anapeza kuti mwala wagubuduzidwa pamanda achikumbutsowo,+  ndipo atalowa m’mandamo, mtembo wa Ambuye Yesu sanaupezemo.+  Atathedwa nzeru ndi zimenezi, anangoona amuna awiri ovala zovala zonyezimira ataima pambali pawo.+  Amayiwo anagwidwa ndi mantha ndi kuweramira pansi. Ndiyeno amunawo anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukufunafuna Munthu wamoyo pakati pa akufa?  [[Iye kuno kulibe, waukitsidwa.]]*+ Kumbukirani zimene anakuuzani pamene anali ku Galileya.+  Paja ananena kuti Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m’manja mwa anthu ochimwa ndi kupachikidwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.”+  Choncho anakumbukira mawu akewo.+  Pamenepo anachoka kumanda achikumbutsowo n’kubwerera kukanena zonsezi kwa ophunzira 11 aja ndi kwa ena onse.+ 10  Amayiwa anali Mariya Mmagadala, Jowana+ ndi Mariya mayi wa Yakobo. Komanso amayi+ ena onse amene anali nawo pamodzi anali kuuza atumwi zinthu zimenezi. 11  Koma kwa iwo, zimene anali kuwauzazo zinali zopanda pake ndipo sanawakhulupirire amayiwo.+ 12  [[Koma Petulo ananyamuka ndi kuthamangira kumanda achikumbutsoko, ndipo atasuzumira mkati, anangoona nsalu zokulungira mtembo zokha. Choncho anachoka ali wodabwa kwambiri ndi zimene zinachitikazo.]] 13  Koma tsiku lomweli, awiri a iwo anali pa ulendo wopita kumudzi wina wotchedwa Emau, pamtunda wa pafupifupi makilomita 11 kuchokera ku Yerusalemu. 14  Iwowa anali kukambirana zimene zinachitikazo.+ 15  Tsopano ali mkati mokambirana ndi kufunsana, Yesu anafika+ ndi kuyamba kuyenda nawo limodzi. 16  Koma m’maso mwawo sanathe kumuzindikira.+ 17  Iye anawafunsa kuti: “Kodi ndi nkhani zanji zimene mukukambirana mukuyenda pamsewu pano?” Iwo anangoima chilili ndi nkhope zachisoni. 18  Poyankha, mmodzi dzina lake Keleopa anamufunsa kuti: “Kodi iwe ukukhala wekhawekha m’Yerusalemu monga mlendo, moti sukudziwa zimene zachitika mmenemo m’masiku amenewa?” 19  Iye anawafunsa kuti: “Zinthu zotani?” Iwo anamuuza kuti: “Zinthu zokhudza Yesu Mnazareti,+ amene anali mneneri+ wamphamvu m’ntchito ndi m’mawu pamaso pa Mulungu ndi anthu onse. 20  Komanso zokhudza mmene ansembe athu aakulu ndi olamulira anamuperekera ku chiweruzo cha imfa ndi kumupachika.+ 21  Komatu ife tinali kuyembekezera kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli.+ Kuwonjezera pamenepo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni zinthu zimenezi. 22  Komanso amayi ena+ m’gulu lathu atidabwitsa kwambiri. Iwo analawirira m’mawa kwambiri kumanda achikumbutsoko, 23  koma mtembo wake sanaupeze. Anabwerako n’kumanena kuti aonanso masomphenya a angelo, amene awauza kuti iye ali ndi moyo. 24  Si zokhazo, enanso m’gulu lathu lomweli anapita kumanda achikumbutsoko,+ ndipo anapezadi kuti zili momwemo, mmene amayiwo ananenera, koma iyeyo sanamuone.” 25  Pamenepo iye anati: “Opanda nzeru inu ndi okayikakayika pa zonse zimene aneneri ananena!+ 26  Kodi sikunali kofunikira kuti Khristu amve zowawa+ zonsezi ndi kulowa mu ulemerero wake?”+ 27  Pamenepo anayamba kuwatanthauzira zinthu zokhudza iyeyo m’Malemba onse, kuyambira ndi Zolemba za Mose+ ndi za aneneri zonse.+ 28  Kenako anayandikira mudzi umene anali kupita, ndipo iye anachita ngati akupitirira ndi ulendo wake. 29  Koma iwo anamuumiriza kuti: “Tiyeni tikhalebe limodzi, chifukwa kunja kwayamba kuda ndipo tsiku latha kale.” Pamenepo analowa ndi kukakhala nawo. 30  Tsopano atakhala pansi n’kumadya nawo chakudya, anatenga mkate ndipo anaudalitsa, kuunyemanyema ndi kuwagawira.+ 31  Ataona izi, maso awo anatsegukiratu ndipo anamuzindikira, kenako iye anazimiririka.+ 32  Iwo anayamba kuuzana kuti: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumira pamene anali kulankhula nafe mumsewu, ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?” 33  Pa ola lomwelo ananyamuka ndi kubwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anakapeza ophunzira 11 aja komanso ena amene anali nawo, atasonkhana pamodzi. 34  Iwo anawauza kuti: “N’zoonadi, Ambuye wauka kwa akufa ndipo waonekera kwa Simoni!”+ 35  Apa nawonso anafotokoza zimene zinachitika pamsewu ndi mmene iwo anamuzindikirira pamene ananyemanyema mkate.+ 36  Akulankhula choncho Yesu anaimirira pakati pawo [[ndi kuwauza kuti: “Mtendere ukhale nanu.”]] 37  Koma iwo anaganiza kuti aona mzimu, ndipo anadzidzimuka kwambiri ndi kuchita mantha.+ 38  Koma iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuvutika maganizo? Bwanji mukukayikakayika m’mitima yanu? 39  Onani manja ndi mapazi angawa, mutsimikize kuti ndine ndithu. Ndikhudzeni muone,+ chifukwa mzimu ulibe mnofu ndi mafupa+ ngati anga amene mukuwaonawa.” 40  [[Pamene anali kunena zimenezi, anawaonetsa manja ndi mapazi ake.]] 41  Koma iwo, pokhalabe osakhulupirira+ chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, iye anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?”+ 42  Anamupatsa chidutswa cha nsomba yowotcha,+ 43  ndipo iye analandira ndi kudya+ onse akuona. 44  Ndiyeno anawauza kuti: “Pamene ndinali nanu limodzi+ ndinakuuzani mawu akuti, zonse zokhudza ine zolembedwa m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri+ ndi m’Masalimo+ ziyenera kukwaniritsidwa.” 45  Pamenepo anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.+ 46  Kenako anawauza kuti: “Mmene zachitikiramu ndi mmene zinalembedwera kuti Khristu adzazunzika ndi kuuka kwa akufa tsiku lachitatu,+ 47  ndipo pa maziko a dzina lake, m’mitundu yonse+ mudzalalikidwa za kulapa kuti machimo akhululukidwe.+ Kuyambira ku Yerusalemu+ 48  inu mudzakhala mboni+ za zimenezi. 49  Ndipo ine ndidzatumiza kwa inu chimene Atate wanga analonjeza. Koma inu mukhalebe mumzindawu kufikira mutalandira mphamvu zochokera kumwamba.”+ 50  Pamenepo anawatsogolera kupita nawo ku Betaniya. Kumeneko anakweza manja ake ndi kuwadalitsa.+ 51  Pamene anali kuwadalitsa choncho, analekana nawo, ndi kuyamba kukwera kumwamba.+ 52  Pamenepo anamugwadira ndi kubwerera ku Yerusalemu ali ndi chimwemwe chochuluka.+ 53  Nthawi zonse iwo anali m’kachisi kutamanda Mulungu.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Lu 23:34.