Luka 15:1-32
15 Tsopano okhometsa msonkho+ komanso anthu ochimwa,+ onse anali kubwera kwa iye kudzamumvetsera.
2 Afarisi ndi alembi ataona zimenezi anayamba kung’ung’udza kuti: “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa ndi kudya nawo limodzi.”+
3 Pamenepo anawauza fanizo ili:
4 “Ndani wa inu amene atakhala ndi nkhosa 100, imodzi n’kutayika, sangasiye nkhosa 99 zinazo m’chipululu, n’kupita kukafunafuna imodzi yotayikayo kufikira ataipeza?+
5 Ndipotu akaipeza amainyamula paphewa pake ndipo amakondwera.+
6 Akafika kunyumba amasonkhanitsa mabwenzi ake ndi anthu oyandikana naye n’kuwauza kuti, ‘Kondwerani nane limodzi, chifukwa ndapeza nkhosa yanga imene inatayika ija.’+
7 Ndithu ndikukuuzani, kumwamba kudzakhalanso chisangalalo chochuluka chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa+ kuposa cha anthu 99 olungama osafunika kulapa.+
8 “Kapena ndi mayi uti amene atakhala ndi ndalama zokwana madalakima 10, imodzi n’kumutayika, sangayatse nyale ndi kusesa m’nyumba n’kuifufuza mosamala mpaka ataipeza?
9 Ndipo akaipeza amasonkhanitsa amayi ena amene ndi mabwenzi ake ndi oyandikana nawo, n’kuwauza kuti, ‘Kondwerani nane limodzi, chifukwa ndapeza khobidi la dalakima linanditayika lija.’
10 Choncho ndikukuuzani, kumakhala chisangalalo chochuluka kwa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa.”+
11 Kenako ananena kuti: “Munthu wina anali ndi ana aamuna awiri.+
12 Wamng’ono pa awiriwo anapempha bambo ake kuti, ‘Bambo, mundipatsiretu cholowa changa pa chuma chanuchi.’+ Pamenepo bamboyo anagawa chuma chakecho+ kwa anawo.
13 Patangopita masiku owerengeka, mwana wamng’ono uja anasonkhanitsa zinthu zonse n’kupita kudziko lina lakutali. Kumeneko anasakaza chuma chake chonse mwa kulowerera m’makhalidwe oipa.+
14 Atawononga zonse, m’dziko lonselo munagwa njala yaikulu, ndipo iye anayamba kuvutika kwambiri.
15 Moti anapita kukadziphatika kwa nzika ina ya m’dzikolo, ndipo anam’tumiza kubusa kwake kuti azikaweta nkhumba.+
16 Iye anafika pomalakalaka chakudya cha nkhumbazo, ndipo palibe amene anali kum’patsa kanthu.+
17 “Nzeru zitam’bwerera, anati, ‘Komatu aganyu ambiri a bambo ali ndi chakudya chochuluka, koma ine kuno ndikufa ndi njala!
18 Basi ndinyamuka ndizipita+ kwa bambo anga ndikawauze kuti: “Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu.+
19 Sindilinso woyenera kutchedwa mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.”’
20 Choncho ananyamukadi n’kupita kwa bambo ake. Ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa chifundo. Pamenepo anamuthamangira ndi kumukumbatira ndipo anamupsompsona mwachikondi.
21 Ndiyeno mwanayo anauza bambo akewo kuti, ‘Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu.+ Sindilinso woyenera kutchedwa mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.’+
22 Koma bambowo anauza akapolo ake kuti, ‘Fulumirani, tengani mkanjo wabwino kwambiri uja mumuveke!+ Mumuvekenso mphete+ kudzanja lake ndi nsapato kumapazi kwake.
23 Mubweretse mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa,+ mumuphe ndipo tidye tisangalale.
24 Chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa koma tsopano wakhalanso ndi moyo,+ anatayika koma wapezeka.’ Chotero onse anayamba kukondwerera.
25 “Koma mwana wamkulu+ anali kumunda. Ndiyeno pobwerako, atayandikira kunyumbako, anamva anthu akuimba nyimbo ndi kuvina.
26 Choncho anaitana mmodzi wa antchito ndi kumufunsa chimene chinali kuchitika.
27 Iye anamuuza kuti, ‘Mng’ono wanu+ wabwera, ndipo bambo anu+ amuphera mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa, chifukwa amulandira ali bwinobwino.’
28 Pamenepo iye anakwiya kwambiri moti sanafune n’komwe kulowamo. Kenako bambo akewo anatuluka ndi kuyamba kumuchonderera.+
29 Poyankha iye anauza bambo akewo kuti, ‘Ine zaka zonsezi ndakhala ndikukugwirirani ntchito ngati kapolo, ndipo sindinaphwanyepo malamulo anu n’kamodzi komwe, koma simunandipatseko ngakhale kamwana ka mbuzi kuti ndisangalale ndi mabwenzi anga.+
30 Koma atangofika mwana wanuyu,+ amene anadya chuma chanu ndi mahule,+ mwamuphera mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa bwino.’+
31 Pamenepo bambowo anauza mwanayo kuti, ‘Mwana wanga, iwe wakhala nane nthawi zonse, ndipo zinthu zonse zimene ine ndili nazo ndi zako.+
32 Komatu sitikanachitira mwina, tinayeneradi kusangalala ndi kukondwera, chifukwa m’bale wakoyu anali wakufa koma tsopano ali ndi moyo, anali wotayika koma tsopano wapezeka.’”+