Luka 4:1-44

4  Tsopano Yesu anachoka ku Yorodano atadzazidwa ndi mzimu woyera. Ndipo mzimuwo unamutenga ndi kumuyendetsa uku ndi uku m’chipululu+  kwa masiku 40,+ kumene anali kuyesedwa+ ndi Mdyerekezi. Komanso m’masiku amenewo sanali kudya chilichonse, choncho masikuwo atatha, anamva njala.  Mdyerekezi ataona zimenezi anamuuza kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu kuti usanduke mkate.”  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha.’”+  Choncho anakwera naye pamwamba ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’kanthawi kochepa.  Ndiyeno Mdyerekezi anamuuza kuti: “Ndikupatsani ulamuliro+ pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.+  Chotero ngati inuyo mungandiweramireko+ kamodzi kokha, ulamuliro wonsewu udzakhala wanu.”  Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako+ ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+  Kenako anamutengera ku Yerusalemu, ndipo anamukweza pamwamba pa khoma+ la mpanda wa kachisi n’kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi kuchokera pano.+ 10  Pajatu Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake za inu, kuti akutetezeni.’+ 11  Choncho, ‘Adzakunyamulani m’manja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala uliwonse.’”+ 12  Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Pajatu Malemba amati, ‘Usamuyese, Yehova Mulungu wako.’”+ 13  Choncho Mdyerekeziyo atamaliza mayesero onsewo, anamusiya kufikira nthawi ina yabwino.+ 14  Tsopano Yesu anabwerera ku Galileya+ atadzazidwa ndi mphamvu ya mzimu. Ndipo mbiri yake yabwino inamveka ponseponse m’madera onse ozungulira.+ 15  Komanso, anayamba kuphunzitsa m’masunagoge awo, ndipo anthu onse anali kumulemekeza.+ 16  Kenako anabwera ku Nazareti,+ kumene analeredwa. Malinga ndi chizolowezi chake pa tsiku la sabata, analowa m’sunagoge,+ ndi kuimirira kuti awerenge Malemba. 17  Pamenepo anamupatsa mpukutu wa mneneri Yesaya. Iye anafunyulula mpukutuwo ndi kupeza pamene panalembedwa mawu akuti: 18  “Mzimu wa Yehova+ uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu,+ 19  ndi kudzalalikira chaka chovomerezeka kwa Yehova.”+ 20  Atatero anapinda mpukutuwo, n’kuubwezera kwa wotumikira mmenemo ndi kukhala pansi. Maso onse m’sunagogemo anali pa iye kumuyang’anitsitsa. 21  Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”+ 22  Pamenepo onse anayamba kumutamanda ndi kudabwa ndi mawu ogwira mtima+ otuluka pakamwa pake, mwakuti anali kunena kuti: “Kodi iyeyu si mwana wa Yosefe?”+ 23  Zitatero iye anawauza kuti: “Mosakayikira mawu akuti, ‘Wochiritsa+ iwe, dzichiritse wekha,’ mudzawagwiritsa ntchito pa ine. Mudzanena kuti: ‘Tinamva kuti unachita zinthu zambiri ku Kaperenao.+ Zinthu zimenezo+ uzichitenso kwanu kuno.’”+ 24  Iye ananenanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe mneneri amene amalandiridwa kwawo. 25  Mwachitsanzo, ndikukuuzani ndithu kuti, Munali akazi ambiri amasiye mu Isiraeli m’masiku a Eliya, pamene kumwamba kunatsekedwa zaka zitatu ndi miyezi 6, mwakuti m’dziko lonse munagwa njala yaikulu.+ 26  Koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa akazi amenewo. M’malomwake anatumizidwa kwa mkazi wamasiye ku Zarefati+ m’dziko la Sidoni. 27  Ndiponso, munali akhate ambiri mu Isiraeli m’nthawi ya mneneri Elisa. Komabe palibe aliyense wa iwo amene anayeretsedwa, koma Namani, mwamuna wa ku Siriya.”+ 28  Tsopano onse amene anali kumvetsera mawu amenewa m’sunagogemo anakwiya kwambiri.+ 29  Iwo ananyamuka ndipo mwamsangamsanga anamutulutsira kunja kwa mzinda. Kenako anapita naye pamwamba pa phiri limene anamangapo mzinda wawo, kuti akam’ponye kuphedi.+ 30  Koma iye anangodutsa pakati pawo n’kumapita.+ 31  Choncho anapita ku Kaperenao,+ mzinda wa ku Galileya. Ndipo anali kuwaphunzitsa pa sabata. 32  Kumeneko anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake,+ chifukwa anali kulankhula ndi mphamvu za ulamuliro.+ 33  Tsopano m’sunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu,+ chiwanda chonyansa, ndipo anafuula ndi mawu amphamvu kuti: 34  “Tili nanu chiyani,+ Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani+ bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu.”+ 35  Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye.” Choncho chiwandacho chinagwetsa munthuyo pansi pakati pawo, kenako chinatuluka mwa iye osamuvulaza.+ 36  Ataona zimenezi, onse anadabwa kwambiri, ndipo anayamba kukambirana kuti: “Kulankhula kumeneku ndi kwa mtundu wanji anthuni? Taonani! Akutha kudzudzula mizimu yonyansa mwa ulamuliro ndi mphamvu, ndipo mizimuyo ikutulukadi.”+ 37  Choncho mbiri yake inapitiriza kufalikira ponseponse m’midzi yonse yozungulira.+ 38  Atatuluka m’sunagogemo, anakalowa m’nyumba ya Simoni. Kumeneko apongozi aakazi a Simoni anali kudwala malungo* aakulu, choncho anam’pempha kuti apite kumeneko chifukwa cha mayiwo.+ 39  Chotero anaima pamene mayiwo anagona ndi kuwachiritsa,+ ndipo malungowo anatheratu. Nthawi yomweyo mayiwo anadzuka n’kuyamba kuwatumikira.+ 40  Koma pamene dzuwa linali kulowa, onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweretsa kwa iye. Ndipo iye anawachiritsa mwa kuika manja ake pa aliyense.+ 41  Ziwanda nazonso zinatuluka mwa anthu ambiri.+ Zinali kufuula kuti: “Inu ndinu Mwana+ wa Mulungu.” Koma iye anali kudzudzula ziwandazo, ndipo sanali kuzilola kuti zilankhule,+ chifukwa zinali kudziwa kuti iye+ ndi Khristu.+ 42  Kutacha, anatuluka ndi kupita kumalo kopanda anthu.+ Koma khamu la anthu linayamba kumufunafuna mpaka linafika kumene iye anali, ndipo anthuwo anayesa kumuletsa kuti asawasiye. 43  Koma iye anawauza kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.”+ 44  Choncho anapita n’kumalalikira m’masunagoge a mu Yudeya.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.
Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”