Luka 22:1-71
22 Tsopano chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa, chotchedwanso kuti Pasika,+ chinali kuyandikira.
2 Komanso ansembe aakulu ndi alembi anali kufunafuna njira yabwino yophera Yesu,+ pakuti anali kuopa anthu.+
3 Koma Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikariyoti, mmodzi wa ophunzira 12 aja.+
4 Iye anapita kukakambirana ndi ansembe aakulu ndi oyang’anira kachisi za njira yabwino yomuperekera kwa iwo.+
5 Iwo anakondwa, ndipo anagwirizana kuti amupatse ndalama zasiliva.+
6 Choncho iye anavomereza, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke kwa iwo popanda khamu la anthu pafupi.+
7 Tsopano tsiku la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa linafika, tsiku loyenera kupha nyama yoperekera nsembe ya pasika.+
8 Yesu anatumiza Petulo ndi Yohane kuti: “Pitani mukatikonzere+ pasika kuti tidye.”
9 Iwo anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti?”
10 Iye anawayankha kuti:+ “Mukalowa mumzinda, mwamuna wina wosenza mtsuko wa madzi akumana nanu. Mukamutsatire kunyumba imene akalowe.+
11 Ndipo mukauze mwininyumba imeneyo kuti, ‘Mphunzitsi akufunsa kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti, mmene ine ndidyeremo pasika pamodzi ndi ophunzira anga?”’+
12 Ndiyeno munthu ameneyo akakusonyezani chipinda chachikulu cham’mwamba chokonzedwa bwino. Mukakonzere mmenemo.”+
13 Choncho ananyamuka ndi kupita. Kumeneko zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo anakonza pasika kumeneko.+
14 Nthawi itakwana, anakhala patebulo la chakudya, atumwi akenso anali naye limodzi.+
15 Ndiyeno anawauza kuti: “Ndinali wofunitsitsa kudya pasika uyu limodzi ndi inu ndisanalowe m’masautso.
16 Pakuti ndikukuuzani, sindidzadyanso pasika kufikira zonse zimene pasikayu akuimira zitakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.”+
17 Ndiyeno analandira kapu+ ndi kuyamika, kenako anati: “Landirani kapu iyi, nonse imwani mopatsirana.
18 Ndithu ndikukuuzani, Kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utafika.”+
19 Kenako anatenga mkate.+ Atayamika anaunyemanyema n’kuwapatsa, ndipo anati: “Mkate uwu ukuimira thupi langa+ limene likuperekedwa chifukwa cha inu.+ Muzichita zimenezi pondikumbukira.”+
20 Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu+ atadya chakudya chamadzulocho. Iye anati: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano+ pamaziko a magazi anga,+ amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.+
21 “Koma taonani! Wondipereka+ ndili naye limodzi patebulo pompano.+
22 Chifukwa Mwana wa munthu akuchoka malinga n’zimene zinanenedweratu.+ Koma, tsoka kwa munthu amene akumupereka!”+
23 Choncho anayamba kufunsana ndi kukambirana pakati pawo za amene anakonza chiwembu chimenecho.+
24 Komanso, panabuka mkangano woopsa pakati pawo za amene anali kuoneka wamkulu kwambiri.+
25 Koma Yesu anawauza kuti: “Mafumu a mitundu ya anthu amachita ulamuliro pa anthu awo, ndipo amene ali ndi mphamvu pa anthuwo amatchedwa Opereka zabwino.+
26 Inu musakhale otero.+ Koma amene ali wamkulu kwambiri pa nonsenu akhale ngati wamng’ono kwambiri pa nonsenu,+ ndipo amene ali mtsogoleri akhale wotumikira.+
27 Kodi wamkulu ndani, amene akudya patebulo kapena amene akutumikira? Si amene akudya patebulo kodi? Koma ine ndili pakati panu monga wotumikira.+
28 “Komabe, inu mwakhalabe ndi ine+ m’mayesero anga.+
29 Choncho ndikuchita nanu pangano,+ mmene Atate wanga wachitira pangano la ufumu ndi ine,+
30 kuti mukadye+ ndi kumwa patebulo langa mu ufumu wanga,+ ndipo mukakhala m’mipando yachifumu+ kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.
31 “Simoni, Simoni! Ndithu Satana+ akufuna anthu inu, kuti akupeteni ngati tirigu.+
32 Koma ine ndakupempherera+ iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe. Chotero iwenso, ukabwerera, ukalimbikitse+ abale ako.”
33 Pamenepo iye anauza Yesu kuti: “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu limodzi kundende kapena kufa nanu limodzi.”+
34 Koma iye anati: “Ndikukuuza iwe Petulo, Tambala asanalire lero, undikana katatu kuti sundidziwa.”+
35 Yesu anauzanso ophunzirawo kuti: “Pamene ndinakutumizani+ opanda chikwama cha ndalama, thumba la chakudya, kapena nsapato, munasowa kanthu kodi?” Iwo anati: “Ayi!”
36 Pamenepo anawauza kuti: “Koma tsopano amene ali ndi chikwama cha ndalama achitenge, chimodzimodzinso thumba la chakudya. Ndipo amene alibe lupanga agulitse malaya ake akunja n’kugula lupanga.
37 Pakuti ndikukuuzani kuti mawu olembedwawa ayenera kukwaniritsidwa mwa ine. Mawuwo ndi akuti, ‘Ndipo anamutenga ngati mmodzi wa anthu osamvera malamulo.’+ Pakuti chimene chikukhudza ine chikukwaniritsidwa.”+
38 Pamenepo iwo anati: “Ambuye, onani! Tili ndi malupanga awiri awa.” Iye anawauza kuti: “Amenewa ndi okwanira.”
39 Atachoka kumeneko anapita kuphiri la Maolivi monga anali kuchitira nthawi zonse. Ophunzira nawonso anamutsatira.+
40 Atafika pamalowo anauza ophunzirawo kuti: “Pempherani kosalekeza, kuti musalowe m’mayesero.”+
41 Iye analekana nawo ndi kuyenda kamtunda, kutalika kwake ngati pamene pangagwere mwala munthu atauponya. Kumeneko anagwada ndi kuyamba kupemphera,
42 kuti: “Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni kapu iyi. Komatu chifuniro chanu chichitike,+ osati changa.”+
43 Pamenepo mngelo wochokera kumwamba anaonekera kwa iye ndi kumulimbikitsa.+
44 Koma atazunzika koopsa mumtima mwake, anapitiriza kupemphera ndi mtima wonse+ ndipo thukuta lake linaoneka ngati madontho amagazi amene akugwera pansi.+
45 Kenako ananyamuka pamene anali kupemphererapo n’kupita kwa ophunzira aja. Koma anawapeza atagona chifukwa cha chisoni.+
46 Iye anawauza kuti: “Mukugona chifukwa chiyani? Dzukani, pitirizani kupemphera kuti musalowe m’mayesero.”+
47 Mawu adakali m’kamwa, panafika khamu la anthu, limodzi ndi Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, akuwatsogolera.+ Ndiyeno Yudasi anapita pamene panali Yesu kukamupsompsona.+
48 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa munthu mwa kupsompsona?”+
49 Anthu amene anali naye pafupi ataona zimene zinali kuchitika, anati: “Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?”+
50 Wina wa iwo anatemadi kapolo wa mkulu wa ansembe ndi kuduliratu khutu lake lakumanja.+
51 Koma Yesu anati: “Basi! Lekani zimenezi.” Ndipo anagwira khutu lija ndi kumuchiritsa.+
52 Yesu pamenepo anafunsa ansembe aakulu, oyang’anira kachisi ndi akulu amene anam’londola kumeneko, kuti: “Bwanji mwabwera ndi malupanga ndi zibonga ngati mukukalimbana ndi wachifwamba?+
53 Tsiku ndi tsiku ndinali nanu m’kachisi+ koma simunandigwire.+ Koma ino tsopano ndi nthawi yanu+ komanso nthawi ya ulamuliro+ wa mdima.”+
54 Pamenepo anamugwira ndi kumutenga,+ ndipo anakamulowetsa m’nyumba ya mkulu wa ansembe.+ Koma Petulo anali kuwatsatira chapatali.+
55 Atasonkha moto mkati mwa bwalo ndi kukhala pansi onse pamodzi, Petulo nayenso anakhala nawo pamenepo.+
56 Koma mayi wina wantchito anamuona atakhala pafupi ndi moto wowala ndipo anamuyang’ana ndi kunena kuti: “Bambo awanso anali naye limodzi.”+
57 Koma iye anakana+ kuti: “Mayi iwe, ameneyu ine sindimudziwa ayi.”+
58 Patapita kanthawi pang’ono, munthu wina anamuona ndi kunena kuti: “Iwenso uli m’gulu la ophunzira ake.” Koma Petulo anati: “Munthu iwe, si ine ayi.”+
59 Patapita pafupifupi ola lathunthu, munthu winanso anayamba kunena motsimikiza kuti: “Ndithu sindikukayika, munthu uyunso anali naye limodzi, ndipo iyeyu ndi Mgalileya!”+
60 Koma Petulo anati: “Munthu iwe, ine sindikudziwa zimene ukunena.” Nthawi yomweyo, mawu ali m’kamwa, tambala analira.+
61 Pamenepo Ambuye anacheuka ndi kuyang’ana Petulo, ndipo Petulo anakumbukira mawu amene Ambuye anamuuza aja, akuti: “Tambala asanalire lero, undikana katatu.”+
62 Ndipo anatuluka panja ndi kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.+
63 Tsopano amuna amene anagwira Yesu aja anayamba kumuchitira zachipongwe,+ ndi kumumenya.+
64 Anali kumuphimba kumaso ndi kumufunsa kuti: “Losera. Wakumenya ndani?”+
65 Ndipo anapitiriza kunena zambiri zomunyoza.+
66 Kenako kutacha, bungwe la akulu, kuphatikizapo ansembe aakulu komanso alembi, anasonkhana pamodzi,+ ndipo anamutengera kuholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda.* Kumeneko iwo anati:+
67 “Tiuze ngati ndiwe Khristu.”+ Koma iye anawayankha kuti: “Ngakhale ndikuuzeni, simukhulupirira.+
68 Komanso nditakufunsani, simungathe n’komwe kuyankha.+
69 Koma kuyambira tsopano Mwana wa munthu+ adzakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu la Mulungu.”+
70 Atanena izi onse anati: “Kodi ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anawayankha kuti: “Inunso mukunena nokha+ kuti ndine amene.”
71 Iwo anati: “Tifuniranjinso umboni wina?+ Apatu tadzimvera tokha kuchokera pakamwa pake.”+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”