Luka 10:1-42

10  Pambuyo pake, Ambuye anasankha anthu ena 70+ ndi kuwatumiza awiriawiri+ kuti atsogole kupita mumzinda ndi malo alionse kumene iye adzafikeko.  Kenako anayamba kuwauza kuti: “Zokolola+ n’zochulukadi, koma antchito+ ndi ochepa. Choncho pemphani+ Mwini zokololazo kuti atumize antchito+ okam’kololera.  Pitani. Inetu ndikukutumizani monga nkhosa+ pakati pa mimbulu.  Musatenge chikwama cha ndalama, thumba la chakudya,+ kapena nsapato. Ndipo musamachedwe mukamapereka moni panjira.+  Mukafika panyumba, choyamba muzinena kuti, ‘Mtendere ukhale panyumba pano.’+  Ndipo ngati pakhomopo pali munthu wokonda mtendere, mtendere wanu udzakhala pa iye.+ Koma ngati palibe, udzabwerera kwa inu.+  Choncho khalani m’nyumba yamtendereyo.+ Muzidya ndi kumwa zimene angakupatseni,+ chifukwa wantchito ayenera kulandira malipiro ake.+ Musamachoke kumene mwafikirako n’kupita kunyumba zina.+  “Komanso mukalowa mumzinda ndipo iwo n’kukulandirani, muzidya zimene akukonzerani.  Muzichiritsanso+ odwala mmenemo ndipo muziwauza kuti, ‘Ufumu wa Mulungu+ wakuyandikirani.’ 10  Koma mukalowa mumzinda ndipo sanakulandireni,+ muzichokamo ndi kupita m’misewu yawo n’kunena kuti, 11  ‘Ngakhale fumbi la mumzinda wanu uno, limene lamamatira kumapazi kwathu, tikukusansirani.+ Komabe, kumbukirani kuti, ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 12  Ndithu ndikukuuzani, chilango cha Sodomu+ pa tsiku limenelo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha mzinda umenewo. 13  “Tsoka iwe Korazini!+ Tsoka iwe Betsaida!+ Chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika kumeneko zikanachitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu kumeneko akanalapa kalekale atavala ziguduli n’kukhala paphulusa.+ 14  Choncho chilango cha Turo ndi Sidoni pa chiweruzo chidzakhala chocheperako kusiyana ndi chanu.+ 15  Iwenso Kaperenao, kodi udzakwezedwa kumwamba kapena?+ Ku Manda*+ n’kumene udzatsikira ndithu! 16  “Amene akukumverani,+ akumveranso ine. Ndipo amene akunyalanyaza+ inu akunyalanyazanso ine. Ndipotu amene akunyalanyaza ine akunyalanyazanso amene anandituma.” 17  Tsopano anthu okwana 70 aja anabwerera ali osangalala. Iwo anauza Yesu kuti: “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera+ pamene tinagwiritsa ntchito dzina lanu.” 18  Ndiyeno iye anawauza kuti: “Ndinayamba kuona Satana atagwa+ kale ngati mphezi kuchokera kumwamba. 19  Taonani! Inetu ndakupatsani ulamuliro kuti muzitha kupondaponda njoka+ ndi zinkhanira.+ Komanso ndakupatsani ulamuliro pa mphamvu zonse za mdani,+ ndipo palibe chimene chidzakuvulazeni. 20  Komano, musakondwere ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina+ anu alembedwa kumwamba.” 21  Nthawi yomweyo Yesu anakondwera+ kwambiri mwa mzimu woyera n’kunena kuti: “Atate ndikukutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa zinthu izi mwazibisa kwa anzeru+ ndi ozama m’maphunziro, koma mwaziulula kwa tiana. Inde Atate, chifukwa inu munakonda kuti zinthu zikhale chonchi. 22  Atate wanga wapereka+ zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso Atatewo+ palibe amene akuwadziwa bwino koma Mwana+ yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululira za Atatewo.” 23  Ndiyeno Yesu ndi ophunzira akewo ali kwaokha, anawauza kuti: “Anthu amene maso awo amaona zimene inu mukuonazi ndi odala.+ 24  Pakuti ndikukuuzani, Aneneri ndi mafumu ambiri analakalaka kuona+ zimene mukuzionazi, koma sanazione. Analakalaka kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.” 25  Kenako munthu wina wodziwa Chilamulo+ anaimirira kuti amuyese. Iye anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, ndizichita chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 26  Yesu anamufunsa kuti: “Kodi m’Chilamulo analembamo chiyani?+ Umawerengamo zotani?” 27  Iye anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, mphamvu zako zonse, ndi maganizo ako onse.’+ Komanso, ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+ 28  Pamenepo anamuuza kuti: “Wayankha molondola. ‘Uzichita zimenezo, ndipo udzapeza moyo.’”+ 29  Koma pofuna kudzionetsa kuti ndi wolungama, munthuyo anafunsa Yesu kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndani kwenikweni?”+ 30  Poyankha Yesu anati: “Munthu wina anali kuyenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko. Ndipo anakumana ndi achifwamba amene anam’vula ndi kumumenya koopsa. Kenako anapita, n’kumusiya ali pafupi kufa. 31  Ndiye zinangochitika kuti wansembe wina anali kuyenda mumsewu womwewo, koma atamuona, anangomulambalala.+ 32  Chimodzimodzinso Mlevi, atadutsa msewuwo n’kufika pamalo amenewo ndi kumuona, anangomulambalala.+ 33  Koma panafika Msamariya+ wina amene anali kudutsanso msewu umenewo. Ndipo atamuona, anagwidwa chifundo. 34  Choncho anam’yandikira ndi kumanga mabala ake. Anathira mafuta ndi vinyo m’mabalamo.+ Kenako anam’kweza pachiweto chake n’kupita naye kunyumba ya alendo kumene anam’samalira. 35  Tsiku lotsatira anatulutsa madinari awiri ndi kupereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Ndiyeno anamuuza kuti, ‘Musamalireni bwino, mukawononga ndalama zina zowonjezera, ndidzakubwezerani ndikadzabwera.’ 36  Ndani mwa atatuwa amene iweyo ukuona kuti anakonda+ munthu amene anakumana ndi achifwambayu?” 37  Iye anayankha kuti: “Ndi amene anam’chitira chifundoyo.”+ Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Pita, iwenso uzikachita zomwezo.”+ 38  Tsopano pamene anali kuyenda, analowa m’mudzi wina. Kumeneko mayi wina dzina lake Marita+ anamulandira m’nyumba mwake monga mlendo. 39  Mayi ameneyu anali ndi m’bale wake dzina lake Mariya. Iyeyu anakhala pansi pafupi+ ndi Ambuye n’kumamvetsera mawu awo. 40  Koma Marita anatanganidwa+ ndi ntchito zochuluka. Choncho anafika pafupi n’kunena kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti m’bale wangayu wandilekerera ndekha ntchito?+ Tamuuzani kuti andithandize.” 41  Poyankha Ambuye anamuuza kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa+ ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri.+ 42  Komatu zinthu zofunika kwenikweni n’zochepa+ chabe, mwinanso n’chimodzi chokha basi. Kumbali yake, Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri,+ ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.”

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 5.