Luka 1:1-80

1  Ambiri anayesetsa kulemba nkhani yofotokoza zochitika zenizeni+ zimene ife tonse timazikhulupirira.  Iwo analemba ndendende mmene anatiuzira anthu amene anakhala mboni zoona ndi maso+ ndi atumiki a uthengawo+ kuchokera pa chiyambi.+  Inenso, popeza kuti ndafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi, ndafunitsitsa kuti ndikulembereni mwatsatanetsatane,+ inu wolemekezeka+ koposa, a Teofilo.+  Ndachita izi kuti mudziwe bwinobwino kuti zinthu zimene anakuphunzitsani ndi mawu apakamwa n’zodalirika.+  M’masiku a Herode,*+ mfumu ya Yudeya, kunali wansembe wina wotchedwa Zekariya wa m’gulu la ansembe lotchedwa Abiya.+ Iyeyu anali ndi mkazi wochokera mwa ana aakazi a Aroni,+ dzina lake Elizabeti.  Onse awiriwo anali olungama+ pamaso pa Mulungu chifukwa choyenda mokhulupirika,+ mogwirizana ndi malamulo onse+ komanso zofunika za m’chilamulo+ cha Yehova.+  Koma iwo analibe mwana, chifukwa Elizabeti anali wosabereka,+ ndipo onse awiri anali okalamba.  Tsopano pamene Zekariya anali kugwira ntchito monga wansembe pamaso pa Mulungu, kuimira gawo lake,+  malinga ndi mwambo wa ansembe, inali nthawi yake yakuti azilowa m’nyumba yopatulika ya Yehova,+ n’kupereka nsembe zofukiza.+ 10  Khamu lonse la anthu linali kupemphera panja, pa ola lopereka nsembe zofukizalo.+ 11  Mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye, ataimirira kudzanja lamanja la guwa lansembe zofukiza.+ 12  Tsopano Zekariya anavutika mumtima ataona zimenezo, ndipo anagwidwa ndi mantha.+ 13  Koma mngeloyo anamuuza kuti: “Usachite mantha Zekariya, chifukwa pembedzero lako lamveka ndithu.+ Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera mwana wamwamuna, ndipo udzamutche Yohane.+ 14  Udzakondwa ndi kusangalala kwambiri, ndipo ambiri adzasangalala+ ndi kubadwa kwake 15  chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova.+ Koma asadzamwe vinyo ngakhale pang’ono+ kapena chakumwa chaukali chilichonse. Ndipo adzadzazidwa ndi mzimu woyera kuyambira ali m’mimba mwa mayi ake.+ 16  Iye adzatembenuza ana ambiri a Isiraeli kuti abwerere kwa Yehova+ Mulungu wawo. 17  Komanso, adzatsogola monga kalambulabwalo wa Mulungu ali ndi mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya.+ Iye adzatembenuza mitima+ ya abambo kuti ikhale ngati ya ana, ndipo osamvera adzawatembenuzira ku nzeru yeniyeni ya anthu olungama. Adzachita izi kuti asonkhanitsire Yehova+ anthu okonzedwa.”+ 18  Ndiyeno Zekariya anafunsa mngeloyo kuti: “Nditsimikiza bwanji zimenezi? Inetu ndine wokalamba,+ mkazi wanganso zaka zake n’zambiri.” 19  Poyankha mngeloyo anamuuza kuti: “Ine ndine Gabirieli,+ amene ndimaima pamaso pa Mulungu, ndipo wandituma kudzalankhula+ nawe ndi kudzalengeza uthenga wabwino wa zinthu izi kwa iwe. 20  Imva tsopano! Udzakhala chete,+ osatha kulankhula mpaka tsiku limene zimenezi zidzachitike. Izi zidzachitika chifukwa sunakhulupirire mawu anga amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoikidwiratu.” 21  Pa nthawiyi n’kuti anthu akuyembekezerabe Zekariya,+ ndipo anayamba kudabwa ndi kuchedwa kwake m’nyumba yopatulikayo. 22  Koma pamene anatuluka sanathenso kulankhula nawo. Pamenepo iwo anazindikira kuti waona masomphenya+ a chinachake m’nyumba yopatulikayo. Choncho anayamba kulankhula nawo ndi manja okhaokha, osathanso kutulutsa mawu. 23  Tsopano masiku ake otumikira atatha,+ anapita kwawo. 24  Masiku amenewa atadutsa, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pakati,+ ndipo anabindikira miyezi isanu. Iye anali kunena kuti: 25  “Izitu n’zimene Yehova wandichitira masiku ano pamene wandicheukira kuti andichotsere chitonzo pamaso pa anthu.”+ 26  M’mwezi wake wa 6, Mulungu anatumiza mngelo Gabirieli+ kumzinda wina wa Galileya, wotchedwa Nazareti. 27  Anamutumiza kwa namwali amene mwamuna wina wotchedwa Yosefe, wa m’nyumba ya Davide, anamulonjeza kuti adzamukwatira. Namwali+ ameneyu dzina lake anali Mariya.+ 28  Mngelo uja atafika kwa namwaliyu anati: “Mtendere ukhale nawe,+ iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova+ ali nawe.”+ 29  Koma mawu amenewa anam’dabwitsa kwambiri, moti anayamba kusinkhasinkha za moni wamtundu woterewu. 30  Pamenepo mngeloyo anamuuza kuti: “Usaope Mariya, pakuti Mulungu wakukomera mtima.+ 31  Tsopano mvetsera! Udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna.+ Udzam’patse dzina lakuti Yesu.+ 32  Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.+ Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu+ wa Davide atate wake.+ 33  Iye adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti ufumu wake sudzatha konse.”+ 34  Koma Mariya anafunsa mngeloyo kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji, pakuti sindinagonepo+ ndi mwamuna?” 35  Poyankha mngeloyo anauza Mariya kuti: “Mzimu woyera+ udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera,+ Mwana wa Mulungu.+ 36  Ndipotu m’bale wako Elizabeti, amene anthu amamunena kuti mkazi wosabereka,+ nayenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake, ndipo uno ndi mwezi wa 6. 37  Izi zachitika chifukwa zimene Mulungu wanena, sizilephereka.”+ 38  Ndiyeno Mariya anati: “Ndinetu kapolo wa Yehova!+ Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.” Pamenepo mngeloyo anamusiya. 39  Choncho Mariya ananyamuka m’masiku amenewo n’kupita mofulumira kudera lamapiri, kumzinda wina m’dziko la fuko la Yuda. 40  Kumeneko analowa m’nyumba ya Zekariya ndi kupereka moni kwa Elizabeti. 41  Tsopano Elizabeti atamva moni wa Mariya, khanda limene linali m’mimba mwakemo linadumpha. Ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera. 42  Choncho anafuula ndi mawu amphamvu, kuti: “Ndiwe wodalitsidwa mwa akazi onse. N’chodalitsidwanso+ chipatso cha mimba yako! 43  Koma zatheka bwanji kuti dalitso limeneli lindigwere? Zatheka bwanji kuti mayi wa Mbuye wanga+ abwere kwa ine? 44  Waona nanga! Pamenetu mawu a moni wako alowa m’makutu mwangamu, ndithu khanda ladumpha mosangalala kwambiri m’mimba mwangamu.+ 45  Ndipotu ndiwe wodala pakuti unakhulupirira, chifukwa zonse zimene unauzidwa zochokera kwa Yehova+ zidzachitika.”+ 46  Pamenepo Mariya anati: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova.+ 47  Ndipo mzimu wanga sungaleke kusefukira+ ndi chimwemwe mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga.+ 48  Chifukwa waona malo otsika a kapolo wake.+ Ndipo taonani! kuyambira tsopano mibadwo yonse idzanditcha wodala.+ 49  Chifukwa Wamphamvuyo wandichitira zazikulu, ndipo dzina lake ndi loyera.+ 50  Chifundo chake chakhala pa amene amamuopa ku mibadwomibadwo.+ 51  Wachita zamphamvu ndi dzanja lake,+ wabalalitsira kutali odzikweza m’zolinga za mitima yawo.+ 52  Watsitsa anthu amphamvu+ zawo pamipando yachifumu, ndipo wakweza anthu wamba.+ 53  Wakhutitsa anthu anjala ndi zinthu zabwino,+ amene anali ndi chuma wawapitikitsa chimanjamanja.+ 54  Iye wathandiza mtumiki wake Isiraeli.+ Wachita zimenezi posonyeza kuti akukumbukira lonjezo lake lakuti adzasonyeza chifundo kwamuyaya,+ 55  monga momwe anauzira makolo athu akale, Abulahamu ndi mbewu yake.”+ 56  Choncho Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu, kenako anabwerera kwawo. 57  Tsopano nthawi inakwana yakuti Elizabeti achire, ndipo anabereka mwana wamwamuna. 58  Anthu oyandikana naye ndi abale ake anamva kuti Yehova anam’chitira chifundo chachikulu,+ ndipo anayamba kukondwera+ naye pamodzi. 59  Pa tsiku la 8, iwo anabwera kudzachita mdulidwe wa mwanayo,+ komanso anafuna kum’patsa dzina la bambo ake, lakuti Zekariya. 60  Koma mayi ake anayankha kuti: “Limenelo iyayi! Dzina lake akhala Yohane.” 61  Pamenepo iwo anamuuza kuti: “Palibe wachibale wako aliyense wotchedwa ndi dzina limenelo.” 62  Ndiyeno anafunsa bambo wake, mwa kulankhula ndi manja, za dzina limene akufuna kuti am’tchule mwanayo. 63  Choncho iye anapempha cholembapo chathabwa ndipo analemba kuti: “Dzina lake ndi Yohane.”+ Pamenepo onse anadabwa. 64  Nthawi yomweyo pakamwa pake panatseguka,+ lilime lake linamasuka, ndipo anayamba kulankhula ndi kutamanda Mulungu. 65  Pamenepo onse okhala moyandikana nawo anagwidwa mantha. Ndipo nkhani imeneyi inali m’kamwam’kamwa m’madera onse a kumapiri a Yudeya. 66  Mwakuti onse amene anamva anazisunga m’mitima mwawo ndi kuzisinkhasinkha.+ Iwo anali kunena kuti: “Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani kwenikweni?” Pakuti dzanja+ la Yehova linalidi pa iye. 67  Pamenepo bambo ake Zekariya anadzazidwa ndi mzimu woyera,+ ndipo ananenera,+ kuti: 68  “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ chifukwa wacheukira anthu ake+ ndi kuwapatsa chipulumutso.+ 69  Iye watikwezera ife nyanga*+ yachipulumutso m’nyumba ya mtumiki wake Davide, 70  monga mmene iye ananenera kudzera pakamwa pa aneneri ake oyera akale,+ 71  za kutipulumutsa kwa adani athu ndiponso m’manja mwa onse odana nafe.+ 72  Kuchitira chifundo makolo athu akale ndi kukumbukira pangano lake loyera,+ 73  lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu lakale Abulahamu,+ 74  kuti pambuyo pakuti tapulumutsidwa m’manja mwa adani,+ atipatse mwayi wochita utumiki wopatulika kwa iye+ mopanda mantha, 75  mokhulupirika ndi mwachilungamo pamaso pake masiku athu onse.+ 76  Koma kunena za iwe, mwanawe, udzatchedwa mneneri wa Wam’mwambamwamba, pakuti udzatsogola pamaso pa Yehova kuti ukakonzeretu njira zake.+ 77  Kukadziwitsa anthu ake za chipulumutso pokhululukidwa machimo awo,+ 78  chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu. Ndi chifundo chimenechi, kuwala kwa m’mawa+ kudzatifikira kuchokera kumwamba,+ 79  ndipo kudzaunikira amene akhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa,+ ndi kutsogolera bwinobwino mapazi athu panjira yamtendere.” 80  Choncho mwana uja anakulirakulira+ ndipo anali kulimba mwauzimu. Iye anali kukhala m’zipululu mpaka tsiku lakuti adzionetsere poyera kwa Isiraeli.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Mt 2:1.
Kapena kuti “mpulumutsi wamphamvu.” Kawirikawiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti nyanga monga chizindikiro cha nyonga, mphamvu, kapena ulamuliro.