Luka 18:1-43
18 Ndiyeno Yesu anawauza fanizo pofuna kuwasonyeza kufunika koti azipemphera nthawi zonse, osaleka.+
2 Iye anati: “Mumzinda winawake munali woweruza wina amene anali wosaopa Mulungu ndiponso wosasamala za munthu.
3 Koma mumzindawo munali mkazi wina wamasiye ndipo anali kupitapita+ kwa woweruza uja kukamupempha kuti, ‘Ndiweruzireni mlandu wanga ndi munthu amene akutsutsana nane, kuti pachitike chilungamo.’
4 Kwa kanthawi ndithu woweruzayo sankafuna, koma pambuyo pake ananena mumtima mwake kuti, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kusamala za munthu,
5 ndionetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa mkazi wamasiyeyu. Ndichita zimenezi kuti asapitirize kumangobwera ndi kundisautsa kwambiri,+ chifukwa mkazi ameneyu akundivutitsa+ mosalekeza.’”
6 Kenako Ambuye anati: “Mwamvatu zimene woweruzayo ananena ngakhale kuti anali wosalungama!
7 Ndithu, ngakhale kuti Mulungu amalezera mtima+ osankhidwa ake, kodi sadzaonetsetsa kuti chilungamo+ chachitika kwa iwo, amene amafuulira kwa iye usana ndi usiku?
8 Ndithu ndikukuuzani, Iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga.+ Koma, Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi chikhulupiriro padziko lapansi?”
9 Yesu ananenanso fanizo lotsatirali kwa ena odzidalira, odziona ngati olungama+ amenenso amaona ena onse ngati opanda pake.+ Iye anati:
10 “Anthu awiri anapita m’kachisi kukapemphera. Mmodzi anali Mfarisi, winayo anali wokhometsa msonkho.
11 Mfarisi uja anaimirira+ ndi kuyamba kupemphera+ mumtima mwake. Iye anati, ‘Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. Iwo ndi olanda, osalungama ndi achigololo. Sindilinso ngati wokhometsa msonkho uyu.+
12 Ine ndimasala kudya kawiri pa mlungu ndipo ndimapereka chakhumi pa zinthu zonse zimene ndimapeza.’+
13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa+ ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’+
14 Ndithu ndikukuuzani, Munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kukhala wolungama kwambiri+ kusiyana ndi wina uja, chifukwa aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzichepetsa adzamukweza.”+
15 Pamenepo anthu anayamba kumubweretsera ana kuti awakhudze ndi manja ake, koma ophunzirawo ataona zimenezo anayamba kuwakalipira.+
16 Komabe Yesu anaitana anawo. Iye anati: “Alekeni anawo abwere kwa ine, musawaletse ayi. Pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa.+
17 Ndithu ndikukuuzani, Aliyense wosalandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowa n’komwe mu ufumuwo.”+
18 Tsopano wolamulira wina anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, ndizichita chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+
19 Yesu anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.+
20 Iwe umadziwa malamulo+ akuti, ‘Usachite chigololo,+ Usaphe munthu,*+ Usabe,+ Usapereke umboni wonama+ ndiponso lakuti, Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’”+
21 Pamenepo iye anati: “Zonsezi ndakhala ndikuzitsatira kuyambira ndili wamng’ono.”+
22 Atamva zimenezo, Yesu anamuuza kuti: “Pali chinthu chimodzi chimene chikusowekabe mwa iwe: Kagulitse zinthu zonse zimene uli nazo n’kugawa ndalamazo kwa anthu osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+
23 Iye atamva zimenezi, anamva chisoni kwambiri, chifukwa anali wolemera kwabasi.+
24 Yesu anamuyang’ana n’kunena kuti: “Zidzakhalatu zovuta kwambiri kuti anthu a ndalama adzalowe mu ufumu wa Mulungu!+
25 Kunena zoona, n’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.”+
26 Amene anamva zimenezi anati: “Ndiye angapulumuke ndani?”
27 Iye anawauza kuti: “Zinthu zosatheka ndi anthu n’zotheka ndi Mulungu.”+
28 Koma Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu ndi kukutsatirani.”+
29 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Palibe amene wasiya nyumba, mkazi, abale, makolo kapena ana, chifukwa cha ufumu wa Mulungu+
30 amene sadzapeza zochuluka kwambiri kuposa zimenezi m’nthawi ino, ndipo m’nthawi* ikubwerayo moyo wosatha.”+
31 Kenako anatengera pambali ophunzira 12 aja ndi kuwauza kuti: “Tamverani! Tsopano tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zinalembedwa ndi aneneri,+ zokhudza Mwana wa munthu zikakwaniritsidwa.+
32 Mwachitsanzo, akamupereka kwa anthu a mitundu ina ndipo akamuseka,+ kum’chitira chipongwe+ ndi kumulavulira.+
33 Akakamaliza kumukwapula+ akamupha,+ koma tsiku lachitatu iye adzauka.”+
34 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la chilichonse cha zimenezi. Mawu amenewa anabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe zimene zinanenedwazo.+
35 Tsopano pamene anali kuyandikira ku Yeriko, munthu wina wakhungu anakhala pansi m’mphepete mwa msewu n’kumapemphapempha.+
36 Atamva khamu la anthu likudutsa chapomwepo, anafunsa chimene chinali kuchitika.
37 Iwo anamuuza kuti: “Yesu Mnazareti akudutsa!”+
38 Atamva zimenezo anafuula kuti: “Yesu, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo!”+
39 Ndiyeno amene anali patsogolo anayamba kumudzudzula mwamphamvu kuti akhale chete. Koma m’pamenenso iye anafuula kwambiri kuti: “Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo.”+
40 Choncho Yesu anaima ndi kulamula kuti munthuyo apite naye kwa iye.+ Atafika pafupi, Yesu anamufunsa kuti:
41 “Ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”+ Iye anayankha kuti: “Ambuye, ndithandizeni kuti ndiyambe kuona.”+
42 Choncho Yesu anamuuza kuti: “Yamba kuona, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+
43 Nthawi yomweyo anayamba kuona,+ ndipo anayamba kumutsatira akulemekeza Mulungu.+ Komanso anthu onse, ataona zimenezi, anatamanda Mulungu.
Mawu a M'munsi
^ Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.