Luka 14:1-35
14 Kanthawi kena atalowa m’nyumba ya mmodzi wa akuluakulu a Afarisi pa sabata kukadya chakudya,+ Afarisiwo anali kumuyang’anitsitsa.+
2 Patsogolo pake panakhala munthu amene anali kudwala matenda amene anamutupitsa manja ndi miyendo.
3 Atamuona, Yesu analankhula ndi odziwa Chilamulo ndi Afarisiwo kuti: “Kodi n’kololeka kuchiritsa pa sabata kapena ayi?”+
4 Koma iwo anangokhala chete. Pamenepo iye anagwira munthu uja, n’kumuchiritsa ndi kumuuza kuti azipita kwawo.
5 Ndiyeno anawauza kuti: “Ndani wa inu, amene mwana wake kapena ng’ombe yake itagwera m’chitsime+ pa tsiku la sabata, sangaitulutse nthawi yomweyo?”+
6 Iwo sanathe kumuyankha pa zinthu zimenezi.+
7 Ataona mmene anthu oitanidwawo anali kusankhira malo olemekezeka kwambiri, anawauza fanizo kuti:+
8 “Wina akakuitana kuphwando laukwati, usakhale pamalo olemekezeka kwambiri.+ Mwina n’kutheka kuti waitananso wina wolemekezeka kuposa iwe,
9 ndipo amene wakuitana uja angabwere ndi wolemekezekayo kudzakuuza kuti, ‘Choka pamenepa pakhale bambo awa.’ Pamenepo udzachokapo mwamanyazi n’kukakhala kumapeto kwenikweni.+
10 Koma ukaitanidwa, pita ndipo ukakhale kumapeto kwenikweni,+ kuti munthu amene wakuitana uja akafika adzakuuze kuti, ‘Bwanawe, khala pamalo aulemuwa.’ Pamenepo udzalemekezeka pamaso pa alendo anzako onse.+
11 Pakuti aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”+
12 Kenako anauzanso munthu amene anamuitana uja kuti: “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usaitane mabwenzi ako, kapena abale ako, kapena afuko lako, kapena anthu olemera omwe amakhala nawe pafupi. Mwina nthawi ina iwonso angadzakuitane ndipo kudzakhala ngati kukubwezera.
13 Koma ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi akhungu.+
14 Ukatero udzakhala wodala, chifukwa alibe choti adzabweze kwa iwe. Pakuti udzabwezeredwa pa kuuka+ kwa anthu olungama.”
15 Atamva izi, mmodzi wa alendo anzake anamuuza kuti: “Wodala ndi munthu wakudya chakudya mu ufumu wa Mulungu.”+
16 Yesu anamuuza kuti: “Munthu wina anakonza phwando lalikulu la chakudya chamadzulo ndipo anaitana anthu ambiri.+
17 Nthawi ya chakudya chamadzulocho itakwana, anatumiza kapolo wake kukauza oitanidwawo kuti, ‘Tiyeni,+ chifukwa zonse zakonzedwa tsopano.’
18 Koma onse mofanana anayamba kupereka zifukwa zokanira.+ Woyamba anamuuza kuti, ‘Ine ndagula munda, choncho ndiyenera kupita kukauona. Pepani sinditha kufika!’+
19 Wina ananena kuti, ‘Ine ndagula ng’ombe 10 zapagoli ndipo ndikupita kukaziyesa. Pepani sinditha kufika!’+
20 Komanso wina anati, ‘Ine ndangokwatira kumene,+ choncho sindingathe kubwera.’
21 Ndiyeno kapolo uja anabwerera kukanena zimenezi kwa mbuye wake. Pamenepo mwininyumba anakwiya ndi kuuza kapolo wake kuti, ‘Pita mwamsanga m’misewu ndi m’njira za mumzindawu, ukatenge anthu osauka, otsimphina, akhungu ndi olumala ndi kubwera nawo kuno.’+
22 Patapita kanthawi kapolo uja anati, ‘Mbuyanga, zimene munalamula zachitika, komabe malo adakalipo.’
23 Ndiyeno mbuye uja anauza kapolo wakeyo kuti, ‘Pita m’misewu+ ndi malo a kumpanda, uwalimbikitse kuti abwere kuno kuti nyumba yanga idzaze.+
24 Pakuti ndikukuuzani anthu inu, Palibe ndi mmodzi yemwe mwa oitanidwa aja amene adzalaweko chakudya changa chamadzulochi.’”+
25 Tsopano khamu lalikulu la anthu linali kuyenda limodzi ndi Yesu. Kenako anacheuka ndi kuwauza kuti:
26 “Ngati wina wabwera kwa ine, koma osadana ndi bambo ake, mayi ake, mkazi wake, ana ake, abale ake ndi alongo ake, ngakhale moyo wake umene,+ sangakhale wophunzira wanga.+
27 Aliyense wosanyamula mtengo wake wozunzikirapo* ndi kunditsatira ine sangakhale wophunzira wanga.+
28 Mwachitsanzo, ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge,+ kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?
29 Akapanda kutero, angayale maziko koma osatha kuimaliza, ndipo onse oona angayambe kumuseka,
30 n’kumanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba bwinobwino kumanga, koma zamukanika kumaliza.’
31 Kapena ndi mfumu yanji, imene popita kukakumana ndi mfumu inzake pa nkhondo, siyamba yakhala pansi ndi kuganiza mofatsa ngati asilikali ake 10,000 angathe kulimbana ndi asilikali 20,000 a mfumu yobwera kudzalimbana naye?+
32 Koma akaona kuti sangakwanitse, mwamsanga amatumiza akazembe kwa mfumu inayo isanafike pafupi, kukapempha mtendere.+
33 Choncho, dziwani ichi, ndithu palibe aliyense wolephera kulekana ndi chuma chake chonse+ amene angathe kukhala wophunzira wanga.
34 “Kunena zoona, mchere ndi wabwino. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, kodi mphamvu yake ingabwezeretsedwe bwanji?+
35 Ndi wosayeneranso ngakhale kuuthira m’nthaka kapena m’manyowa. Anthu amangoutaya kunja. Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 9.