Luka 23:1-56
23 Pamenepo khamu lonselo linanyamuka, onse pamodzi, n’kupita naye kwa Pilato.+
2 Ndiyeno anayamba kumuneneza+ kuti: “Ife tapeza munthu uyu akupandutsa+ mtundu wathu ndi kuletsa anthu kuti asamakhome msonkho+ kwa Kaisara, komanso iyeyu akunena kuti ndi Khristu mfumu.”+
3 Tsopano Pilato anamufunsa funso kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?” Pomuyankha iye anati: “Mukunena nokha.”+
4 Pamenepo Pilato anauza ansembe aakulu ndi khamu la anthulo kuti: “Sindikupeza mlandu uliwonse mwa munthu uyu.”+
5 Koma iwo anaumirira kuti: “Iyeyu akusokoneza anthu mwa kuphunzitsa mu Yudeya monse, ngakhalenso kuyambira ku Galileya mpaka kudzafika kuno.”
6 Atamva zimenezo, Pilato anafunsa ngati munthuyu ndi Mgalileya.
7 Ndiyeno, atadziwa kuti ndi wochokera m’chigawo cholamulidwa ndi Herode,*+ anamutumiza kwa Herode, amene m’masiku amenewo anali mu Yerusalemu.
8 Herode ataona Yesu anakondwera kwambiri, chifukwa kwa nthawi yaitali ndithu anali kufunitsitsa kuti amuone+ popeza anali kumva+ za iye. Komanso anali kuyembekezera kuona chizindikiro chimene iye angachite.
9 Tsopano anayamba kumufunsa zambiri, koma iye sanayankhe.+
10 Komabe ansembe aakulu ndi alembi anali kumangonyamukanyamuka ndi kumuneneza mwaukali.+
11 Pamenepo Herode pamodzi ndi asilikali ake omulondera anamupeputsa.+ Anamuchitira zachipongwe+ mwa kumuveka chovala chonyezimira ndipo anamutumizanso kwa Pilato.
12 Tsiku lomwelo Herode ndi Pilato+ anakhala mabwenzi tsopano, koma m’mbuyo monsemo izi zisanachitike, anali pa udani.
13 Ndiyeno Pilato anasonkhanitsa ansembe aakulu, olamulira ndi anthu ena
14 ndi kuwauza kuti: “Inu mwabweretsa munthu uyu kwa ine monga wolimbikitsa anthu kuukira. Koma mwaona nokha pano! Inetu ndamufunsa pamaso panu, ndipo sindinamupeze ndi chifukwa+ chomuimbira milandu imene mukumunenezayi.
15 Ndipotu ngakhale Herode sanam’peze ndi mlandu, n’chifukwa chake wam’bweza kwa ife. Ndithudi ameneyu sanachite chilichonse choyenera chilango cha imfa.+
16 Choncho ndingomukwapula+ ndi kumumasula.”
17 * ——
18 Koma khamu lonse linafuulira pamodzi kuti: “Ameneyu muthane naye basi,+ koma ife mutimasulire Baraba!”+
19 (Munthu ameneyu anaponyedwa m’ndende chifukwa cha kuukira boma kumene kunachitika mumzindawo, komanso chifukwa chopha munthu.)
20 Pilato analankhula nawo kachiwiri, chifukwa anali wofunitsitsa kumasula Yesu.+
21 Pamenepo anthuwo anayamba kufuula kuti: “M’pachikeni! M’pachikeni!”+
22 Anawafunsa kachitatu kuti: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani? Ine sindikumupeza ndi chifukwa chilichonse chomuphera, choncho ndimukwapula ndi kumumasula.”+
23 Atamva izi, anayamba kumuumiriza mokweza mawu, ndi kumupempha kuti Yesu apachikidwe basi. Anthuwo anali kufuula mwamphamvu moti Pilato anangololera.+
24 Choncho Pilato anapereka chiweruzo chokwaniritsa zofuna za anthuwo.+
25 Iye anamasula+ munthu woponyedwa m’ndende pa mlandu woukira boma ndi kupha munthu, amenenso anthuwo anapempha kuti amumasule. Koma Yesu anamupereka m’manja mwawo kuti zofuna zawo zichitike.+
26 Pamene anali kupita naye, iwo anagwira Simoni, nzika ya ku Kurene, amene anali kuchokera kudera lakumidzi. Iwo anamusenzetsa mtengo wozunzikirapo,* kuti aunyamule ndi kumatsatira pambuyo pa Yesu.+
27 Koma khamu lalikulu la anthu linali kumutsatira pamodzi ndi amayi ambiri amene anali kudziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni ndipo anali kumulirira.
28 Yesu anacheukira amayiwo ndi kunena kuti: “Ana aakazi a Yerusalemu inu, lekani kundilirira. Koma mudzilirire nokha ndi ana anu.+
29 Chifukwa masiku akubwera pamene anthu adzanena kuti, ‘Odala ndi akazi osabereka, amene sanaberekepo, komanso amene mabere awo sanayamwitsepo!’+
30 M’masiku amenewo iwo adzayamba kuuza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza zitunda kuti, ‘Tikwirireni!’+
31 Pakuti ngati akuchita izi pamene mtengo uli wauwisi, kuli bwanji mtengowo ukadzauma?”+
32 Anthuwo anatenganso amuna ena awiri ochita zoipa, kuti akawaphe limodzi ndi Yesu.+
33 Tsopano atafika pamalo otchedwa Chibade,+ anamupachika pamenepo pamodzi ndi amuna ochita zoipawo. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja, wina kumanzere kwake.+
34 [[Koma Yesu anati: “Atate, akhululukireni,+ chifukwa sakudziwa chimene akuchita.”]]* Ndipo iwo anagawana malaya ake mwa kuchita maere.+
35 Anthu anangoima chilili kuonerera zochitikazo.+ Koma olamulira anali kumunyogodola kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, m’lekeni adzipulumutse yekha,+ ngati iyeyu alidi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwa.”+
36 Asilikali nawonso anamuchitira zachipongwe,+ anamuyandikira ndi kumupatsa vinyo wowawasa+
37 ndi kunena kuti: “Ngati ulidi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.”
38 Pamwamba pake analembapo mawu akuti: “Uyu ndiye mfumu ya Ayuda.”+
39 Komanso mmodzi wa ochita zoipa amene anapachikidwa naye pamodziwo anayamba kumulankhulira zachipongwe+ kuti: “Kodi si iwe Khristu? Dzipulumutse wekha, limodzi ndi ife.”
40 Poyankha mnzake uja anamudzudzula kuti: “Kodi iwe suopa Mulungu eti, poona kuti nawenso ukulandira chilango chofanana ndi cha munthu ameneyu?+
41 Ifetu m’pake kulangidwa chonchi, pakuti tikulandiriratu zonse zotiyenera malinga ndi zimene tinachita. Koma munthu uyu sanalakwe chilichonse.”+
42 Kenako anapitiriza kunena kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.”+
43 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine+ m’Paradaiso.”+
44 Tsopano nthawi inali cha m’ma 12 koloko masana,* koma kunagwa mdima padziko lonse lapansi mpaka 3 koloko masana,*+
45 popeza dzuwa linachita mdima. Pa nthawi imeneyi nsalu yotchinga+ ya m’nyumba yopatulika inang’ambika pakati+ kuchokera pamwamba mpaka pansi.
46 Pamenepo Yesu anafuula mokweza mawu kuti: “Atate, ndikuikiza mzimu*+ wanga m’manja mwanu.” Atanena zimenezi anatsirizika.+
47 Poona zochitikazo, kapitawo wa asilikali anayamba kutamanda Mulungu kuti: “Ndithudi munthu uyu anali wolungama.”+
48 Anthu onse amene anasonkhana kumeneko kudzaona zochitikazo, ataona zonse zimene zinachitika, anayamba kubwerera akudziguguda pachifuwa.
49 Komanso onse amene anali kumudziwa anaimirira chapatali ndithu.+ Ndipo amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anaimiriranso chapomwepo n’kumaonerera zinthu zimenezi.+
50 Tsopano panali mwamuna wina dzina lake Yosefe, amene anali wa m’Khoti Lalikulu la Ayuda, munthu wabwino ndi wolungama.+
51 Munthu ameneyu sanavomereze chiwembu chawo ndi zochita zawo.+ Yosefe anali wochokera ku Arimateya, mzinda wa Ayudeya, ndipo anali kuyembekezera ufumu wa Mulungu.+
52 Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu.+
53 Choncho anautsitsa+ ndi kuukulunga munsalu yabwino kwambiri, kenako anakauika m’manda+ ogobedwa muthanthwe, mmene anali asanaikemo munthu chikhalire.+
54 Tsopano linali Tsiku Lokonzekera,+ ndipo chisisira cha madzulo chosonyeza kuyambika kwa sabata+ chinali kuyambika.
55 Koma amayi amene anayenda limodzi ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anamutsatira kukaona manda achikumbutsowo+ ndi mmene mtembo wakewo anauikira.+
56 Atatero anabwerera kukakonza zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira.+ Komabe pa tsiku la sabata+ anapuma malinga ndi chilamulo.
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 9.
^ Mikutiramawu yophatikiza ikusonyeza mawu amene mulibe m’mipukutu ina yakale koma akupezeka m’mipukutu ina.
^ Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
^ Mawu ake enieni, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
^ Onani Zakumapeto 4.