Luka 9:1-62

9  Tsopano Yesu anasonkhanitsa atumwi 12 aja ndi kuwapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse ndi kuti azitha kuchiritsa matenda.+  Choncho anawatumiza kukalalikira ufumu wa Mulungu ndi kuchiritsa anthu.  Iye anawauza kuti: “Musanyamule kanthu pa ulendowu, musatenge ndodo, kapena thumba la chakudya, kapena mkate, kapena ndalama zasiliva, kapena kutenga malaya awiri amkati.+  Koma mukafika pakhomo lililonse, khalani pamenepo kufikira nthawi yochoka kumeneko.+  Kulikonse kumene anthu sakakulandirani, potuluka mumzinda+ umenewo, sansani fumbi kumapazi anu kuti ukhale umboni wowatsutsa.”+  Pamenepo ananyamuka ndi kulowa m’deralo m’mudzi ndi mudzi. Iwo anali kulengeza uthenga wabwino ndi kuchiritsa anthu kwina kulikonse.+  Tsopano Herode* wolamulira chigawo anamva zonse zimene zinali kuchitika. Iye anathedwa nzeru chifukwa ena anali kunena kuti Yohane anauka kwa akufa.+  Koma ena anali kunena kuti Eliya waonekera. Enanso anali kunena kuti winawake mwa aneneri akale wauka.  Ndiyeno Herode anati: “Yohane ndinamudula mutu.+ Nanga uyu ndaninso amene akuchita zomwe ndikumvazi?” Choncho anali kufunitsitsa kumuona.+ 10  Atumwi aja atabwerako anafotokozera Yesu zimene iwo anachita.+ Atatero anawatenga ndi kupita nawo kwaokhaokha+ mumzinda wotchedwa Betsaida. 11  Koma khamu la anthu linadziwa ndi kum’tsatira. Iye anawalandirabe bwino ndi kuyamba kuwauza za ufumu wa Mulungu,+ ndipo anachiritsa amene anafunika kuchiritsidwa.+ 12  Komano nthawi inali itapita. Choncho atumwi 12 aja anafika ndi kumuuza kuti: “Auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite m’midzi ndi m’madera apafupi kuti akapeze malo ogona ndi chakudya, chifukwa kumene tili kuno n’kopanda anthu.”+ 13  Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.”+ Iwo anati: “Tilibe chilichonse kuno koma mitanda ya mkate isanu ndi nsomba+ ziwiri zokha basi. Mwina tingapite kukagula chakudya chokwanira anthu onsewa.”+ 14  Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000.+ Koma Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Auzeni akhale m’magulu, muja amakhalira akamadya chakudya. Pagulu lililonse pakhale anthu pafupifupi 50.”+ 15  Iwo anachitadi zimenezo, mwakuti onsewo anawakhazika bwinobwino. 16  Kenako anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija ndipo anayang’ana kumwamba ndi kudalitsa chakudyacho. Kenako ananyemanyema mitanda ya mkate ndi nsombazo n’kupereka kwa ophunzira kuti apatse anthuwo.+ 17  Choncho onse anadya ndi kukhuta, ndipo anatolera zotsala kudzaza madengu 12.+ 18  Nthawi inayake, pamene anali kupemphera payekha, ophunzira ake anafika kwa iye onse pamodzi. Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Kodi anthuwa akumati ine ndine ndani?”+ 19  Poyankha iwo anati: “Amati ndinu Yohane M’batizi. Koma ena amati ndinu Eliya. Enanso amati mmodzi wa aneneri akale wauka.”+ 20  Pamenepo anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Petulo anayankha kuti:+ “Ndinu Khristu+ wa Mulungu.” 21  Ndiyeno anawalangiza mwamphamvu kuti asauze aliyense zimenezo.+ 22  Kenako anati: “Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri. Iye adzakanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno adzaphedwa,+ koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ 23  Kenako anauza onse kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha+ ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo* tsiku ndi tsiku ndi kunditsatira mosalekeza.+ 24  Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine, adzaupulumutsa.+ 25  Kunena zoona, kodi munthu angapindulenji ngati atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma iyeyo n’kudzivulaza kapena kutaya moyo wake?+ 26  Pakuti aliyense wochita manyazi ndi ine, komanso ndi mawu anga, Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi akadzafika mu ulemerero wake, wa Atate wake ndi wa angelo oyera.+ 27  Koma ndikukuuzani ndithu, Pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe kufikira choyamba ataona ufumu wa Mulungu.”+ 28  Patapita masiku pafupifupi 8 chinenereni mawu amenewa, iye anatenga Petulo, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera nawo m’phiri kukapemphera.+ 29  Pamene anali kupemphera, maonekedwe+ a nkhope yake anasintha ndipo chovala chake chinaoneka choyera kwambiri ndi chonyezimira.+ 30  Ndiyeno panaonekanso anthu awiri akukambirana naye. Anthu amenewa anali Mose ndi Eliya.+ 31  Amenewa anaonekera ndi ulemerero ndipo anayamba kukambirana za mmene adzachokere m’dzikoli, ku Yerusalemu.*+ 32  Apa n’kuti Petulo ndi ena amene anali naye atatopa ndi tulo. Koma mmene anayeranso m’maso anaona ulemerero+ wake ndiponso amuna awiri ataima naye. 33  Tsopano pamene amenewa anali kulekana naye, Petulo anauza Yesu kuti:+ “Mlangizi, ndi bwino kuti ife tizikhala pano. Choncho timange mahema atatu, limodzi lanu, limodzi la Mose ndi lina la Eliya.” Koma iye sanali kuzindikira zimene anali kunena. 34  Pamene anali kunena zimenezi, kunachita mtambo ndipo unayamba kuwaphimba. Pamene mtambowo unali kuwakuta, anachita mantha.+ 35  Ndiyeno mawu+ anatuluka mumtambomo akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga, amene ndinam’sankha.+ Mumvereni.”+ 36  Pamene mawuwo anali kumveka, anaona kuti Yesu ali yekha.+ Koma iwo anakhala chete ndipo sanauze aliyense m’masiku amenewo chilichonse mwa zimene anaonazo.+ 37  Tsiku lotsatira, atatsika m’phirimo, chikhamu cha anthu chinam’chingamira.+ 38  Pamenepo munthu wina anafuula kuchokera m’khamulo kuti: “Mphunzitsi, ndikukupemphani kuti mukaone mwana wanga wamwamuna, chifukwa ndi mmodzi yekhayo.+ 39  Mzimu umam’gwira, ndipo mwadzidzidzi amafuula, kenako umam’tsalimitsa kwinaku akuchita thovu. Mzimu+ umenewu umamuvulaza kwambiri ndipo suchoka msanga. 40  Ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse, koma alephera.”+ 41  Poyankha Yesu anati: “Inu a m’badwo+ wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo, kodi ndikhala nanube ndi kupitiriza kukupirirani mpaka liti? Bwera naye kuno mwana wakoyo.”+ 42  Koma ngakhale pamene anali kufika naye kwa iye, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kum’tsalimitsa mwamphamvu. Yesu anakalipira mzimu wonyansawo ndi kuchiritsa mnyamatayo. Kenako anamupereka kwa bambo ake.+ 43  Pamenepo, onse anadabwa ndi mphamvu zodabwitsa+ za Mulungu. Tsopano onse adakali odabwa ndi zonse zimene anali kuchita, Yesu anauza ophunzira ake kuti: 44  “Mumvetse bwino mawu awa, pakuti Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu.”+ 45  Koma ophunzirawo sanamvetsebe tanthauzo la mawu amenewa. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo kuti asazindikire, ndipo anaopa kumufunsa za mawu amenewa.+ 46  Kenako iwo anayamba kukhala ndi maganizo ofuna kudziwa amene ali wamkulu koposa pakati pawo.+ 47  Yesu podziwa zimene anali kuganiza mumtima mwawo, anatenga mwana wamng’ono, n’kumuimika pafupi ndi iye.+ 48  Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense wolandira mwana wamng’ono uyu m’dzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense wolandira ine walandiranso amene anandituma ine.+ Pakuti aliyense wokhala ngati wamng’ono+ pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.”+ 49  Ndiyeno Yohane ananena kuti: “Mlangizi, tinaona munthu wina akutulutsa ziwanda+ m’dzina lanu, choncho ife tinamuletsa+ chifukwa sakukutsatirani pamodzi ndi ife.”+ 50  Koma Yesu anamuuza kuti: “Musamuletse amuna inu, chifukwa amene sakutsutsana nanu ali kumbali yanu.”+ 51  Pamene masiku oti akwere kumwamba+ anali kukwana, anatsimikiza mtima kupita ku Yerusalemu. 52  Choncho anatsogoza amithenga. Iwo ananyamuka ndi kukalowa m’mudzi wa Asamariya,+ kukakonzekera kufika kwake. 53  Koma iwo sanamulandire chifukwa mtima wake pa ulendowo unali ku Yerusalemu.+ 54  Ophunzira ake, Yakobo ndi Yohane,+ ataona zimenezi anati: “Ambuye, kodi mukufuna tiwaitanire moto+ kuchokera kumwamba kuti uwanyeketse?” 55  Koma iye anatembenuka ndi kuwadzudzula. 56  Choncho anapita kumudzi wina. 57  Tsopano ali pa ulendowo, winawake anauza Yesu kuti: “Ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.”+ 58  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamira mutu wake.”+ 59  Kenako anauza munthu wina kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Koma munthuyo anati: “Ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.”+ 60  Yesu anamuyankha kuti: “Aleke akufa+ aike akufa awo, koma iwe pita kukalengeza ufumu wa Mulungu+ kwina kulikonse.” 61  Winanso ananena kuti: “Ine ndikutsatirani Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsanzika a m’banja langa.”+ 62  Yesu anamuuza kuti: “Aliyense wogwira pulawo+ koma n’kumayang’ana zinthu za m’mbuyo+ sayenera ufumu wa Mulungu.”

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.
Onani Zakumapeto 9.
Mawu ake enieni, “za kuchoka kwake kumene iye anayenera kudzakwaniritsa ku Yerusalemu.”