Luka 5:1-39
5 Nthawi inayake khamu la anthu linali kumvetsera pamene Yesu anali kuphunzitsa mawu a Mulungu m’mphepete mwa nyanja ya Genesarete.*+ Kenako anthuwo anayamba kumupanikiza.
2 Pamenepo iye anaona ngalawa ziwiri atazikocheza m’mphepete mwa nyanjayo, koma asodzi anali atatsikamo ndipo anali kutsuka maukonde awo.+
3 Choncho iye analowa m’ngalawa imodzi, imene inali ya Simoni, ndipo anamupempha kuti aisunthire m’madzi pang’ono. Kenako anakhala pansi, ndipo ali m’ngalawamo+ anayamba kuphunzitsa khamu la anthulo.
4 Atamaliza kulankhula, anauza Simoni kuti: “Palasira kwakuya, ndipo muponye maukonde+ anu kuti muphe nsomba.”
5 Koma poyankha Simoni anati: “Mlangizi, ife tagwira ntchito usiku wonse koma osapha kalikonse.+ Koma popeza mwanena ndinu, ndiponya maukondewa.”
6 Atachita zimenezo, anakola nsomba zochuluka kwambiri. Ndipo maukonde awo anayamba kung’ambika.
7 Choncho anakodola anzawo amene anali m’ngalawa ina kuti adzawathandize.+ Iwo anabweradi, ndipo nsombazo zinadzaza ngalawa zonse ziwiri, moti ngalawazo zinayamba kumira.
8 Ataona zimenezi, Simoni Petulo+ anagwada ndi kuweramira pamawondo a Yesu n’kumuuza kuti: “Ambuye, chokani pali ine pano, chifukwa ndine munthu wochimwa.”+
9 Simoni anadabwa kwambiri ndi nsomba zimene anaphazo, chimodzimodzi ena onse amene anali naye limodzi.
10 Komanso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo,+ amene anali kugwirizana ndi Simoni anadabwa kwambiri. Koma Yesu anauza Simoni kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.”+
11 Choncho ngalawazo anafika nazo kumtunda, ndipo iwo anasiya chilichonse ndi kumutsatira.+
12 Nthawi inanso pamene anali mumzinda wina, anakumana ndi munthu wakhate thupi lonse. Pamene anaona Yesu, munthuyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndi kum’pempha, kuti: “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+
13 Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake n’kumukhudza, ndipo anati: “Ndikufuna. Khala woyera.” Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.+
14 Kenako analamula munthuyo kuti asauze aliyense.+ Ndiyeno anamuuza kuti: “Koma upite ukadzionetse kwa wansembe,+ ndipo ukapereke nsembe+ ya kuyeretsedwa kwako, monga mmene Mose analamulira, kuti ikhale umboni kwa iwo.”+
15 Koma mbiri yake inali kufalikira kwambiri, ndipo makamu a anthu anali kusonkhana pamodzi kudzamumvetsera ndi kudzachiritsidwa matenda awo.+
16 Koma iye anakhalabe kwayekha m’chipululu ndi kupitiriza kupemphera.+
17 Tsiku lina iye anali kuphunzitsa, ndipo Afarisi ndi aphunzitsi a chilamulo ochokera m’midzi yonse ya Galileya, ku Yudeya ndi ku Yerusalemu anakhala pansi pamalo omwewo. Ndipo mphamvu ya Yehova inali pa iye kuti athe kuchiritsa.+
18 Kenako panafika anthu atanyamula munthu wakufa ziwalo pakabedi. Iwo anali kufunafuna njira yoti amulowetsere ndi kumuika pafupi ndi Yesu.+
19 Koma atalephera kudutsa naye chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, anakwera padenga.* Ndipo kudzera pabowo limene anatsegula padengapo, anamutsitsa limodzi ndi kabediko n’kumufikitsa pakati pa anthu amene anali pamaso pa Yesu.+
20 Ataona chikhulupiriro chawo, anati: “Bwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+
21 Pamenepo alembi ndi Afarisi anayamba kudzifunsa, kuti: “Ndani ameneyu kuti azinyoza Mulungu chonchi?+ Winanso ndani amene angakhululukire machimo? Si Mulungu yekha kodi?”+
22 Koma Yesu, pozindikira zimene anali kuganiza anawayankha kuti: “Kodi mukuganiza chiyani m’mitima mwanu?+
23 Chapafupi n’chiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka uyende’?+
24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo . . .” anauza munthu wakufa ziwalo uja kuti: “Ndikunena ndi iwe, Nyamuka, tenga kabedi kakoka uzipita kwanu.”+
25 Nthawi yomweyo anaimirira onse akuona, ndipo ananyamula chogonera chake chija n’kupita kwawo, akutamanda Mulungu.+
26 Pamenepo anthu onsewo anadabwa kwambiri,+ ndipo anayamba kutamanda Mulungu, mwakuti anagwidwa ndi mantha. Iwo anali kunena kuti: “Taona zodabwitsa lero!”+
27 Zimenezi zitachitika iye anachokako. Kenako anaona wokhometsa msonkho wotchedwa Levi atakhala pansi mu ofesi yokhomera msonkho. Ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”+
28 Pamenepo Leviyo anasiya chilichonse,+ ndipo ananyamuka n’kumutsatira.
29 Tsopano Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake. Kumeneko kunali khamu lalikulu la okhometsa msonkho ndi ena ambiri, ndipo anali kudyera limodzi.+
30 Afarisi ndi alembi awo ataona izi, anayamba kung’ung’udza ndi kufunsa ophunzira ake kuti: “N’chifukwa chiyani inu mumadya ndi kumwa limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?”+
31 Poyankha, Yesu anawauza kuti: “Anthu athanzi safuna dokotala,+ koma odwala ndi amene amamufuna.+
32 Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa kuti alape.”+
33 Iwo anamuuza kuti: “Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri ndi kupemphera mopembedzera. Ophunzira a Afarisi amachitanso chimodzimodzi, koma anuwa amangodya ndi kumwa.”+
34 Yesu anawayankha kuti: “Inu simungauze anzake a mkwati kuti asale kudya pamene mkwatiyo ali nawo limodzi, mungatero ngati?+
35 Koma masiku adzafika pamene mkwati+ adzachotsedwa pakati pawo.+ Pamenepo iwo adzasala kudya masiku amenewo.”+
36 Komanso, anawapatsa fanizo kuti: “Palibe amene amadula chigamba pamalaya akunja atsopano n’kuchisokerera pamalaya akunja akale. Munthu akachita zimenezo, chigamba chatsopanocho chimachoka pansalu yakaleyo. Ndiponso chigamba cha nsalu yatsopanocho sichiyenerana ndi malaya akalewo.+
37 Komanso, palibe amene amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa akale. Munthu akachita zimenezo, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba achikopawo.+ Vinyoyo amatayika ndipo matumba achikopawo amawonongeka.+
38 Koma vinyo watsopano ayenera kuikidwa m’matumba achikopa atsopano.
39 Munthu akamwa vinyo wakale safunanso watsopano, chifukwa amanena kuti, ‘Wakaleyu+ ali bwino kwambiri.’”
Mawu a M'munsi
^ M’Baibulo, “nyanja ya Genesarete” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Galileya, komanso nyanja ya Tiberiyo.
^ Kapena kuti “patsindwi.”