Luka 3:1-38
3 M’chaka cha 15 cha ulamuliro wa Kaisara Tiberiyo, Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode*+ anali wolamulira chigawo cha Galileya. Filipo m’bale wake anali wolamulira chigawo cha madera a Itureya ndi Tirakoniti. Ndipo Lusaniyo anali wolamulira chigawo cha Abilene.
2 M’masiku amenewo Anasi anali wansembe wamkulu ndipo Kayafa+ anali mkulu wa ansembe. Pa nthawiyo mawu a Mulungu anafika kwa Yohane+ mwana wa Zekariya m’chipululu.+
3 Choncho iye anabwera m’midzi yonse yapafupi ndi Yorodano. Anali kulalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+
4 Anali kuchita zimenezi monga mmene analembera m’buku la mawu a Yesaya mneneri kuti: “Tamverani! Winawake akufuula m’chipululu kuti, ‘Konzani njira ya Yehova anthu inu! Wongolani misewu yake.+
5 Dzenje lililonse likwiriridwe, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zisalazidwe. Njira zokhotakhota zikhale zowongoka ndipo malo okumbikakumbika akhale osalala bwino.+
6 Anthu onse adzaona njira ya Mulungu yopulumutsira.’”+
7 Pamenepo anayamba kuuza khamu la anthu obwera kwa iye kudzabatizidwa kuti: “Ana a njoka inu,+ ndani wakuchenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwerawo?+
8 Ndiyetu mubale zipatso zosonyeza kuti mwalapa.+ Ndipo musayambe kunena kuti, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’ Pakuti ndikukuuzani kuti Mulungu ali ndi mphamvu yokhoza kuutsira Abulahamu ana kuchokera ku miyala iyi.
9 Ndithudi, nkhwangwa yaikidwa kale pamizu ya mitengo. Chotero mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa ndi kuponyedwa pamoto.”+
10 Ndiyeno khamu la anthu linali kumufunsa kuti: “Nanga tichite chiyani?”+
11 Poyankha iye anali kuwauza kuti: “Munthu amene ali ndi malaya awiri amkati agawireko munthu amene alibiretu. Amenenso ali ndi chakudya achite chimodzimodzi.”+
12 Okhometsa msonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa, ndipo anali kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, tichite chiyani?”+
13 Iye anali kuwauza kuti: “Musamalipiritse anthu zochuluka kuposa msonkho woikidwa.”+
14 Komanso, asilikali anali kumufunsa kuti: “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anali kuwauza kuti: “Musamavutitse anthu kapena kunamizira+ aliyense, koma muzikhutira ndi zimene mumalandira.”+
15 Tsopano pamene anthu anali kuyembekezera Khristu, ndipo onse anali kuganiza m’mitima yawo za Yohane kuti: “Kodi Khristu uja si ameneyu?”+
16 Yohane anawayankha onsewo kuti: “Inetu ndikukubatizani m’madzi. Koma wina wamphamvu kuposa ine akubwera, amene ine sindili woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.+ Iyeyu adzakubatizani ndi mzimu woyera ndi moto.+
17 Fosholo yake youluzira mankhusu* ili m’manja mwake. Akufuna kuyeretseratu mbee! malo ake opunthirapo mbewu ndi kututira+ tirigu munkhokwe yake. Koma mankhusu+ adzawatentha ndi moto+ umene sungazimitsidwe.”
18 Iye anaperekanso malangizo ena ambiri ndi kupitiriza kulengeza uthenga wabwino kwa anthu.
19 Ndiyeno popeza kuti Yohane anadzudzula Herode wolamulira chigawo, pa nkhani yokhudza Herodiya, mkazi wa m’bale wake, komanso chifukwa cha zoipa zonse zimene Herode anachita,+
20 Herode anawonjezera choipa china pa zonsezo: Anatsekera Yohane m’ndende.+
21 Pamene anthu onse anali kubatizidwa, Yesu+ nayenso anabatizidwa. Ndipo pamene anali kupemphera, kumwamba+ kunatseguka.
22 Pamenepo mzimu woyera wooneka ngati nkhunda unatsika kudzamutera. Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba, akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.”+
23 Pamene Yesu anayamba ntchito yake,+ anali ndi zaka pafupifupi 30.+ Anthu ankakhulupirira kuti Yesu analimwana+ wa Yosefe,+mwana wa Heli,
24 mwana wa Matati,mwana wa Levi,mwana wa Meliki,mwana wa Yananai,mwana wa Yosefe,
25 mwana wa Matatiyo,mwana wa Amosi,mwana wa Nahumu,mwana wa Esili,mwana wa Nagai,
26 mwana wa Maati,mwana wa Matatiyo,mwana wa Semeini,mwana wa Yoseki,mwana wa Yoda,
27 mwana wa Yoanani,mwana wa Resa,mwana wa Zerubabele,+mwana wa Salatiyeli,+mwana wa Neri,
28 mwana wa Meliki,mwana wa Adi,mwana wa Kosamu,mwana wa Elimadama,mwana wa Ere,
29 mwana wa Yesu,*mwana wa Eliezere,mwana wa Yorimu,mwana wa Matati,mwana wa Levi,
30 mwana wa Sumeoni,mwana wa Yudasi,mwana wa Yosefe,mwana wa Yonamu,mwana wa Eliyakimu,
31 mwana wa Meleya,mwana wa Mena,mwana wa Matata,mwana wa Natani,+mwana wa Davide,+
32 mwana wa Jese,+mwana wa Obedi,+mwana wa Boazi,+mwana wa Salimoni,+mwana wa Naasoni,+
33 mwana wa Aminadabu,+mwana wa Arini,+mwana wa Hezironi,+mwana wa Perezi,+mwana wa Yuda,+
34 mwana wa Yakobo,+mwana wa Isaki,+mwana wa Abulahamu,+mwana wa Tera,+mwana wa Nahori,+
35 mwana wa Serugi,+mwana wa Reu,+mwana wa Pelegi,+mwana wa Ebere,+mwana wa Shela,+
36 mwana wa Kainani,mwana wa Aripakisadi,+mwana wa Semu,+mwana wa Nowa,+mwana wa Lameki,+
37 mwana wa Metusela,+mwana wa Inoki,+mwana wa Yaredi,+mwana wa Mahalaliyeli,+mwana wa Kainani,+
38 mwana wa Enosi,+mwana wa Seti,+mwana wa Adamu,+mwana wa Mulungu.
Mawu a M'munsi
^ “Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
^ Dzina limene talimasulira pano kuti “Yesu,” mipukutu ina yakale imati “Yose.”