Luka 11:1-54
11 Tsopano Yesu anali kupemphera pamalo enaake. Atatsiriza, mmodzi wa ophunzira ake anamuuza kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera,+ ngati mmene Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”+
2 Pamenepo iye anawauza kuti: “Mukamapemphera+ muzinena kuti, ‘Atate, dzina lanu liyeretsedwe.+ Ufumu wanu ubwere.+
3 Mutipatse chakudya+ chathu chalero malinga ndi chakudya chofunika pa tsikuli.
4 Ndipo mutikhululukire machimo athu,+ pakuti nafenso timakhululukira aliyense amene amatilakwira.*+ Komanso musatilowetse m’mayesero.’”+
5 Kenako anawauza kuti: “Ndani wa inu amene ali ndi bwenzi lake kumene angapite pakati pa usiku kukam’pempha kuti, ‘Bwanawe, ndibwerekeko mitanda itatu ya mkate,
6 chifukwa mnzanga wangofika kumene kuchokera ku ulendo ndipo ndilibe chomupatsa’?
7 Ndiyeno ali m’nyumbayo n’kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine.+ Takhoma kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona kale. Sindingadzukenso kuti ndikupatse kanthu.’
8 Ndithu ndikukuuzani, Adzadzuka ndi kum’patsa zonse zimene akufuna, osati chifukwa chakuti ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha kukakamira kwake.+
9 Choncho ndikukuuzani, Pemphanibe,+ ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna,+ ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.
10 Pakuti aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzam’tsegulira.
11 Kodi kapena pakati panu alipo bambo amene mwana wake+ atam’pempha nsomba, angam’patse njoka m’malo mwa nsomba?
12 Kapena atam’pempha dzira iye angam’patse chinkhanira?
13 Choncho ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu+ mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera+ kwa amene akum’pempha.”
14 Nthawi inayake anali kutulutsa chiwanda cholepheretsa munthu kulankhula.+ Chiwandacho chitatuluka, munthu wosalankhulayo analankhula, ndipo khamu la anthu linadabwa kwambiri.
15 Koma ena mwa iwo anati: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule* wolamulira wa ziwanda.”+
16 Koma ena pofuna kumuyesa, anayamba kumupempha kuti awasonyeze chizindikiro+ chochokera kumwamba.
17 Podziwa maganizo awo,+ iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha, ndipo nyumba yogawanika imagwa.+
18 Choncho ngati Satana wagawanika, ufumu wake ungalimbe bwanji?+ Chifukwa inu mukuti ndikutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule.
19 Ngati ndikutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule, kodi otsatira anu+ akuzitulutsa ndi chiyani? Pa chifukwa chimenechi iwo adzakuweruzani.
20 Koma ngati ziwandazo ndikuzitulutsa ndi chala cha Mulungu,+ ndiye kuti ufumu wa Mulungu wakufikiranidi modzidzimutsa.+
21 Munthu wamphamvu,+ wokhala ndi zida zokwanira, akamalondera nyumba yake, chuma chake chimatetezeka.
22 Koma wina wamphamvu kuposa iyeyu+ akabwera n’kumugonjetsa,+ amamulanda zida zake zonse zimene amadalira, ndipo katundu amene wamulanda, amamugawa kwa ena.
23 Amene sali kumbali yanga akutsutsana ndi ine, ndipo amene sasonkhanitsa anthu pamodzi ndi ine amawabalalitsa.+
24 “Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa m’malo ouma kufunafuna malo okhala, koma akapanda kupezeka, umanena kuti, ‘Ndibwerera m’nyumba yanga mmene ndinatuluka muja.’+
25 Tsopano ukafikamo umapeza muli mosesa bwino komanso mokongola.
26 Kenako umapita kukatenga mizimu ina 7+ yoipa kwambiri kuposa umenewu, ndipo ikalowa mkatimo, imakhala mmenemo. Potsirizira pake zochita za munthu ameneyu zimakhala zoipa kwambiri kuposa poyamba paja.”+
27 Pamene anali kunena mawu amenewa, mayi wina m’khamu la anthulo anafuula n’kumuuza kuti: “Ndi wodala mayi+ amene mimba yake inanyamula inu ndiponso amene munayamwa mabere ake!”
28 Koma iye anati: “Ayi, m’malomwake, Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”+
29 Pamene anthu osonkhana pamodzi anali kuchulukirachulukira, iye anayamba kunena kuti: “M’badwo uwu ndi m’badwo woipa, ukufuna chizindikiro.+ Koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.+
30 Monga momwe Yona+ anakhalira chizindikiro kwa anthu a ku Nineve, Mwana wa munthu adzakhalanso chizindikiro ku m’badwo uwu.
31 Mfumukazi+ ya kum’mwera adzaiimiritsa pa chiweruzo limodzi ndi anthu a m’badwo uwu, ndipo idzawatsutsa. Chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa+ Solomo ali pano.
32 Anthu a ku Nineve adzaimirira pa chiweruzo limodzi ndi m’badwo uwu ndipo adzautsutsa. Chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa+ Yona ali pano.
33 Munthu akayatsa nyale saiika m’chipinda cha pansi kapena kuivundikira ndi dengu, koma amaiika pachoikapo nyale,+ kuti onse olowa aone kuwala.
34 Nyale ya thupi ndi diso lako. Ngati diso lako lili lolunjika pa chinthu chimodzi, thupi lako lonse limawala kwambiri.+ Koma ngati lili loipa, thupi lako limachita mdima.
35 Chotero khala tcheru. Mwina kuwala kumene kuli mwa iwe ndiko mdima.+
36 Choncho ngati thupi lako lonse lili lowala kwambiri, popanda mbali ina yamdima, thupi lonse lidzawala kwambiri+ ngati mmene nyale imachitira pokuunikira ndi kuwala kwake.”
37 Atalankhula zimenezi, Mfarisi wina anam’pempha kuti akadye naye.+ Choncho iye anapitadi kukadya chakudya.
38 Koma Mfarisiyo anadabwa kuona kuti anayamba kudya chakudyacho asanasambe.+
39 Choncho Ambuye anamuuza kuti: “Inu Afarisi mumayeretsa kunja kwa kapu ndi mbale, koma mkati+ mwanu mwadzaza maganizo ofuna kulanda zinthu za anthu ndi kuchita zinthu zoipa.+
40 Anthu opanda nzeru inu! Amene anapanga kunja+ anapanganso mkati, si choncho kodi?
41 Koma inu, perekani zimene zili mkati monga mphatso zachifundo,+ mukatero zina zonse zokhudza inuyo zidzakhala zoyera.
42 Tsoka inu Afarisi, chifukwa mumapereka chakhumi+ cha timbewu ta minti ndi ta luwe, ndi cha mbewu zakudimba zamtundu uliwonse. Koma mumanyalanyaza chilungamo ndi chikondi cha Mulungu! Unalidi udindo wanu kuchita zinthu zimenezi, koma simunayenera kusiya zinazo.+
43 Tsoka inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yakutsogolo m’masunagoge ndi kupatsidwa moni m’misika!+
44 Tsoka inu, chifukwa muli ngati manda achikumbutso osaonekera, moti anthu amayenda pamwamba pake koma osadziwa!”+
45 Poyankha wina wodziwa+ Chilamulo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, izi mukunenazi mukunyoza ndi ife tomwe.”
46 Pamenepo iye anati: “Tsoka inunso odziwa Chilamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wovuta kunyamula, koma inuyo simukhudza katunduyo ngakhale ndi chala chokha!+
47 “Tsoka inu, chifukwa mumamanga manda achikumbutso a aneneri, komatu makolo anu ndi amene anawapha!+
48 Mosakayikira, ndinu mboni pa zimene makolo anu anachita. Ndipo mukugwirizana+ nawonso, chifukwa iwo anapha+ aneneri, pamene inu mukumanga manda awo.
49 Pa nkhani imeneyi, nzeru+ ya Mulungu inanenanso kuti, ‘Ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, koma iwo adzapha ndi kuzunza ena mwa iwo.
50 N’chifukwa chake m’badwo uwu udzafunsidwa za magazi a aneneri,+ okhetsedwa kuchokera pamene dziko linakhazikika.+
51 Kuyambira magazi a Abele+ mpaka magazi a Zekariya,+ amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi nyumba yopatulika.’+ Inde, ndikukuuzani, m’badwo uwu udzafunsidwa za magazi amenewo.
52 “Tsoka inu odziwa Chilamulo, chifukwa munalanda anthu kiyi yowathandiza kudziwa zinthu.+ Inuyo simunalowemo, ndipo ofuna kulowamo munawatsekereza!”+
53 Choncho atachoka kumeneko, alembi ndi Afarisi anayamba kumuunjirira koopsa ndi kum’panikiza ndi mafunso okhudza zinthu zina.
54 Anali kuyembekezera+ kumva mawu oti amutape nawo m’kamwa.+