Chivumbulutso 21:1-27
21 Tsopano ndinaona kumwamba+ kwatsopano ndi dziko lapansi+ latsopano, pakuti kumwamba+ kwakale ndi dziko lapansi lakale+ zinali zitachoka, ndipo kulibenso nyanja.+
2 Ndinaonanso mzinda woyera,+ Yerusalemu Watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba+ kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi+ wokongoletsedwera mwamuna wake.+
3 Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Taonani! Chihema+ cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo,+ ndipo iwo adzakhala anthu ake.+ Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.+
4 Iye adzapukuta misozi+ yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.+ Sipadzakhalanso kulira,+ kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”+
5 Ndipo wokhala pampando wachifumu+ anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.”+ Ananenanso kuti: “Lemba, pakuti mawu awa ndi odalirika ndi oona.”
6 Anandiuzanso kuti: “Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi mapeto.+ Aliyense womva ludzu, ndidzamupatsa madzi a m’kasupe wa moyo kwaulere.+
7 Aliyense wopambana pa nkhondo adzalandira zimenezi monga cholowa. Ineyo ndidzakhala Mulungu wake,+ ndipo iye adzakhala mwana wanga.+
8 Koma amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa,+ opha anthu,+ adama,+ ochita zamizimu, opembedza mafano,+ ndi onse abodza,+ gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto+ ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+
9 Ndipo kunabwera mmodzi wa angelo 7 aja, amene anali ndi mbale 7 zodzaza ndi miliri+ 7 yotsiriza. Iye anandiuza kuti: “Bwera kuno ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.”+
10 Choncho, mu mphamvu ya mzimu, ananditengera kuphiri lalikulu ndi lalitali,+ ndipo anandionetsa mzinda woyera,+ Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu,+
11 uli ndi ulemerero wa Mulungu.+ Unali wonyezimira ngati mwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi.+
12 Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali,+ ndipo unali ndi zipata 12. Pazipatazo panali angelo 12, ndipo panalembedwa mayina a mafuko 12 a ana a Isiraeli.+
13 Kum’mawa kwa mzindawo kunali zipata zitatu, kumpoto zipata zitatu, kum’mwera zipata zitatu, ndipo kumadzulo kwake zipata zitatu.+
14 Mpanda wa mzindawo unalinso ndi miyala yomangira maziko+ yokwana 12, ndipo pamiyalayo panali mayina 12 a atumwi 12+ a Mwanawankhosa.
15 Tsopano amene anali kundilankhula uja ananyamula bango+ lagolide loyezera, kuti ayeze mzindawo, zipata zake, ndi mpanda wake.+
16 Mzindawo unali ndi mbali zinayi zofanana kutalika kwake. M’litali mwake n’chimodzimodzi ndi m’lifupi mwake. Mngeloyo anayeza mzindawo+ ndi bangolo, ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000* kuuzungulira. M’litali mwake, m’lifupi mwake, ndi msinkhu wake, n’zofanana.
17 Anayezanso mpanda wake, ndipo unali wautali mikono 144,* malinga ndi muyezo wa munthu, umene ulinso wofanana ndi muyezo wa mngelo.
18 Mpandawo unali womangidwa ndi mwala wa yasipi,+ ndipo mzindawo unali womangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi.
19 Maziko+ a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yonse:+ maziko oyamba anali amwala wa yasipi,+ achiwiri wa safiro,+ achitatu wa kalikedo, achinayi wa emarodi,+
20 achisanu wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito,+ a 8 wa belulo, a 9 wa topazi,+ a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto, ndipo a 12, wa ametusito.*+
21 Komanso zitseko za pazipata 12 zija zinali ngale 12. Chitseko chilichonse chinali ngale imodzi.+ Ndipo msewu waukulu wa mumzindawo unali wopangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi.
22 Sindinaone kachisi mumzindawo,+ pakuti Yehova+ Mulungu Wamphamvuyonse+ ndiye anali kachisi+ wake, komanso Mwanawankhosa ndiye kachisi wake.+
23 Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, pakuti ulemerero wa Mulungu unauwalitsa,+ ndipo nyale yake inali Mwanawankhosa.+
24 Mitundu ya anthu idzayenda mwa kuwala kwake,+ ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mumzindawo.+
25 Zipata zake sizidzatsekedwa n’komwe masana,+ ndipo usiku sudzakhalako.+
26 Iwo adzabweretsa ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu mumzindawo.+
27 Koma chilichonse chosapatulika, ndi aliyense wochita zonyansa+ ndiponso wabodza,+ sadzalowa mumzindawo.+ Amene adzalowemo ndi okhawo olembedwa mumpukutu wa moyo, umene ndi wa Mwanawankhosa.+
Mawu a M'munsi
^ Mamita pafupifupi 64.
^ Yonseyi ndi miyala yamtengo wapatali yamitundu yosiyanasiyana, ndipo ina ndi yokhala ndi mitundu ingapo yosiyana m’mwala umodzi.