Chivumbulutso 8:1-13

8  Atamatula+ chidindo cha 7,+ kumwamba kunangoti chete! pafupifupi hafu ya ola.  Kenako ndinaona angelo 7+ ataimirira pamaso pa Mulungu, ndipo anapatsidwa malipenga 7.  Mngelo wina anafika ndi kuimirira kuguwa+ lansembe. Iye anali ndi chiwiya chofukiziramo chagolide, ndipo anamupatsa zofukiza zambiri+ kuti azipereke nsembe limodzi ndi mapemphero a oyera onse paguwa lansembe lagolide, limene linali pamaso pa mpando wachifumu.  Pamenepo, utsi wa zofukizazo unakwera pamaso pa Mulungu kuchokera m’dzanja la mngeloyo limodzi ndi mapemphero+ a oyera.  Koma nthawi yomweyo, mngeloyo anatenga chiwiya chofukiziramo chija, n’kudzazamo moto+ umene anapala paguwa lansembe, ndi kuuponyera kudziko lapansi.+ Ndiyeno kunagunda mabingu,+ kunamveka mawu, ndipo kunachita mphezi+ ndi chivomezi.+  Angelo 7 okhala ndi malipenga+ 7+ aja, anakonzekera kuliza malipengawo.  Mngelo woyamba analiza lipenga lake. Atatero, panaoneka matalala ndi moto,+ zosakanikirana ndi magazi. Zimenezi zinaponyedwa kudziko lapansi. Ndipo gawo limodzi mwa magawo atatu a dziko lapansi linapsa.+ Kuwonjezera pamenepo, gawo limodzi mwa magawo atatu a mitengo linapsa, komanso zomera zonse zobiriwira+ zinapsa.  Kenako mngelo wachiwiri analiza lipenga lake. Ndipo chinachake chokhala ngati phiri lalikulu+ limene likuyaka moto chinaponyedwa m’nyanja.+ Moti gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja, linasanduka magazi.+  Ndipo gawo limodzi mwa magawo atatu a zolengedwa zamoyo zimene zili m’nyanja zinafa.+ Komanso gawo limodzi mwa magawo atatu a ngalawa, linasweka. 10  Tsopano mngelo wachitatu analiza lipenga lake. Ndipo nyenyezi yaikulu yoyaka ngati nyale inagwa kuchokera kumwamba.+ Inagwera pa gawo limodzi mwa magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe a madzi.+ 11  Dzina la nyenyeziyo ndi Chitsamba Chowawa. Choncho gawo limodzi mwa magawo atatu a madzi linakhala lowawa, ndipo anthu ambiri anafa ndi madziwo chifukwa anali owawa.+ 12  Ndiyeno mngelo wachinayi analiza lipenga lake. Atatero, gawo limodzi mwa magawo atatu a dzuwa linakanthidwa. Chimodzimodzinso gawo limodzi mwa magawo atatu a mwezi, ndi a nyenyezi. Zinatero kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a zimenezi lichite mdima, ndi kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a usana+ lisalandire kuunika,+ chimodzimodzinso usiku. 13  Ndipo ndinaona ndi kumva chiwombankhanga+ chikuuluka pafupi m’mlengalenga,+ chikulankhula ndi mawu okweza kuti: “Tsoka, tsoka, tsoka+ kwa okhala padziko lapansi, chifukwa cha malipenga otsalawo, amene angelo atatuwo atsala pang’ono kuwaliza!”+

Mawu a M'munsi