Chivumbulutso 19:1-21

19  Zimenezi zitatha, ndinamva mawu ofuula kumwamba+ ngati mawu a khamu lalikulu, akuti: “Tamandani Ya,* anthu inu!+ Chipulumutso,+ ulemerero, ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,+  chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama.+ Pakuti iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi dama* lake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.”+  Nthawi yomweyo, ananenanso kachiwiri kuti: “Tamandani Ya, anthu inu!+ Utsi wochokera kwa iye udzafuka kwamuyaya.”+  Ndipo akulu+ 24 ndi zamoyo zinayi zija,+ anagwada pansi ndi kuwerama, n’kulambira Mulungu wokhala+ pampando wachifumu, ndi mawu akuti: “Ame! Tamandani Ya,+ anthu inu!”  Komanso, kunamveka mawu ochokera kumpando wachifumu akuti: “Muzitamanda Mulungu wathu, inu nonse akapolo+ ake, inu omuopa, olemekezeka ndi onyozeka omwe.”+  Kenako ndinamva mawu ngati a khamu lalikulu, omveka ngati mkokomo wa madzi ambiri ndi mabingu amphamvu. Mawuwo anati: “Tamandani Ya,+ anthu inu, chifukwa Yehova* Mulungu wathu, Wamphamvuyonse,+ wayamba kulamulira monga mfumu.+  Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Timupatse ulemerero,+ chifukwa ukwati+ wa Mwanawankhosa wafika,+ ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.+  Iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.”+  Mngeloyo anandiuza kuti: “Lemba: Odala ndiwo amene aitanidwa+ ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwati+ wa Mwanawankhosa.” Anandiuzanso kuti: “Awa ndi mawu oona a Mulungu.”+ 10  Pamenepo ndinagwada pansi n’kuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire.+ Koma iye anandiuza kuti:+ “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.+ Lambira Mulungu,+ pakuti kuchitira umboni za Yesu ndiko cholinga cha maulosi.”+ 11  Ndipo nditayang’ana ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera.+ Wokwerapo wake dzina lake linali Wokhulupirika+ ndi Woona.+ Iyeyo anali kuweruza ndi kumenya nkhondo mwachilungamo.+ 12  Maso ake anali ngati lawi la moto+ ndipo pamutu pake panali zisoti zachifumu+ zambiri. Anali ndi dzina+ lolembedwa limene wina aliyense sanali kulidziwa, koma iye yekha. 13  Iye anavala malaya akunja owazidwa magazi,+ ndipo dzina limene anali kutchedwa nalo linali lakuti Mawu+ a Mulungu. 14  Komanso magulu ankhondo amene anali kumwamba, anali kumutsatira pamahatchi oyera, atavala zovala zapamwamba, zoyera bwino, za mbee! 15  M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga+ lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.+ Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa+ cha mkwiyo waukulu wa Mulungu+ Wamphamvuyonse. 16  Pamalaya ake akunja, ngakhale pantchafu yake, anali ndi dzina lolembedwa lakuti, Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.+ 17  Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame+ zonse zouluka chapafupi m’mlengalenga, kuti: “Bwerani kuno, dzasonkhaneni ku phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo, 18  kuti mudzadye minofu+ ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu,+ ya mahatchi+ ndi ya okwerapo ake, ndi minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.” 19  Ndipo ndinaona chilombo,+ mafumu+ a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane+ ndi wokwera pahatchi+ uja ndi gulu lake lankhondo. 20  Koma chilombocho+ chinagwidwa limodzi ndi mneneri+ wonyenga uja, amene anachita zizindikiro+ pamaso pa chilombocho. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo olandira chizindikiro+ cha chilombo ndi olambira chifaniziro chake.+ Adakali amoyo, onse awiri anaponyedwa m’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule.+ 21  Koma ena onse anaphedwa ndi lupanga lalitali la wokwera pahatchi,+ limene linatuluka m’kamwa mwake lija.+ Ndipo mbalame+ zonse zinakhuta+ minofu yawo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya.” Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.
Onani Zakumapeto 7.
Onani Zakumapeto 2.