Chivumbulutso 13:1-18

13  Ndiyeno chinjokacho chinangoima pamchenga+ wa m’mbali mwa nyanja. Kenako ndinaona chilombo+ chikutuluka m’nyanja.+ Chinali ndi nyanga 10+ ndi mitu 7.+ Kunyanga yake iliyonse kunali chisoti chachifumu. Koma pamitu yake panali mayina onyoza Mulungu.+  Chilombo chimene ndinaonacho chinali ngati nyalugwe,+ koma mapazi ake anali ngati a chimbalangondo,+ ndipo pakamwa pake panali ngati pa mkango.+ Chinjoka+ chija chinapatsa chilombocho mphamvu yake, mpando wake wachifumu, komanso ulamuliro wake waukulu.+  Ndiyeno ndinaona mutu wake umodzi ukuoneka kuti wavulazidwa kwambiri. Koma ngakhale kuti balalo linali loti chikanafa nalo,+ linapola. Ndipo dziko lonse lapansi linatsatira chilombocho pochita nacho chidwi.  Iwo analambira chinjoka chija chifukwa chinapatsa chilombo ulamuliro. Ndipo analambira chilombocho ndi mawu awa: “Ndani ali ngati chilombo, ndipo ndani angamenyane nacho?”  Chilombocho chinapatsidwa pakamwa polankhula zinthu zodzitukumula+ ndi zonyoza.+ Chinapatsidwanso mphamvu yochita ulamuliro kwa miyezi 42.+  Chilombocho chinatsegula pakamwa pake n’kumanyoza Mulungu,+ dzina lake ndi malo ake okhala, ndiponso amene akukhala kumwamba.+  Chinaloledwa+ kuchita nkhondo ndi oyerawo ndi kuwagonjetsa.+ Chinapatsidwanso ulamuliro pa anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chinenero chilichonse ndi dziko lililonse.  Ndipo onse okhala padziko lapansi adzachilambira. Anthu onsewa mayina awo sanalembedwe mumpukutu+ wa moyo, umene Mwanawankhosa amene anaphedwa,+ ndiye mwiniwake. Mpukutuwo unakonzedwa kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.+  Aliyense amene ali ndi makutu amve.+ 10  Ngati wina akuyenera kutengedwa ukapolo, adzapitadi ku ukapoloko.+ Ngati wina adzapha ndi lupanga, adzaphedwa ndi lupanga.+ Apa m’pamene oyera+ akufunika kupirira+ ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro.+ 11  Kenako ndinaona chilombo+ china chikutuluka pansi pa dziko lapansi.+ Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa, koma chinayamba kulankhula ngati chinjoka.+ 12  Chilombocho chinalamulira ndi mphamvu zonse za chilombo choyambacho+ pamaso pa chilombo choyambacho. Chinachititsa dziko lapansi ndi okhalamo kulambira chilombo choyamba chija, chimene bala lake limene chinayenera kufa nalo, linapola.+ 13  Chinachitanso zizindikiro zazikulu,+ moti chinapangitsa ngakhale moto kugwera padziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuona. 14  Chilombocho chinasocheretsa okhala padziko lapansi chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Ndipo chinauza okhala padziko lapansi kupanga chifaniziro+ cha chilombo chimene chinali ndi bala la lupanga+ chija, koma chimene chinapulumuka. 15  Ndipo chinaloledwa kupereka mpweya ku chifaniziro cha chilombo chija, kuti chifaniziro cha chilombocho chithe kulankhula, ndi kuchititsa kuti onse amene mwa njira iliyonse salambira chifaniziro+ cha chilombocho, aphedwe. 16  Chilombocho chinakakamiza anthu onse,+ olemekezeka ndi onyozeka, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti apatsidwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo.+ 17  Chinachita izi kuti aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi chizindikirocho, dzina+ la chilombo, kapena nambala ya dzina lake.+ 18  Apa ndiye pofunika nzeru: Amene ali ndi nzeru awerengere nambala ya chilombocho, pakuti ndi nambala ya munthu.+ Nambala yake ndi 666.+

Mawu a M'munsi