Chivumbulutso 1:1-20
1 Chivumbulutso+ choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa,+ kuti aonetse akapolo ake+ zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.+ Yesuyo anatumiza mngelo wake+ kuti adzapereke Chivumbulutsocho mwa zizindikiro+ kwa kapolo wake Yohane.+
2 Yohaneyo anachitira umboni mawu a Mulungu,+ ndiponso umboni umene Yesu Khristu anapereka,+ kutanthauza zonse zimene anaona.
3 Wodala+ ndi munthu amene amawerenga mokweza,+ ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu,+ komanso amene akusunga zolembedwamo,+ pakuti nthawi yoikidwiratu ili pafupi.+
4 Ine Yohane, ndikulembera mipingo 7+ ya m’chigawo cha Asia.
Kukoma mtima kwakukulu, ndi mtendere zikhale nanu kuchokera kwa “Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,”+ ndiponso kuchokera kwa mizimu 7+ yokhala pamaso pa mpando wake wachifumu.
5 Komanso, kuchokera kwa Yesu Khristu, “Mboni Yokhulupirika,”+ “Woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,”+ ndiponso “Wolamulira wa mafumu a dziko lapansi.”+
Kwa iye amene amatikonda,+ amenenso anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake enieniwo,+
6 n’kutipanga kukhala mafumu+ ndi ansembe+ kwa Mulungu wake ndi Atate wake, kwa iyeyo kukhale ulemerero ndi mphamvu kwamuyaya.+ Ame.
7 Taonani! Akubwera ndi mitambo,+ ndipo diso lililonse lidzamuona,+ ngakhalenso anthu amene anamulasa.+ Ndipo mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye.+ Ame.
8 “Ine ndine Alefa ndi Omega,”*+ akutero Yehova Mulungu, “Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,+ Wamphamvuyonse.”+
9 Ine Yohane, m’bale wanu ndi wogawana nanu masautso+ a Yesu,+ mu ufumu+ ndi m’kupirira,+ ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.+
10 Mwa mzimu,+ ndinapezeka kuti ndili+ m’tsiku la Ambuye,+ ndipo kumbuyo kwanga ndinamva mawu amphamvu+ ngati kulira kwa lipenga.
11 Mawuwo anali akuti: “Zimene uone, lemba+ mumpukutu ndi kuutumiza kumipingo 7+ yotsatirayi: wa ku Efeso,+ wa ku Simuna,+ wa ku Pegamo,+ wa ku Tiyatira,+ wa ku Sade,+ wa ku Filadefiya,+ ndi wa ku Laodikaya.”+
12 Ndinacheuka kuti ndione, kuti ndani amene anali kundilankhula. Nditacheuka, ndinaona zoikapo nyale 7 zagolide.+
13 Pakati pa zoikapo nyalezo, panali wina wooneka ngati mwana wa munthu+ atavala chovala chofika kumapazi, atamanga lamba wagolide pachifuwa.
14 Komanso, mutu ndi tsitsi lake zinali zoyera+ ngati ubweya wa nkhosa woyera, zoyera kwambiri kuti mbee! Ndipo maso ake anali ngati lawi la moto.+
15 Mapazi ake anali ngati mkuwa woyengedwa+ bwino ukamanyezimira m’ng’anjo, ndipo mawu+ ake anali ngati mkokomo wa madzi ambiri.
16 M’dzanja lake lamanja anali ndi nyenyezi 7.+ M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse.+ Nkhope yake inali yowala ngati dzuwa limene likuwala kwambiri.+
17 Nditamuona, ndinagwa pamapazi ake ngati kuti ndafa.
Ndipo anandigwira ndi dzanja lake lamanja ndi kundiuza kuti: “Usachite mantha.+ Ine ndine Woyamba+ ndi Wotsiriza,+
18 ndiponso wamoyo.+ Ndinali wakufa,+ koma taona, ndili ndi moyo kwamuyaya,+ ndipo ndili ndi makiyi a imfa+ ndi a Manda.*+
19 Choncho lemba zimene waona, zimene zikuchitika panopa, ndi zimene zidzachitike pambuyo pa zimenezi.+
20 Koma za chinsinsi chopatulika cha nyenyezi 7,+ zimene waona m’dzanja langa lamanja, ndi za chinsinsi cha zoikapo nyale 7 zagolide,+ tanthauzo lake ndi ili: Nyenyezi 7, zikuimira angelo* a mipingo 7, ndipo zoikapo nyale 7, zikuimira mipingo 7.+