Chivumbulutso 9:1-21

9  Kenako mngelo wachisanu analiza lipenga+ lake. Ndipo ndinaona nyenyezi+ imene inagwera kudziko lapansi kuchokera kumwamba. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi+ wa dzenje+ lolowera kuphompho.  Pamene inatsegula dzenje lolowera kuphompholo, utsi+ ngati wa m’ng’anjo yaikulu+ unatuluka m’dzenjemo, ndipo dzuwa ndi mpweya zinada+ ndi utsi wa m’dzenjewo.  Mu utsiwo, munatuluka dzombe+ n’kubwera padziko lapansi. Dzombelo linapatsidwa ulamuliro wofanana ndi umene zinkhanira+ za padziko lapansi zili nawo.  Ndipo linauzidwa kuti lisawononge zomera za padziko lapansi, kapena chilichonse chobiriwira, kapena mtengo uliwonse, koma livulaze anthu okhawo amene alibe chidindo cha Mulungu pamphumi pawo.+  Dzombelo silinaloledwe kupha anthuwo, koma linauzidwa kuti liwazunze+ miyezi isanu. Ndipo kuzunzika kwawo kunali kofanana ndi mmene munthu amazunzikira akalumidwa ndi chinkhanira.+  M’masiku amenewo, anthuwo adzafunafuna imfa,+ koma sadzaipeza. Adzalakalaka kufa, koma imfa izidzawathawa.  Dzombelo linali kuoneka ngati mahatchi+ okonzekera nkhondo. Pamitu pawo panali zinthu zooneka ngati zisoti zachifumu zokhala ngati zagolide. Nkhope zawo zinali ngati nkhope za amuna,+  koma tsitsi lawo linali ngati la akazi.+ Mano awo anali ngati a mikango.+  Pachifuwa pawo panali zotetezera+ zokhala ngati zachitsulo. Ndipo phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magaleta+ okokedwa ndi mahatchi ambiri omwe akuthamangira kunkhondo.+ 10  Dzombelo linali ndi michira ndi mbola ngati zinkhanira.+ M’michira yawoyo ndi mmene munali ulamuliro wawo wovulaza anthuwo kwa miyezi isanu. 11  Dzombelo lili ndi mfumu. Mfumuyo ndiye mngelo wa phompho.+ M’Chiheberi, dzina lake ndi Abadoni, koma m’Chigiriki ali ndi dzina lakuti Apoliyoni.+ 12  Tsoka limodzilo linapita. Koma masoka ena awiri+ anali kubwera pambuyo pa zimenezi. 13  Kenako mngelo wa 6+ analiza lipenga+ lake. Ndipo ndinamva mawu amodzi+ kuchokera panyanga za paguwa lansembe lagolide+ lokhala pamaso pa Mulungu. 14  Mawuwo anauza mngelo wa 6 amene anali ndi lipengayo kuti: “Masula angelo anayi+ omangidwa+ amene ali kumtsinje waukulu wa Firate.”+ 15  Angelo anayiwo anamasulidwa. Iwo anali okonzekera kuti pa ola, tsiku, mwezi, ndi chaka chimenecho, aphe gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu. 16  Ndipo chiwerengero cha makamu a asilikali okwera pamahatchi, chinali miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda.* Chimenechi ndicho chiwerengero chawo chimene ndinamva. 17  Mahatchi ndi okwerapowo ndinawaona motere m’masomphenyawo: Anavala zoteteza pachifuwa zofiira ngati moto, zobiriwira ngati mwala wa huwakinto, ndi zachikasu ngati sulufule. Mitu ya mahatchiwo inali ngati mitu ya mikango,+ ndipo m’kamwa mwawo munali kutuluka moto, utsi, ndi sulufule.+ 18  M’kamwa mwawomo munalinso kutuluka miliri itatu iyi: Moto, utsi, ndi sulufule, ndipo inapha gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu. 19  Ulamuliro wa mahatchiwo unali m’kamwa mwawo ndi m’michira yawo, pakuti michira yawo inali ngati njoka,+ ndipo inali ndi mitu. Zinthu zimenezi anali kuwononga nazo anthu. 20  Koma anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi, sanalape ntchito za manja awo.+ Sanalape kulambira ziwanda+ ndi mafano agolide, asiliva,+ amkuwa, amwala, ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva, kapena kuyenda.+ 21  Iwo sanalape ntchito zawo zopha anthu,+ zamizimu,+ dama lawo, ngakhalenso umbava wawo.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “20,000 kuchulukitsa ndi 10,000,” imene ndi 200 miliyoni. Onani mawu a m’munsi pa Chv 5:11.