Chivumbulutso 14:1-20

14  Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa+ ataimirira paphiri la Ziyoni.+ Limodzi naye panali enanso 144,000+ olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate+ wake pamphumi pawo.  Kenako ndinamva phokoso kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri,+ ndiponso ngati phokoso la bingu lamphamvu. Phokoso ndinamvalo linali ngati la oimba amene akuimba motsagana ndi azeze awo.+  Iwo anali kuimba+ nyimbo yokhala ngati yatsopano+ pamaso pa mpando wachifumu, pamaso pa zamoyo zinayi,+ ndi pamaso pa akulu.+ Palibe anatha kuiphunzira nyimboyo, koma 144,000+ amene anagulidwa+ padziko lapansi.  Awa ndiwo amene sanadziipitse ndi akazi,+ ndipo ali ngati anamwali.+ Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.+ Iwowa anagulidwa+ kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira+ zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.  M’kamwa mwawo simunapezeke chinyengo,+ ndipo alibe chilema.+  Ndinaona mngelo winanso akuuluka chapafupi m’mlengalenga.+ Iye anali ndi uthenga wabwino+ wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.+  Iye anali kunena mofuula kuti: “Opani Mulungu+ ndi kumupatsa ulemerero,+ chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika.+ Chotero lambirani Iye amene anapanga+ kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.”+  Kenako mngelo wina wachiwiri anamutsatira, ndipo anati: “Wagwa! Babulo+ Wamkulu wagwa,+ amene anachititsa mitundu yonse ya anthu kumwako vinyo+ wa mkwiyo wake ndi wa dama* lake!”+  Mngelo wina wachitatu anawatsatira, ndipo ananena mofuula kuti: “Ngati wina walambira chilombo+ ndi chifaniziro chake,+ ndipo walandira chizindikiro pamphumi kapena padzanja lake,+ 10  adzamwanso vinyo wosasungunula wa mkwiyo+ wa Mulungu amene akuthiridwa m’kapu ya mkwiyo wake. Ndipo adzazunzidwa+ ndi moto ndi sulufule+ pamaso pa angelo oyera, ndi pamaso pa Mwanawankhosa. 11  Ndipo utsi wa kuzunzidwa kwawo udzafuka kwamuyaya.+ Amene anali kulambira chilombo ndi chifaniziro chake, ndiponso aliyense amene walandira chizindikiro+ cha dzina lake, sadzapuma usana ndi usiku. 12  Kwa oyerawo,+ amene akusunga malamulo a Mulungu+ ndi kutsatira chikhulupiriro+ cha Yesu, apa ndiye pofunika kupirira.” 13  Kenako ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti: “Lemba: Odala ndiwo anthu amene akufa+ mwa Ambuye+ kuyambira pa nthawi ino kupita m’tsogolo.+ Mzimu ukuti, alekeni akapumule ku ntchito yawo imene anaigwira mwakhama, pakuti zimene anachita zikupita nawo limodzi.” 14  Nditayang’ana, ndinaona mtambo woyera. Pamtambopo panakhala winawake ngati mwana wa munthu,+ atavala chisoti chachifumu chagolide+ kumutu kwake, chikwakwa chakuthwa chili m’dzanja lake. 15  Mngelo wina anatuluka m’nyumba yopatulika ya pakachisi, akufuula kwa wokhala pamtambo uja ndi mawu okweza, kuti: “Tsitsa chikwakwa chako ndi kuyamba kumweta,+ chifukwa ola la kumweta lafika.+ Pakuti zokolola za padziko lapansi zapsa bwino.”+ 16  Choncho wokhala pamtambo uja anatsitsira chikwakwa chake chija kudziko lapansi mwamphamvu, ndipo anamweta dziko lapansi. 17  Mngelo winanso anatuluka m’nyumba yopatulika ya pakachisi amene ali kumwamba,+ nayenso ali ndi chikwakwa chakuthwa. 18  Ndipo mngelo winanso anatuluka kuguwa lansembe. Iyeyu anali ndi ulamuliro pa moto.+ Anafuula kwa mngelo amene anali ndi chikwakwa chakuthwa uja ndi mawu okweza, akuti: “Tsitsa chikwakwa chako chakuthwacho umwete mpesa wa padziko lapansi,+ ndi kusonkhanitsa pamodzi masango a mphesa zake, chifukwa mphesa zakezo zapsa.” 19  Mngeloyo+ anatsitsira chikwakwa chake kudziko lapansi mwamphamvu, ndi kumweta mpesa+ wa padziko lapansi. Ndiyeno anauponya m’choponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu.+ 20  Ndipo anapondaponda mopondera mphesamo kunja kwa mzinda,+ ndipo magazi anatuluka m’choponderamo mphesacho mpaka kufika m’zibwano za mahatchi,+ n’kuyenderera mtunda wa masitadiya 1,600.*+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.
Makilomita 296. “Sitadiya” ndi muyezo wakale wachigiriki woyezera mtunda. “Sitadiya” imodzi ndi yofanana ndi mamita 185.