Chivumbulutso 18:1-24
18 Zimenezi zitatha, ndinaona mngelo wina akutsika kumwamba wokhala ndi ulamuliro+ waukulu. Ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero wake.+
2 Iye anafuula ndi mawu amphamvu,+ akuti: “Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa,+ ndipo wakhala malo okhala ziwanda, ndiponso obisalamo mpweya+ uliwonse wonyansa wotuluka m’kamwa, komanso obisalamo mbalame iliyonse yonyansa ndi yodedwa.+
3 Iye wamwetsa mitundu yonse ya anthu+ vinyo wa mkwiyo, vinyo wa dama lake. Ndipo mafumu a dziko lapansi anachita naye dama.+ Amalonda oyendayenda+ a padziko lapansi analemera chifukwa cha zinthu zambiri zamtengo wapatali zimene mkazi ameneyu anadziunjikira mopanda manyazi.”+
4 Ndipo ndinamva mawu ena kumwamba, akuti: “Tulukani mwa iye anthu anga,+ ngati simukufuna kugawana naye machimo ake,+ ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.
5 Pakuti machimo ake aunjikana mpaka kumwamba,+ ndipo Mulungu wakumbukira+ zochita zake zopanda chilungamo.
6 M’bwezereni monga mmene iye anachitira.+ M’chitireni mowirikiza kawiri. Ndithu, wirikizani kawiri zinthu zimene iyeyo anachita.+ M’kapu+ imene anaikamo chakumwa chosakaniza, ikanimo chakumwa chakecho+ kuwirikiza kawiri.+
7 Pa muyezo umene anadzipezera ulemerero ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, pa muyezo womwewo mumuzunze ndi kumuliritsa.+ Pakuti mumtima mwake akumanena kuti, ‘Ine ndine mfumukazi.+ Sindine mkazi wamasiye,+ ndipo sindidzalira+ ngakhale pang’ono.’
8 Ndiye chifukwa chake m’tsiku limodzi, miliri yake idzafika. Miliri yakeyo+ ndiyo imfa, kulira, ndi njala. Ndipo adzanyekeratu ndi moto+ chifukwa Yehova Mulungu, amene anamuweruza, ndi wamphamvu.+
9 “Mafumu+ a dziko lapansi amene anachita naye dama ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, adzalira ndi kudziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye,+ poona utsi+ wofuka chifukwa cha kupsa kwake.
10 Ndipo ataima patali poona kuzunzika kwake, adzati,+ ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe!+ Babulo iwe, mzinda wamphamvu! Chifukwa mu ola limodzi, chiweruzo chako chafika!’+
11 “Komanso, amalonda oyendayenda+ a padziko lapansi adzamulira+ maliro ndi kumva chisoni, chifukwa palibenso wina wowagula katundu wawo yense,
12 katundu yense+ wagolide, siliva, mwala wamtengo wapatali, ndi ngale. Komanso palibe wowagula nsalu zabwino kwambiri, zofiirira, zasilika, zofiira kwambiri, ndi mtengo uliwonse wa fungo lokoma, komanso chilichonse chopangidwa ndi mnyanga, chilichonse chopangidwa ndi mtengo wapamwamba, ndi chamkuwa, chachitsulo, ndi chamwala wa mabo.+
13 Komanso palibe wowagula sinamoni, amomo,* zofukiza, mafuta onunkhira, lubani, vinyo, mafuta a maolivi, ufa wabwino kwambiri, tirigu, ng’ombe, nkhosa, mahatchi, ngolo, akapolo, ndi anthu.+
14 Zoonadi, chipatso chabwino chimene moyo wako unali kulakalaka+ chakuchokera. Zinthu zako zonse zabwino ndi zokongola zawonongeka, ndipo anthu sadzazipezanso.+
15 “Amalonda oyendayenda+ a zinthu zimenezi, amene analemerera pa iye, adzaima patali chifukwa cha mantha poona kuzunzika kwake. Iwo adzamulira maliro ndi kumva chisoni+
16 ndipo azidzati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe+ wovala zovala zapamwamba, zofiirira, ndi zofiira kwambiri. Mzinda wokongoletsedwa mochititsa kaso iwe, ndi zokongoletsera zagolide, zamwala wamtengo wapatali, ndi zangale.+
17 Zachisoni, chifukwa mu ola limodzi, chuma chochulukachi chawonongedwa!’+
“Woyendetsa ngalawa aliyense ndi munthu aliyense woyenda panyanja kuchokera kulikonse,+ ogwira ntchito m’ngalawa ndi onse oyenda panyanja pochita malonda awo, anaima patali.+
18 Poona utsi wofuka chifukwa cha kupsa kwake, iwo anafuula kuti, ‘Ndi mzinda uti ungafanane ndi mzinda waukulu+ umenewu?’
19 Iwo anathira fumbi pamitu pawo+ akufuula, kulira ndi kumva chisoni,+ ndipo anati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwu, umene unalemeretsa+ onse okhala ndi ngalawa panyanja+ chifukwa cha chuma chake chamtengo wapatali, pakuti mu ola limodzi, wawonongedwa.’+
20 “Kondwerani kumwambako+ chifukwa cha zimene zamuchitikira. Inunso oyera,+ inu atumwi,+ ndi inu aneneri, kondwerani chifukwa Mulungu wamuweruza ndi kumupatsa chilango chifukwa cha zomwe anakuchitirani.”+
21 Ndiyeno mngelo wamphamvu ananyamula mwala wooneka ngati mphero yaikulu+ n’kuuponya m’nyanja,+ ndipo anati: “Mzinda waukulu wa Babulo udzaponyedwa pansi mofulumira ndi mwamphamvu chonchi, ndipo sudzapezekanso.+
22 Pamenepo kuimba kwa oimba motsagana ndi zeze, kwa oimba zitoliro, kwa oimba malipenga, ndi kwa oimba ena, sikudzamvekanso+ mwa iwe. Mwa iwe simudzapezekanso mmisiri wa ntchito iliyonse, ngakhale phokoso la mphero silidzamvekanso mwa iwe.
23 Kuwala kwa nyale sikudzaunikanso mwa iwe. Mawu a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso+ mwa iwe, chifukwa amalonda ako oyendayenda+ anali anthu apamwamba+ padziko lapansi, ndiponso mitundu yonse ya anthu inasocheretsedwa ndi zochita zako zamizimu.+
24 Mwa iye munapezeka magazi+ a aneneri,+ a oyera,+ ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “zonunkhiritsa zochokera ku India.”